CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZARA 6-10
Yehova Amafuna Kuti Tizimutumikira ndi Mtima Wonse
Ezara anakonzekera kubwerera ku Yerusalemu
Ezara analoledwa ndi Mfumu Aritasasita kuti apite ku Yerusalemu kukathandiza anthu kuti azilambira Yehova
Mfumu inapatsa Ezara “zopempha zake zonse” kuti akamangire nyumba ya Yehova. Inamupatsa golide, siliva, tirigu, vinyo, mafuta ndi mchere. Malinga ndi ndalama za masiku ano, zonse zingakwane madola 100 miliyoni a ku America
Ezara ankakhulupirira kuti Yehova ateteza atumiki ake
Ulendo wobwerera ku Yerusalemu unali wovuta
Unali mtunda wa makilomita pafupifupi 1,600 ndipo ankadutsa m’malo oopsa
Ulendowu unatenga miyezi pafupifupi 4
Anthu obwererawo anafunika kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu, kulimba mtima komanso kukonda kwambiri kulambira Yehova
EZARA ANATENGA . . .
Golide ndi siliva zolemera matalente oposa 750
MAVUTO AMENE ANTHU ANAKUMANA NAWO POBWERERA . . .
Magulu a zigawenga, kutentha kwa m’chipululu, zilombo zolusa