MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo—Chikhulupiriro
N’CHIFUKWA CHIYANI KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO N’KOFUNIKA?
Chikhulupiriro n’chofunika kuti tizichita zimene Mulungu amasangalala nazo.—Aheb. 11:6
Kukhulupirira zimene Mulungu anatilonjeza kumatithandiza kupirira tikakumana ndi mayesero.—1 Pet. 1:6, 7
Kupanda chikhulupiriro kungachititse munthu kuti achite tchimo.—Aheb. 3:12, 13
KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TILI NDI CHIKHULUPIRIRO?
Tizipemphera kuti tikhale ndi chikhulupiriro.—Luka 11:9, 13; Agal. 5:22
Tiziwerenga Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha.—Aroma 10:17; 1 Tim. 4:15
Nthawi zonse tizicheza ndi anthu amene ali ndi chikhulupiriro.—Aroma 1:11, 12
Kodi ndingalimbitse bwanji chikhulupiriro changa komanso cha anthu a m’banja langa?
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA ZINTHU ZIMENE ZINGAKULIMBIKITSENI KUKHALA OKHULUPIRIKA—CHIKHULUPIRIRO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi “chikhulupiriro chopanda chinyengo” chimakhala chotani? (1 Tim. 1:5)
Kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, kodi tiyenera kupewa maganizo olakwika ati?
N’chifukwa chiyani tidzafunika kukhala ndi chikhulupiriro pa nthawi ya chisautso chachikulu? (Aheb. 10:39)