Kufunika kwa Phunziro Laumwini Ndiponso Labanja
1. Kodi Bungwe Lolamulira likufuna kuti aliyense azitani ndipo n’chifukwa chiyani?
1 Mofanana ndi nthawi ya Atumwi, Bungwe Lolamulira masiku ano likuyesetsa kuti lisamalire atumiki a Yehova. (Mac. 15:6, 28) Pamene chisautso chachikulu chikuyandikira ndi bwino kuti wofalitsa Ufumu aliyense akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Kodi nthawi imene munkapita ku Phunziro la Buku la Mpingo mudzaigwiritsa ntchito motani? Tikukulimbikitsani nonse kugwiritsa ntchito bwino nthawi imeneyi pa kuphunzira Baibulo ndi banja lanu. Tikamatero, tidzayamba kupindula kwambiri chifukwa chowerenga mozama mawu ouziridwa a Mulungu omwe ndi madzi a moyo.—Sal. 1:1-3; Aroma 11:33, 34.
2. Kodi nthawi yathu ya kulambira kwa pabanja tingaigwiritse ntchito motani?
2 Nthawi ya Kulambira kwa Pabanja: Mitu ya mabanja iyenera kukwaniritsa udindo umene Yehova anawapatsa poonetsetsa kuti akuphunzira Baibulo ndi banja lawo nthawi zonse. (Deut 6:6, 7) Abale ndi alongo osakwatira amene sakusamalira aliyense ayenera kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi pophunzira Baibulo paokha komanso kufufuza. Ndi bwino kuti tonsefe ‘tidziwombolere nthawi yoyenerera’ kuti tiziphunzira komanso kusinkhasinkha. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhalabe olimba mwauzimu ‘m’masiku oipawa.’—Aef. 5:15, 16.
3, 4. Kodi panthawiyi tingagwiritsire ntchito chiyani, ndipo tiyenera kuganizira kwambiri za chiyani?
3 Zinthu Zimene Mungaphunzire: Mungapeze mfundo zosangalatsa zimene mungakambirane pa phunziro lanu la Baibulo mu Mlozera Nkhani wa Magazini a Nsanja ya Olonda, Mlozera Nkhani wa Magazini a Galamukani!, Watch Tower Publications Index kapena mu laibulale ya pa kompyuta yotchedwa Watchtower Library. Mabanja angagwiritsenso ntchito nkhani za mu Nsanja ya Olonda zimene zimatuluka kawirikawiri monga zakuti, “Chinsinsi cha Banja Losangalala,” “Phunzitsani Ana Anu” ndiponso “Zoti Achinyamata Achite.” Komanso m’magazini ya Galamukani! mumakhala nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” ndi nkhani zinanso zosangalatsa zofotokoza zinthu zochititsa chidwi m’chilengedwe.
4 Kuwerenga Baibulo mosathamanga kungakhomereze mfundo za m’Baibulo m’maganizo ndi m’mitima ya anthu onse m’banjamo. (Aheb. 4:12) Nthawi zina mungathe kuonera ndi kukambirana vidiyo iliyonse yopangidwa ndi gulu la Yehova. Pali mwayi wosankha nokha zimene mungaphunzire komanso woganizira mmene mungaziphunzirire. Ndi bwino kufunsa ena m’banja lanu kuti anene zimene akufuna kuti muphunzire komanso njira zophunzirira zimene zingawasangalatse.
5. N’chifukwa chiyani kuphunzira Baibulo patokha ndiponso kuphunzira ndi banja kuli kofunika kwambiri masiku ano?
5 Kufunika Kwake Panopo: Kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova panopa kutithandiza ‘kuchirimika ndi kupenya chipulumutso cha Yehova.’ (Eks. 14:13) Makolo ayenera kutsatira malangizo a Mulungu kuti alere bwino ana awo “pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota.” (Afil. 2:15) Ana nawonso afunika kuthandizidwa kuti asatengere makhalidwe oipa amene afala m’masukulu masiku ano. (Miy. 22:3, 6) Anthu apabanja ayenera kulimbitsa ubale wawo ndi Yehova kuti banja lawo likhale “chingwe cha nkhosi zitatu.” (Mlaliki 4:12) Motero, tiyeni tigwiritse ntchito nthawi yathu yotsalayi kuti tilimbitse ‘chikhulupiriro chathu choyera kopambana.’—Yuda 20.