CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 7-11
“Mtima Wako Usapatuke”
Mfundo za Yehova zikhoza kutiteteza. Koma kuti zizitithandiza tiyenera kuzikonda ndi mtima wathu wonse. (Miy. 7:3) Mtumiki wa Yehova akalola kuti mtima wake upatuke, zimakhala zosavuta kuti Satana amupusitse. Chaputala 7 cha Miyambo chimafotokoza za mnyamata wina yemwe analola kuti mtima wake umupusitse. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira mnyamatayu?
Satana amagwiritsa ntchito zinthu zimene tatchulazi pofuna kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova
Tikakhala anzeru ndiponso omvetsa zinthu tidzatha kuoneratu ndiponso kupewa mavuto amene angabwere ngati titachita zinthu zoipa