Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 April tsamba 8
  • Kodi Chofunika Kwambiri kwa Ine N’chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chofunika Kwambiri kwa Ine N’chiyani?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kukwaniritsa Zolinga Zauzimu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kodi Yehova Amalidalitsa Liti Khama la Munthu?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Ndingakwanitse Bwanji Zolinga Zanga?
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 April tsamba 8
Yakobo akulimbana ndi mngelo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Chofunika Kwambiri kwa Ine N’chiyani?

Yakobo analimbana ndi mngelo kuti apeze chinthu chofunika kwambiri chomwe ndi madalitso ochokera kwa Yehova. (Ge 32:24-31; Ho 12:3, 4) Nanga bwanji ifeyo? Kodi timayesetsa kumvera Yehova kuti atidalitse? Mwachitsanzo, ngati zitachitika kuti patsiku la misonkhano tikufunika kugwira ovataimu, kodi tingasankhe kuchita chiyani? Tikamayesetsa kutumikira Yehova pomupatsa nthawi yathu, mphamvu zathu komanso chuma chathu, iye adzatikhuthulira ‘madalitso oti tidzasowa powalandirira.’ (Mki 3:10) Komanso adzatitsogolera, kutiteteza ndiponso kutipatsa zofunikira pamoyo wathu.​—Mt 6:33; Ahe 13:5.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUSASIYE KUKHALA NDI ZOLINGA ZAUZIMU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Mpainiya akugwira ntchito yolembedwa yomasulira m’chinenero cha manja.

    Kodi mlongoyu anayesedwa bwanji ndi zinthu zimene ankazikonda?

  • Mpainiya yemwe uja akugwira ntchito mpaka usiku ndipo muofesi mwake muli mdima.

    Kodi ntchito yathu ingakhale bwanji chiyeso?

  • Timoteyo akuwerenga mpukutu mpaka usiku ndipo waima pafupi ndi windo.

    N’chifukwa chiyani Timoteyo ankafunika kupitirizabe kukhala ndi zolinga ngakhale anali wolimba mwauzimu?​—1Ti 4:16

  • Mpainiya ndi mlongo wina akupereka moni kwa munthu yemwe amaphunzira naye Baibulo asanayambe kuphunzira.

    Kodi chinthu chofunika kwambiri pamoyo wanu n’chiyani?

    Kodi zochita zathu zingasonyeze bwanji kuti timaona kuti kutumikira Yehova ndikofunika kwambiri pamoyo wathu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena