Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 September tsamba 7
  • Kodi Mungapereke Nthawi ndi Mphamvu Zanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungapereke Nthawi ndi Mphamvu Zanu?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Mukhale ndi Zolinga mu Chaka Chautumiki Chikubwerachi​—Thandizani pa Ntchito Yazomangamanga
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Pakufunika Kumanga Nyumba za Ufumu Mofulumira
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Amatumikira Abale Awo Achikristu M’mayiko Ena
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 September tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mungapereke Nthawi ndi Mphamvu Zanu?

M’bale akumwetulira pamene akudula paipi yachitsulo pa ntchito yomanga malo olambirira.

Mogwirizana ndi zimene analosera Yesaya, mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ikukula kwambiri. (Yes 54:2) Chifukwa cha zimenezi, timafunika kumanga Nyumba za Ufumu, Malo a Misonkhano komanso maofesi a nthambi atsopano. Nyumbazi zikamangidwa, zimafunika kuzisamalira ndipo pakapita nthawi, zina zimafunika kuzikonzanso. Popeza pali ntchito zonsezi, kodi tingachite chiyani kuti tipatse Yehova nthawi ndi mphamvu zathu?

  • Tikhoza kumayeretsa nawo Nyumba ya Ufumu nthawi ya kagulu kathu ka utumiki ikafika

  • Tingadzipereke kuti atiphunzitse zofunika kuchita posamalira Nyumba ya Ufumu

  • Tikhoza kulemba Fomu ya Wofuna Kutumikira Mongodzipereka M’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga (DC-50) kuti nthawi ndi nthawi tizithandiza nawo ntchito zomanga ndi kukonzanso nyumba zina zolambiriramo m’dera lathu

  • Tikhoza kulemba Fomu ya Amene Akufuna Utumiki Wongodzipereka (A-19) kuti tidzipereke kwa mlungu umodzi kapena kuposerapo kumathandiza nawo ntchito za pa ofesi ya nthambi yam’dziko lathu kapena panyumba zina za ofesi ya nthambiyo

ONERANI MBALI INA YA VIDIYO YAKUTI PAKUKONZEDWA ZOMANGA BETELI YATSOPANO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Fotokozani mmene takhala tikugwiritsira ntchito mavidiyo ambiri kuposa kale kuyambira 2014.

  • Kuti tizitha kukhala ndi mavidiyo onse ofunikira, kodi gulu lakonza zomanga chiyani, nanga ntchitoyi idzayamba liti ndipo idzatha liti?

  • Kodi anthu odzipereka angathandize bwanji pa ntchito imeneyi?

  • Ngati anthu akufuna kudzathandiza nawo ntchito yomanga ku Ramapo, n’chifukwa chiyani akufunika kulemba fomu (DC-50) komanso kuthandiza nawo ntchito za Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga za m’dera lakwawo?

  • Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yehova akutsogolera ntchitoyi?

  • Kodi tingatani kuti tithandize nawo ntchitoyi ngakhale kuti sitingakwanitse kugwira nawo ntchito yomanga yeniyeniyo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena