‘Musachite Mantha’
1. Kodi tingakumane ndi mavuto otani mofanana ndi Yeremiya?
1 Pamene Yeremiya anasankhidwa kuti akhale mneneri, ankadziona kuti sangakwanitse ntchitoyo. Koma Yehova anamulimbikitsa kuti, “usachite mantha,” ndipo mwachikondi anamupatsa mphamvu kuti athe kukwanitsa ntchito imene anam’patsa. (Yer. 1:6-10) Masiku ano, manyazi kapena kudzikayikira kungatilepheretse kuchita nawo utumiki bwinobwino. Nthawi zina kuopa zimene anthu angayankhe kapena mmene angationere, kungatilepheretse kulalikira. Kodi mantha angati amenewa tingawathetse motani? Nanga tingapeze madalitso otani?
2. Kodi kukonzekera kungatithandize bwanji kuchepetsa mantha pochita utumiki?
2 Konzekerani Pasadakhale: Kukonzekera mokwanira n’kofunika kwambiri kuti tichepetse mantha. Mwachitsanzo, ngati titaoneratu zimene anthu ambiri amanena zomwe zingalepheretse kukambirana nawo, tingathe kuyankha anthu ena amene safuna kuti tiwalalikire. (Miy. 15:28) Mungachite bwino kugwiritsa ntchito nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kuyesezeratu mmene mungagonjetsere mavuto amene mungakumane nawo kusukulu ndiponso mu utumiki.—1 Pet. 3:15.
3. Kodi kukhulupirira Yehova kumatithandiza bwanji kuthetsa mantha?
3 Muzikhulupirira Yehova: Kudalira Mulungu ndi njira yabwino yothetsera mantha. Yehova akutitsimikizira kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10-13) Palibe thandizo lina limene lingapose pamenepa. Kuwonjezera pamenepa, Yesu anatitsimikizira kuti ngakhale titakumana ndi zinthu zosayembekezereka, mzimu woyera wa Mulungu udzatithandiza kuchitira umboni moyenerera. (Maliko 13:11) Choncho, nthawi zonse muzipemphera kwa Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera.—Luka 11:13.
4. Kodi timakhala ndi madalitso otani tikamapirira mu utumiki ngakhale tikukumana ndi mavuto?
4 Madalitso: Tikamapirira mu utumiki pamene tikukumana ndi zovuta, zimatithandiza kukhala olimba kuti tidzathe kupirira mayesero m’tsogolo. Timakhala olimba mtima, ndipo khalidwe limeneli ndi limene limasonyeza kuti munthu ali ndi mzimu woyera. (Mac. 4:31) Komanso tikamathetsa mantha modalira thandizo la Yehova, timalimbitsa chidaliro chathu chakuti iye ndiye mpulumutsi wathu. (Yes. 33:2) Komanso timakhala osangalala ndiponso okhutira chifukwa chodziwa kuti tikusangalatsa Atate wathu wakumwamba. (1 Pet. 4:13, 14) Choncho, tisamachite mantha polengeza uthenga wa Ufumu molimba mtima, ndipo nthawi zonse tizikhulupirira kuti Yehova adzatithandiza.