CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 13-16
Musamaope Zilombo Zoopsa
Kumvetsa zimene zilombo zotchulidwa m’chaputala 13 cha buku la Chivumbulutso zimaimira, kungatithandize kuti tisamaziope komanso kuzilambira ngati mmene anthu a m’dzikoli amachitira.
Gwirizanitsani Chilombo Chilichonse ndi Zimene Chikuimira
CHILOMBO
Chinjoka.—Chiv. 13:1.
Chilombo cha mitu 7 ndi nyanga 10.—Chiv. 13:1, 2
Chilombo cha nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa.—Chiv. 13:11
Chifaniziro cha chilombo.—Chiv. 13:15
ULAMULIRO WAMPHAMVU
Ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America
League of Nations ndi bungwe lomwe linabwera pambuyo pake la United Nations
Satana Mdyerekezi
Maboma onse a anthu, omwe akutsutsana ndi Mulungu