Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 June tsamba 2
  • Kodi Mumakhulupirira Kwambiri Zimene Yehova Analonjeza?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakhulupirira Kwambiri Zimene Yehova Analonjeza?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Amakwaniritsa Malonjezo
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Zimene Yoswa Anakumbukira
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoswa
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Iye Amafuna Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 June tsamba 2

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumakhulupirira Kwambiri Zimene Yehova Analonjeza?

Yoswa komanso Solomo anatsimikiza kuti mawu onse amene Yehova ananena anakwaniritsidwa. (Yos. 23:14; 1 Maf. 8:56) Zimene anthu awiriwa ananena zingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu.​—2 Akor. 13:1; Tito 1:2.

Kodi Yehova anakwaniritsa bwanji malonjezo ake m’nthawi ya Yoswa? Limodzi ndi banja lanu, onerani vidiyo yakuti ‘Palibe Ngakhale Mawu Amodzi Omwe Sanakwaniritsidwe.’ Kenako yankhani mafunso otsatirawa: (1) Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Rahabi? (Aheb. 11:31; Yak. 2:24-26) (2) Kodi chitsanzo cha Akani chikusonyeza bwanji kuti kusamvera kumabweretsa mavuto? (3) Kodi n’chifukwa chiyani amuna a ku Gibeoni, ngakhale kuti anali odziwa kumenya nkhondo, ananamiza Yoswa n’kuchita pangano la mtendere ndi Aisiraeli? (4) Kodi mawu a Yehova anakwaniritsidwa bwanji pamene mafumu 5 a Aamori ankaopseza Aisiraeli? (Yos. 10:5-14) (5) Kodi Yehova anakuthandizani bwanji inuyo chifukwa choika Ufumu ndi chilungamo chake pamalo oyamba?​—Mat. 6:33.

Tikamaganizira zonse zimene Yehova anachita, zimene akuchita panopa komanso zimene adzachite m’tsogolo, chikhulupiriro chathu pa malonjezo ake chimalimba kwambiri.​—Aroma 8:31, 32.

Yoswa

Kodi muli ndi chikhulupiriro ngati cha Yoswa?

MAFUNSO OYENERA KUWAGANIZIRA:

  • Kodi ndi maulosi ati a m’Baibulo omwe mukuona kuti akukwaniritsidwa masiku ano?

  • Kodi ndi maulosi ati a m’Baibulo amene mumafunitsitsa mutaona akukwaniritsidwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena