CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 60-68
Tamandani Yehova Wakumva Pemphero
Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukwaniritsa zomwe munamulonjeza
Tikamauza Yehova m’pemphero zimene tamulonjeza, zimatithandiza kuti tikwaniritsedi zimene tamulonjezazo
Chinthu chofunika kwambiri chimene tingalonjeze Mulungu n’choti tidzamutumikira kwa moyo wathu wonse
Hana
Muzisonyeza kuti mumakhulupirira Yehova pomuuza zakukhosi kwanu
Mapemphero athu angakhale abwino kwambiri ngati titamafotokozera Yehova zimene zili mumtima mwathu
Tikamatchula m’pemphero chinthu chenicheni chimene tikufuna, sitivutika kuzindikira kuti Yehova wayankha mapemphero athu
Yesu
Yehova amamva mapemphero a anthu a mitima yabwino
Yehova amamvetsera mapemphero a “anthu a mitundu yonse” omwe amafunitsitsa kumudziwa komanso kuchita zofuna zake
Tikhoza kupemphera kwa Yehova nthawi iliyonse
Koneliyo
Lembani nkhani zina zimene mukufuna kutchula m’mapemphero anu.