CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 12-16
Nzeru Ndi Yabwino Kuposa Golide
Kodi nzeru yochokera kwa Mulungu ndi yamtengo wapatali chifukwa chiyani? Imathandiza anthu kuti asamachite zinthu zoipa komanso imateteza moyo wawo. Imawathandizanso kuti akhale ndi khalidwe labwino ndiponso kuti azilankhula zabwino.
Nzeru imathandiza munthu kuti asakhale wodzikuza
Munthu wanzeru amazindikira kuti Yehova ndi amene amapereka nzeru
Anthu amene zinthu zikuwayendera bwino komanso omwe apatsidwa udindo winawake ayenera kusamala kwambiri kuti asakhale onyada kapena odzikuza
Nzeru imathandiza munthu kuti azilankhula zolimbikitsa
Munthu wanzeru amayesetsa kuzindikira zinthu zabwino zimene ena amachita ndipo amalankhula zabwino zokhudza anthuwo
Mawu anzeru amakhala olimbikitsa ndiponso okoma ngati uchi, osati aukali kapena oyambitsa mikangano