Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 February tsamba 8
  • Pitirizani Kudikira Mopirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kudikira Mopirira
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni Kulandira Mphoto
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • “Mulole Kuti Kupirira Kumalize Kugwira Ntchito Yake”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Chipiriro—Nchofunika kwa Akristu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kuthamanga Makaniwo Mwachipiriro
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 February tsamba 8

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Pitirizani Kudikira Mopirira

Kodi mwakhala mukudikira kwa nthawi yaitali bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ubwere? Kodi mukupitirizabe kudikira mopirira ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto? (Aroma 8:25) Akhristu ena amatsutsidwa, kuzunzidwa, kutsekeredwa m’ndende ngakhale kufuna kuphedwa kumene. Enanso akupirira mayesero monga matenda aakulu komanso ukalamba.

Kodi n’chiyani chingatithandize kupitiriza kudikira mopirira ngakhale tikukumana ndi mavuto amenewa? Tingalimbitse chikhulupiriro chathu tikamawerenga Baibulo komanso kusinkhasinkha zimene tawerengazo. Tiziganizira kwambiri zimene tikuyembekezera m’tsogolomu. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 12:2) Komanso tizipempha mochonderera kwa Yehova kuti atipatse mphamvu yake ya mzimu woyera. (Luka 11:10, 13; Aheb. 5:7) Yehova yemwe ndi Atate wathu wachikondi angatithandize “kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.”​—Akol. 1:11.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, TIYENERA ‘KUTHAMANGA MOPIRIRA’​—MUSAMAKAYIKIRE KUTI MUDZAPEZA MPHOTO NDIPO KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Jamie ali mu utumiki ndi mkazi wake

    Kodi ndi “zinthu zosayembekezereka” ziti zimene zingachitike pa moyo wathu? (Mlal. 9:11)

  • Jamie ali ndi matenda ofa ziwalo ndipo a Carl akukambirana naye lemba la m’Baibulo

    Kodi pemphero lingatithandize bwanji tikamakumana ndi mayesero?

  • Jamie ndi a Carl akulimbikitsa banja lina

    Ngati panopa sitingathenso kutumikira Yehova ngati kale, n’chifukwa chiyani tiyenera kumangochita zimene tingakwanitse?

  • Jamie akuganizira ali m’paradaiso atakhalanso wathanzi

    Muziyang’anabe pamphoto

    N’chiyani chimene chimakuthandizani kuti musamakayikire kuti mudzalandira mphoto?

Kodi mungathandize bwanji anthu amene akukumana ndi mayesero komanso anthu a m’banja lawo?

  • Muziwauza mawu olimbikitsa komanso musamawayerekezere ndi anthu ena

  • Muzimvetsera akamanena nkhawa zawo

  • Muziwapempherera kapena kupemphera nawo limodzi

  • Muziwaphikira kapena kuwathandiza ntchito zapakhomo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena