Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsamba 3
  • Makolo Muzithandiza Ana Anu Kukhala Odziwa Zinthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo Muzithandiza Ana Anu Kukhala Odziwa Zinthu
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?​—Mbali Yachiwiri
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Makolo Tetezerani Ana Anu!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Ana Athu Ndi Cholowa Chamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 January tsamba 3
Makolo akuphunzitsa ana awo mmene angadzitetezere ndipo anawo akuyeserera mmene anganenere kuti, ‘Ayi!’

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Makolo Muzithandiza Ana Anu Kukhala Odziwa Zinthu

Tikukhala m’dziko limene anthu ambiri amaona kuti zabwino n’zoipa ndipo zoipa n’zabwino. (Yes 5:20) N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amachita zinthu zimene Yehova amadana nazo, monga khalidwe lachiwerewere ndi amuna kapena akazi anzawo. Ana athu akhoza kupusitsidwa ndi anzawo a kusukulu kapena anthu ena kuti achite zoipa. Ndiye kodi mungathandize bwanji ana anu kukonzekera kuti akadzakumana ndi mayesero amenewa kapenanso ena, asadzagonje?

Muzithandiza ana anu kuti azidziwa mfundo za Yehova. (Le 18:3) Mogwirizana ndi msinkhu wawo, muziwaphunzitsa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana. (De 6:7) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndinaphunzitsa ana anga zokhudza kusonyezana chikondi koyenera, kuvala mwaulemu komanso zoti pali zinthu zawo zina zimene ena sayenera kuona? Kodi ana anga angadziwe zoyenera kuchita ngati munthu wina atawaonetsa zinthu zolaula kapena atawauza kuti achite zimene Yehova amadana nazo?’ Kudziwa zoyenera kuchita kungawathandize kuti apewe mavuto ambiri. (Miy 27:12; Mla 7:12) Mukamaphunzitsa ana anu, mumasonyeza kuti mumakonda ana anuwo omwe ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anakupatsani.​—Sl 127:3.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, MANGANI NYUMBA YOLIMBA​—MUZITETEZA ANA ANU KU “ZINTHU ZOIPA” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha mu vidiyo yakuti ‘Mangani Nyumba Yolimba​​—Muziteteza Ana Anu ku ‘Zinthu Zoipa’’ Mayi ndi mwana wake akuonera vidiyo yakuti, ‘Tetezani Ana Anu.’

    N’chifukwa chiyani makolo ena amavutika kuphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana?

  • Chithunzi cha mu vidiyo yakuti ‘Mangani Nyumba Yolimba​​—Muziteteza Ana Anu ku ‘Zinthu Zoipa’’ Makolo akukambirana ndi ana awo awiri mfundo za m’buku la ‘Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso’ komanso mabuku ena.

    N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuphunzitsa ana awo ‘malangizo ndi kaganizidwe ka Yehova’?​—Aef 6:4

  • Chithunzi cha mu vidiyo yakuti ‘Mangani Nyumba Yolimba​​—Muziteteza Ana Anu ku ‘Zinthu Zoipa’’ Makolo a ku Africa akuwerenga mabuku komanso kukambirana ndi ana awo.

    Kudziwa zinthu kumateteza

    Kodi gulu la Yehova latipatsa zinthu ziti zomwe zingathandize makolo kuphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana?​—w19.05 12, bokosi

  • N’chifukwa chiyani nthawi zonse muyenera kumalankhula ndi ana anu nkhani zokhudza kugonana, asanakumane ndi mavuto?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena