Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Mika
1. Kodi n’kutheka kuti Mika ankadzifunsa funso liti, nanga n’chifukwa chiyani tingati ntchito yake sinapite pachabe?
1 ‘Kodi mapeto a dziko loipali adzafika liti?’ Mneneri Mika ayenera ankadzifunsanso funso langati limeneli pamene ankalengeza uthenga wachiweruzo cha Yehova pa ufumu wa Isiraeli ndi Yuda. Komabe ntchito yakeyi sinapite pachabe. Mu 740 B.C.E., mneneriyu adakali moyo, zimene Yehova ananeneratu zokhudza Samariya, zinakwaniritsidwa. (Mika 1:6, 7) Kenako, Yerusalemunso anawonongedwa mu 607 B.C.E. (Mika 3:12) Kodi tingatsanzire bwanji Mika pamene nafenso tikuyembekezera kuti Yehova aweruze dziko loipali?
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuleza mtima pamene tikudikira tsiku la Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi?
2 Khalani Oleza Mtima: Mika analemba kuti: “Koma ine ndidzadikirira Yehova. Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.” (Mika 7:7) Komatu sikuti Mika anangokhala osachita chilichonse, n’kumadikirira kuti tsiku la Yehova lifike. Iye ankatanganidwa kwambiri ndi ntchito yake monga mneneri. Pamene tikudikira tsiku la Yehova, nafenso tiyenera ‘kukhala anthu akhalidwe loyera n’kumachita ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu.’ (2 Pet. 3:11, 12) Yehova akuleza mtima popereka mwayi kwa anthu kuti alape. (2 Pet. 3:9) Choncho, timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizitengera chitsanzo kwa aneneri pa nkhani ya kuleza mtima.—Yak. 5:10.
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera?
3 Muzidalira Yehova: Mika anali ndi ntchito yovuta kwambiri, koma ankadalira Yehova kuti amuthandize kugwira ntchito yakeyi. (Mika 3:8) Nafenso Yehova amadziwa kuti sitingakwanitse kugwira ntchito imene watipatsa patokha. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipempha Yehova kuti atithandize. Iye amapereka mphamvu moolowa manja kwa amene akufunikira, n’cholinga choti akwaniritse udindo wawo monga Akhristu. (Sal. 84:5, 7; Yes. 40:28-31) Kodi pali nthawi inayake pa moyo wanu, pamene munaona kuti Yehova wakupatsani mphamvu kuti mukwanitse kuchita zinazake? Kodi nthawi zonse mumapempha Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera?—Luka 11:13.
4. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Mika?
4 Pa moyo wake wonse, Mika ankaona kuti chinthu chofunika kwambiri ndi kutumikira Yehova. Iye anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti ankakhala pakati pa anthu a makhalidwe oipa. Nafenso tsiku ndi tsiku timakumana ndi zinthu zimene zimayesa kukhulupirika kwathu. Choncho, tiyeni nafenso titsimikize mtima kuti “tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”—Mika 4:5.