Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsamba 13
  • Muzisonyeza Chikondi M’banja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzisonyeza Chikondi M’banja
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Moyo wa Banja Umene Umakondweretsa Mulungu
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Makiyi Aŵiri a Ukwati Wokhalitsa
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 May tsamba 13
Banja likuimba limodzi kumisonkhano.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzisonyeza Chikondi M’banja

Chikondi ndi guluu ndipo chimagwirizanitsa pamodzi anthu a m’banja. Popanda chikondi, banja lingavutike kuti likhale logwirizana. Kodi amuna, akazi komanso makolo angasonyeze bwanji chikondi m’banja?

Mwamuna wachikondi amaganizira zofuna za mkazi wake, maganizo ake komanso mmene akumvera. (Aef 5:28, 29) Iye amapezera banja lake zofunika pamoyo, komanso amathandiza anthu a m’banja lake kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo amachititsa Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse. (1Ti 5:8) Mkazi wachikondi amagonjera mwamuna wake komanso ‘amamulemekeza kwambiri.’ (Aef 5:22, 33; 1Pe 3:1-6) Mwamuna ndi mkazi ayenera kukhala okonzeka kukhululukirana ndi mtima wonse. (Aef 4:32) Makolo achikondi amachita chidwi ndi mwana aliyense ndipo onse amawaphunzitsa kuti azikonda Yehova. (De 6:6, 7; Aef 6:4) Kodi ana anu akukumana ndi mavuto otani kusukulu? Kodi amatani anzawo akamawakakamiza kuchita zinazake? Anthu onse m’banja akamakondana kwambiri, aliyense amadzimva kukhala wotetezeka.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZISONYEZA CHIKONDI CHOSATHA M’BANJA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muzisonyeza Chikondi Chosatha M’banja.’ Mwamuna ndi mkazi wake akukambirana lemba linalake atachoka kumisonkhano.

    Kodi mwamuna wachikondi amasamalira bwanji mkazi wake?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muzisonyeza Chikondi Chosatha M’banja.’ Mlongo yemwe akuchokera kumisonkhano akumvetsera modekha pamene mwamuna wake yemwe si Mboni akuyankhula ndipo akumutsimikizira kuti amamukonda.

    Kodi mkazi wachikondi amasonyeza bwanji kuti amalemekeza kwambiri mwamuna wake?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muzisonyeza Chikondi Chosatha M’banja.’ Banja likukambirana mfundo zimene zinawasangalatsa kumisonkhano pamene akudya.

    Kodi makolo achikondi amathandiza bwanji ana awo kuti azikonda Mawu a Mulungu?

CHENJEZO LOKHUDZA ZIPANGIZO ZAMAKONO

Zipangizo zamakono zikhoza kukuwonongerani nthawi yomwe mukanaigwiritsa ntchito polimbitsa chikondi chanu m’banja. Makolo angafunike kuika malire pa nthawi imene iwowo komanso ana awo azithera pogwiritsa ntchito zipangizozi. Kuwonjezera pamenepo, makolo akufunika kusankha ngati ana awo angamacheze ndi anthu ena pa intaneti komanso anthu amene angamacheze nawowo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena