Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 April tsamba 3
  • Tizilimbikitsa Anzathu Powayankhula Mokoma Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizilimbikitsa Anzathu Powayankhula Mokoma Mtima
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Yobu Anapirira—Nafenso Tingatero!
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Yobu Afupidwa Chifukwa Chokhulupirika
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yobu Analemekeza Dzina la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 April tsamba 3

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 16-20

Tizilimbikitsa Anzathu Powayankhula Mokoma Mtima

Munthu wopereka malangizo ayenera kuyankhula molimbikitsa kwa ena

16:4, 5

  • Yobu anavutika maganizo kwambiri, choncho ankafunika kulimbikitsidwa

  • Anzake atatu a Yobu sananene chilichonse chomulimbikitsa. Iwo ankangomuimba mlandu ndipo zinamusokoneza maganizo kwambiri

Yobu analira chifukwa cha mawu opweteka a Bilidadi

19:2, 25

  • Yobu anadandaulira Mulungu kuti amuthandize kupezako mpumulo, ngakhale kufa kumene

  • Yobu ankakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka ndipo anakhala wokhulupirika nthawi yonse yomwe anakumana ndi mavuto

Elifazi akuyankhula ndi Yobu, Bilidadi ndi Zofari akungoyang’ana

ANTHU AMENE ANKAIMBA MLANDU YOBU

Elifazi

Elifazi:

  • N’kutheka kuti anali wochokera ku Temani, m’dziko la Edomu. Lemba la Yeremiya 49:7 limasonyeza kuti Temani anali malo a nzeru za Aedomu

  • Zikuoneka kuti Elifazi yemwe anali wamkulu komanso wodalirika pa anzake atatu a Yobu omwe ankati abwera kudzamulimbikitsa, ndi amene anali woyamba kuyankhula. Iye anayankhula maulendo atatu komanso kwa nthawi yaitali kuposa anzake aja

Mabodza amene ananena:

  • Ananyoza Yobu chifukwa cha kukhulupirika kwake n’kunena kuti Mulungu sakhulupirira atumiki ake (Yobu 4, 5)

  • Ananena kuti Yobu anali munthu wodzikuza, woipa komanso wosaopa Mulungu (Yobu 15)

  • Ananena kuti Yobu anali munthu waumbombo ndi wopanda chilungamo ndipo ananenanso kuti anthu ndi opanda ntchito kwa Mulungu (Yobu 22)

Bilidadi

Bilidadi:

  • Anali mbadwa ya ku Shuwa. Ayenera kuti ankakhala kufupi ndi mtsinje wa Firate

  • Iye anali wachiwiri kuyankhula ndipo nayenso anayankhula maulendo atatu. Mawu ake anali opweteka kwambiri kuposa a Elifazi

Mabodza amene ananena:

  • Ananena zinthu zosonyeza kuti ana a Yobu anachimwa ndipo anayenera kufa ndiponso kuti Yobu sankakhulupirira Mulungu (Yobu 8)

  • Ananena zinthu zosonyeza kuti Yobu anali wochimwa (Yobu 18)

  • Ananena kuti anthu amangodzivuta akamayesetsa kukhala okhulupirika (Yobu 25)

Zofari

Zofari:

  • Zofari anali wa ku Naama, dera lomwe mwina linali kumpoto chakumadzulo kwa dziko la Arabia

  • Iye anali wachitatu kuyankhula ndipo ndiye anayankhula mawu opweteka kwambiri kuposa anzake onse. Iye anangoyankhula kawiri kokha

Mabodza amene ananena:

  • Ananena kuti Yobu ankayankhula zopanda nzeru ndipo anamuuza kuti asiye kuchita zoipa (Yobu 11)

  • Ananena zinthu zosonyeza kuti Yobu anali munthu woipa ndipo ankasangalala ndi kuchita machimo (Yobu 20)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena