Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 April tsamba 8
  • Kulalikira Komanso Kuphunzitsa N’kofunika Kwambiri Kuti Tipange Ophunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira Komanso Kuphunzitsa N’kofunika Kwambiri Kuti Tipange Ophunzira
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzithandiza Anthu Amene Ali ndi “Maganizo Abwino” Kuti Akhale Ophunzira
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Kodi Mungagwire Nawo Ntchito Yothandiza Anthu Kukhala Ophunzira a Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kulengeza Uthenga Wabwino Mosaleka
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 April tsamba 8

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kulalikira Komanso Kuphunzitsa N’kofunika Kwambiri Kuti Tipange Ophunzira

Yesu analamula otsatira ake kuti athandize anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake. (Mat. 28:19) Kuti zimenezi zitheke pamafunika kulalikira komanso kuphunzitsa. Nthawi zonse tiyenera kumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndizilalikira komanso kuphunzitsa anthu mwaluso muutumiki?’

KULALIKIRA

M’malo modikira kuti anthu abwere kwa ife, tiyenera kupita n’kumakafufuza anthu amene ‘ali oyenerera.’ (Mat. 10:11) Tikakhala mu utumiki, kodi timakhala tcheru kuti tilankhule ndi aliyense amene takumana naye? (Mac. 17:17) Lidiya anakhala wophunzira chifukwa chakuti Paulo ankalalikira mwakhama.​—Mac. 16:13-15.

Samuel akum’patsa Ezekiel magazini; a Solomon ndi a Mary akulalikira kwa Ezekiel ndi Abigail

“Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo” (Mlal. 11:6)

ONERANI VIDIYO YAKUTI, PITIRIZANI KULALIKIRA “MWAKHAMA”​—MWAMWAYI KOMANSO KUNYUMBA NDI NYUMBA KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRIWA:

  • Kodi Samuel anasonyeza bwanji kuti tsiku lililonse ankafunitsitsa kubzala mbewu za choonadi?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizigwiritsa ntchito njira zonse zolalikirira?

  • Kodi tingamalalikire kwa ndani pamene tikuchita zinthu zatsiku ndi tsiku?

KUPHUNZITSA

Kuti tipange ophunzira, si zokwanira kumangosiyira magazini anthu omwe timawapeza. Tiyenera kumapanga maulendo obwereza ndiponso kumachititsa maphunziro a Baibulo n’cholinga chofuna kuthandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. (1 Akor. 3:6-9) Koma bwanji ngati anthu amene tikuchita khama kuti tiwaphunzitse za Ufumu wa Mulungu alibe chidwi? (Mat. 13:19-22) Tiyenera kufufuzabe anthu amene mitima yawo ili ngati ‘nthaka yabwino.’​—Mat. 13:23; Mac. 13:48.

A Solomon ndi a Mary akuphunzira Baibulo ndi Ezekiel ndi Abigail; Ezekiel ndi Abigail akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri

“Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira, koma Mulungu ndiye anakulitsa” (1 Akor. 3:6)

ONERANI VIDIYO YAKUTI, PITIRIZANI KULALIKIRA “MWAKHAMA”​—M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI KOMANSO MUZITHANDIZA ANTHU KUTI AKHALE OPHUNZIRA A YESU KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi a Solomon ndi akazi awo anatani kuti athirire mbewu za choonadi mumtima mwa a Ezekiel ndi akazi awo?

  • Kodi cholinga chathu chizikhala chotani tikamagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira kuphatikizapo kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri?

  • Kodi tingatani kuti tizilimbikira kugwira ntchito yophunzitsa ena choonadi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena