CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 1-3
Chifukwa Chake Nsembe Zinkaperekedwa
Nsembe zimene zinkaperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo zinkasangalatsa Yehova komanso zinkaimira nsembe ya dipo ya Yesu kapena madalitso amene nsembeyo idzabweretse.—Ahe 8:3-5; 9:9; 10:5-10.
Mofanana ndi mmene nyama zimene zinkaperekedwa nsembe zinkayenera kukhala zopanda chilema, Yesu anapereka nsembe thupi lake langwiro, lopanda vuto lililonse—1Pe 1:18, 19; onani chithunzi chapachikuto
Mofanana ndi nsembe zopsereza zomwe zinkaperekedwa zathunthu kwa Mulungu, Yesu anapereka moyo wake wonse kwa Yehova
Mofanana ndi mmene anthu omwe ankapereka nsembe zachiyanjano zovomerezeka analili pa mtendere ndi Mulungu, odzozedwa amene amadya zizindikiro pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye amakhala pa mtendere ndi Mulungu