CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 20-21
Yehova Amakwaniritsa Zomwe Walonjeza
Yehova anadalitsa Abulahamu ndi Sara chifukwa cha chikhulupiriro chawo powapatsa mwana wamwamuna. Patapita nthawi, kumvera kwawo pamene ankakumana ndi mayesero kunasonyeza kuti ankakhulupirira malonjezo a Yehova a m’tsogolo.
Kodi zomwe ndimachita ndikakumana ndi mayesero zimasonyeza bwanji kuti ndimakhulupirira malonjezo a Yehova? Nanga ndingalimbitse bwanji chikhulupiriro changa?