Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp20 No. 3 tsamba 10
  • Muzipemphera Kuti Mulungu Akudalitseni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzipemphera Kuti Mulungu Akudalitseni
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MUZIPEMPHERA MODZICHEPETSA KOMANSO MOCHOKERA PANSI PA MTIMA
  • MUZITCHULA DZINA LA MULUNGU POPEMPHERA
  • MUZIPEMPHERA M’CHINENERO CHANU
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
wp20 No. 3 tsamba 10
Munthu wa ku Middle East akupemphera.

Mulungu, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” amasangalala kumvetsera mapemphero athu.—SALIMO 65:2

Muzipemphera Kuti Mulungu Akudalitseni

Pemphero ndi mphatso yapadera imene Mulungu anapatsa anthu kuti azitha kulankhula naye ndi kufotokoza mmene akumvera. Mneneri Davide anapempha kuti: “Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.” (Salimo 65:2) Koma kodi tizipemphera bwanji kuti Mulungu azimva mapemphero athu komanso kutidalitsa?

MUZIPEMPHERA MODZICHEPETSA KOMANSO MOCHOKERA PANSI PA MTIMA

Mukamapemphera kwa Mulungu ‘mumamukhuthulira za mumtima mwanu’ ndi kumuuza mmene mukumvera. (Salimo 62:8) Mulungu Wamphamvuyonse amakonda mapemphero ochokera pansi pa mtima.

MUZITCHULA DZINA LA MULUNGU POPEMPHERA

Ngakhale kuti Mulungu ali ndi mayina audindo ambiri, dzina lake lenileni ndi limodzi lokha. Paja iye anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) M’Malemba Opatulika, dzina lakuti Yehova limapezeka nthawi zosachepera 7,000. Aneneri ambiri ankatchula dzina lenileni la Mulungu popemphera. Abulahamu anati: “Chonde Yehova, . . . ndiloleni ndilankhulebe [ndi inu].” (Genesis 18:30) Nafenso tizitchula dzina la Mulungu lakuti Yehova tikamapemphera.

MUZIPEMPHERA M’CHINENERO CHANU

Mulungu amamvetsa maganizo athu komanso mmene tikumvera posatengera chinenero chathu. Mawu ake amatitsimikizira kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Komabe, kuti Mulungu atidalitse tiyenera kuchita zambiri kuwonjezera pa kupemphera. M’nkhani zotsatirazi tiona zimene tiyenera kuchita.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena