Kodi Tingatani Kuti Tiziona Kuti Ntchito Yolalikira Ndi Yofunika Kwambiri?
Mkhristu aliyense ayenera kuona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Kugwira ntchitoyi ndi maganizo amenewa kungathandize kuti tidzapulumuke. Kuchita zinthu zili m’munsizi kungatithandize kuti tiziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri.
Tizipemphera nthawi zonse kuti Ufumu wa Mulungu ubwere.—Mat. 6:10.
Tiziwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku n’cholinga choti titeteze mtima wathu.—Aheb. 3:12.
Tizigwiritsa ntchito nthawi mwanzeru.—Aef. 5:15, 16; Afil. 1:10.
Tizikhala ndi diso “lolunjika pa chinthu chimodzi” ndipo tisalole kuti zinthu za m’dzikoli zitisokoneze.—Mat. 6:22, 25; 2 Tim. 4:10.
Tizikhala maso ndipo tizizindikira maulosi a m’Baibulo amene akukwaniritsidwa panopa.—Maliko 13:35-37.
Kuona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri, kungatithandize kuti tizigwira ntchitoyi modzipereka.—Yoh. 4:34, 35.