Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 August tsamba 8
  • Ntchito Zabwino Zimene Yehova Sangaziiwale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Zabwino Zimene Yehova Sangaziiwale
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kupenya ndi Chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mukuitanidwa!
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Beteli N’chiyani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 August tsamba 8
Mlongo akugwira ntchito m’khitchini ya pa Beteli

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ntchito Zabwino Zimene Yehova Sangaziiwale

Atumiki a Yehova onse akhoza kuchita zinthu zomwe Yehova sangaziiwale. Monga mmene kholo limachitira mwana wake akachita zinthu zabwino, Yehova sangaiwale zimene timachita komanso chikondi chimene timasonyeza pa dzina lake. (Mat. 6:20; Aheb. 6:10) N’zoona kuti luso ndi zochitika pa moyo wathu zingakhale zosiyana. Komabe, ngati titachita zonse zomwe tingathe potumikira Yehova, tikhoza kumakhala osangalala. (Agal. 6:4; Akol. 3:23) Kwa zaka zambiri, abale ndi alongo ambirimbiri akhala akutumikira pa Beteli. Kodi nanunso mungakonde kutumikira pa Beteli? Ngati n’zosatheka, kodi pali wina amene mungamulimbikitse kuti ayambe utumikiwu? Kapena mungathandize m’bale kapena mlongo wina amene akuchita utumikiwu kuti apitirizebe?

ONERANI VIDIYO YAKUTI, KODI MUNGAKONDE KUTUMIKIRA PA BETELI? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi cholinga chanu chiyenera kukhala chotani ngati mukufuna kukatumikira pa Beteli?

  • Kodi ndi madalitso ati omwe ena apeza chifukwa chotumikira pa Beteli?

  • Kodi ndi zinthu ziti zomwe munthu ayenera kukwaniritsa kuti ayambe utumiki wa pa Beteli?

  • Kodi mungafunsire bwanji utumiki wa pa Beteli?

M’bale ndi alongo awiri omwe amatumikira pa Beteli akugwira ntchito limodzi pa kompyuta; m’bale akulongedza makatoni a mabuku; m’bale akuchita ukalipentala pa Beteli

Zoyenera Kukwaniritsa Kuti Mukatumikire pa Beteli

  • Muzikonda kwambiri Yehova ndi gulu lake

  • Muyenera kukhala ndi khalidwe loyera komanso kutumikira Yehova ndi chikumbumtima chabwino

  • Muyenera kumavala ndi kudzikongoletsa moyenera monga mtumiki wa Mulungu

  • Muzisankha zosangalatsa zoyenera Akhristu

  • Muyenera kukhala woyambira zaka 19 mpaka 35

  • Muyenera kukhala wathanzi komanso woti simudwala matenda amaganizo

  • Muyenera kukhala kuti mumatha kuwerenga, kulemba komanso kulankhula bwino chinenero cha gawo la nthambi yanu

  • Muyenera kukhala wokonzeka kuchita utumikiwu kwa nthawi yosachepera chaka chimodzi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena