Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 December tsamba 7
  • Kodi Mungakonde Kufunsira Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungakonde Kufunsira Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Mukhale ndi Zolinga mu Chaka Chautumiki Chikubwerachi​—Funsirani Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Amishonale Amapita “Kumalekezero a Dziko Lapansi”
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Sukulu Imene Ophunzira Ake Amathandiza Anthu Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 December tsamba 7
Abale ndi alongo angapo ali m’kalasi ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mungakonde Kufunsira Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?

Kodi muli ndi zaka zoyambira 23 mpaka 65 ndipo mukuchita utumiki wa nthawi zonse? Kodi ndinu wathanzi komanso mutha kukatumikira kulikonse kumene kukufunika ofalitsa ambiri? Ngati mwayankha kuti inde pa mafunsowa, kodi munaganizirapo zolowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? Kungochokera pamene sukuluyi inayamba, mabanja, abale osakwatira komanso alongo osakwatiwa ambirimbiri afunsira kuti akalowe sukuluyi. Koma tikufuna kuti abale ambiri osakwatira afunsire sukulu imeneyi. Mupemphe Yehova kuti akupatseni mtima wofunitsitsa kumusangalatsa komanso kutsanzira Mwana wake. (Sl 40:8; Mt 20:28; Ahe 10:7) Kenako mungachite bwino kuganizira mmene mungachepetsere ntchito kapena maudindo amene muli nawo kuti muyenerere kupita kusukuluyi.

Kodi anthu amene amaliza sukulu imeneyi akhala ndi mwayi wotumikira m’njira ziti? Ena apatsidwa mwayi wokatumikira kudera limene amalankhula chilankhulo china, pomwe ena apatsidwa utumiki wapadera wolalikira m’malo opezeka anthu ambiri m’mizinda. Enanso amakhala oyang’anira madera ogwirizira, oyang’anira madera kapena amishonale. Mukamaganizira zinthu zimene mungachite potumikira Yehova, yesetsani kukhala ndi mtima wa mneneri Yesaya yemwe anati: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”​—Yes 6:8.

ONERANI VIDIYO YAKUTI AMISHONALE AMAGWIRA NTCHITO YOKOLOLA, KENAKO FUNSANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti, ‘Amishonale Amagwira Ntchito Yokolola.’ Mwamuna ndi mkazi wake omwe ndi amishonale ali mu utumiki.

    Kodi amishonale amasankhidwa bwanji?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti, ‘Amishonale Amagwira Ntchito Yokolola.’ Mmishonale ndi mlongo wina akuphunzira Baibulo ndi mzimayi.

    Kodi amishonale akugwira ntchito yotani?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti, ‘Amishonale Amagwira Ntchito Yokolola.’ Mmishonale yemwe ali mumpingo wachinenero chamanja akukambirana ndi m’bale zokhudza fomu ya utumiki wapadera.

    Kodi ndi madalitso otani amene amishonale amapeza?

Kodi mukufuna kudziwa zambiri zokhudza Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? Pitani pamene palembedwa kuti “Mavidiyo” pagawo la Laibulale pa jw.org ndipo pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE TIMACHITA > SUKULU ZOPHUNZITSA BAIBULO. Onerani vidiyo yakuti Sukulu Zophunzitsa Baibulo za ku Africa komanso yakuti Tinapeza Madalitso Ambiri Chifukwa Chophunzitsidwa ndi Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena