MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kukhala Olimba Mtima Sikovuta Kwambiri
Munthu wolimba mtima amakhala wamphamvu komanso saopa. Koma izi sizikutanthauza kuti iye sakhaliratu wopanda mantha. M’malomwake, zikutanthauza kuti iye amachitabe zimene akufunika kuchitazo ngakhale kuti akuchita mantha. Yehova ndi amene amatithandiza kukhala olimba mtima. (Sl 28:7) Kodi achinyamata angasonyeze bwanji kulimba mtima?
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUSAMATSANZIRE ANTHU AMANTHA, KOMA OLIMBA MTIMA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi achinyamata amakumana ndi zinthu ziti zimene zimafunika kulimba mtima?
Kodi ndi nkhani za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kukhala olimba mtima?
Kodi kulimba mtima kumathandiza bwanji ifeyo komanso anthu ena omwe akutiona?