Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsamba 7
  • Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kumvetsa Cholinga cha Kulanga
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mulungu Amatilangiza Chifukwa Chotikonda
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kodi Mungatani Kuti Muzilangiza Bwino Ana Anu?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Chilango Chimabala Chipatso cha Mtendere
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 May tsamba 7
Makolo aima pakhomo ndipo akulira pamene akuona mwana wawo wamwamuna yemwe sakufuna kulapa akuchoka panyumba.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

Mawu akuti chilango kwenikweni amatanthauza kupereka malangizo ndiponso kuphunzitsa munthu. Koma amaphatikizaponso kuthandiza munthu amene walakwitsa zinazake. Yehova amatipatsa chilango n’cholinga choti tizimulambira m’njira imene iye amafuna. (Aro 12:1; Ahe 12:10, 11) Nthawi zina chilango chimakhala chopweteka, koma chimathandiza munthu kukhala wolungama komanso kupeza madalitso. (Miy 10:7) Kodi amene akupereka komanso kulandira chilango ayenera kukumbukira zinthu ziti?

Wopereka. Akulu, makolo komanso anthu ena amayesetsa kupereka chilango mokoma mtima komanso mwachikondi ngati mmene Yehova amachitira. (Yer 46:28) Ngakhale chilango chitakhala champhamvu, chiyenera kuperekedwa mogwirizana ndi mmene zinthu zilili komanso mwachikondi.​—Tit 1:13.

Wolandira. Mulimonse mmene malangizo angaperekedwere, sitiyenera kuwakana koma tiyenera kuwagwiritsa ntchito nthawi yomweyo. (Miy 3:11, 12) Monga anthu opanda ungwiro, tonsefe timafunika malangizo omwe amabwera m’njira zosiyanasiyana. Tikhoza kulandira malangizo tikamawerenga Baibulo kapena pamisonkhano ya mpingo. Koma nthawi zina, ena amafunika kupatsidwa malangizo ndi komiti yoweruza mlandu. Tikamamvera malangizo komanso kuwagwiritsa ntchito tidzakhala ndi moyo wabwino panopa, komanso mpaka kalekale.​—Miy 10:17.

ONERANI VIDIYO YAKUTI “YEHOVA AMALANGA ALIYENSE AMENE IYE AMAMUKONDA,” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Yehova Amalanga Aliyense Amene Iye Amamukonda.’ Canon ali mwana akulalikira limodzi ndi makolo ake.

    Kodi moyo wa Canon unali bwanji poyamba, nanga unasintha motani?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Yehova Amalanga Aliyense Amene Iye Amamukonda.’ Canon akukumana ndi akulu ali wachinyamata.

    Kodi Yehova anam’patsa bwanji malangizo mwachikondi?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Yehova Amalanga Aliyense Amene Iye Amamukonda.’ Patapita nthawi, Canon akucheza ndi achinyamata pamisonkhano ya mpingo.

    Muzikonda chilango chochokera kwa Yehova

    Kodi zimene zinachitikira Canon zikutiphunzitsa chiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena