Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 March tsamba 7
  • Muzigwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzira ndi Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzigwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzira ndi Anthu
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kugwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Kodi Ndizionera Matepi a Nyimbo?
    Galamukani!—2003
  • Muzigwiritsira Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kubwereza Gawo 2
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 March tsamba 7
Mlongo akuonetsa wophunzira wake vidiyo

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzigwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzira ndi Anthu

Anthu amachita chidwi ndi zomwe aona ndipo zimawathandiza kumvetsa komanso kukumbukira zomwe aphunzira. Yehova, monga Mlangizi Wamkulu, wakhala akuphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito zinthu zooneka. (Gen. 15:5; Yer. 18:1-6) Yesu nayenso yemwe anali Mphunzitsi Waluso, ankaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito njira imeneyi. (Mat. 18:2-6; 22:19-21) Masiku ano timagwiritsa ntchito mavidiyo monga njira imodzi yophunzitsira anthu ndipo njirayi ndi yothandiza kwambiri. Kodi nanunso mumagwiritsa ntchito mavidiyo mukamaphunzira Baibulo ndi anthu?

Panakonzedwa mavidiyo 10 omwe cholinga chake n’kutithandiza tikamaphunzira ndi anthu pogwiritsa ntchito kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Mitu ya mavidiyowa ndi yogwirizana ndi funso linalake lomwe likupezeka m’kabukuka. Pazipangizo zamakono, kabukuka kakonzedwanso kuti kazikhala ndi malinki otithandiza kudziwa malo omwe tikufunika kuonetsa vidiyo. Tilinso ndi mavidiyo ena omwe ali ndi mfundo zofanana ndi zomwe zikupezeka m’zinthu zomwe timagwiritsa ntchito pophunzitsa.

Kodi mukuphunzira mfundo ya m’Baibulo imene wophunzira wanu angavutike kuimvetsa? Kodi wophunzira wanuyo akukumana ndi mayesero enaake? Ngati ndi choncho, mungafufuze pa jw.org® kapena pa JW Broadcasting® kuti mupeze vidiyo yomwe ingamuthandize. Mwina mungaonere limodzi vidiyoyo kenako n’kukambirana.

Mavidiyo atsopano amatuluka mwezi ulionse. Mukamaonera mavidiyo amenewa muziganizira mmene mungawagwiritsire ntchito pophunzira ndi anthu.

MAVIDIYO OMWE MUNGAGWIRITSE NTCHITO MUKAMAPHUNZIRA NDI ANTHU KABUKU KA UTHENGA WABWINO

  • Vidiyo yakuti, Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?

    Phunziro 2

    Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?

  • Vidiyo yakuti, Kodi Analemba Baibulo ndi Ndani?

    Phunziro 3

    Kodi Analemba Baibulo ndi Ndani?

  • Vidiyo yakuti, Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

    Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

  • Vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?

    Phunziro 4

    N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?

  • Vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?

    Phunziro 5

    N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?

  • Vidiyo yakuti, Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

    Phunziro 6

    Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

  • Vidiyo yakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

    Phunziro 7

    Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

  • Vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

    Phunziro 8

    N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

  • Vidiyo yakuti, Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?

    Phunziro 10

    Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?

  • Vidiyo yakuti, Kodi Mulungu Amamvetsera Mapemphero Onse?

    Phunziro 12

    Kodi Mulungu Amamvetsera Mapemphero Onse?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena