CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 45-51
Yehova Sadzasiya Anthu Amtima Wosweka
Davide analemba Salimo 51 pambuyo poti mneneri Natani waulula tchimo lachigololo lomwe Davideyo anachita ndi Bateseba. Zimenezi zinkamusautsa mumtima ndipo anadzichepetsa n’kuvomereza tchimo lakelo.—2 Sam. 12:1-14.
Ngakhale kuti Davide anachimwa, Mulungu anali wokonzeka kumukhululukira
Asanavomereze ndiponso kulapa tchimo lakelo, ankasowa mtendere
Davide anavutika mumtima atadziwa kuti wakhumudwitsa Mulungu, mofanana ndi mmene munthu amamvera mafupa ake akaphwanyidwa
Iye ankafunitsitsa kukonzanso ubwenzi wake ndi Mulungu komanso kukhululukidwa n’cholinga choti azisangalala ngati poyamba
Iye anapempha Yehova modzichepetsa kuti amuthandize kukhala ndi mtima womvera
Ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova amukhululukira