MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Tingaphunzire kwa Samueli
Samueli anakhala wokhulupirika kwa Yehova kwa moyo wake wonse. Ali wachinyamata, anakana kuchita zinthu mwachinyengo ngati mmene ankachitira ana a Eli, Hofeni ndi Pinihasi. (1Sa 2:22-26) Samueli anapitiriza kukula ndipo Yehova anali naye. (1Sa 3:19) Iye atakula, anapitirizabe kutumikira Yehova ngakhale pamene ana ake anasiya.—1Sa 8:1-5.
Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Samueli? Ngati ndinu wachinyamata, muzikhala wotsimikiza kuti Yehova amamvetsa mavuto amene mukukumana nawo komanso mmene mukumvera. Iye angakuthandizeni kuti mukhale wolimba mtima. (Yes 41:10, 13) Ngati ndinu kholo, ndipo mwana wanu satumikira Yehova, mungalimbikitsidwe kudziwa kuti Samueli sankakakamiza ana ake, omwe anali atakula, kuti akhalebe okhulupirika n’kumatsatira mfundo zabwino za Yehova. M’malomwake, anasiya nkhaniyi m’manja mwa Mulungu ndipo anakhalabe wokhulupirika n’kumasangalatsa Atate wake wakumwamba, Yehova. Mwina chitsanzo chanu chabwino chingathandize mwana wanu kubwerera kwa Yehova.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE TINGAPHUNZIRE KUCHOKERA KWA SAMUELI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi Samueli ali mwana anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima?
Kodi Danny anasonyeza bwanji kulimba mtima?
Kodi Samueli atakula, anasonyeza bwanji chitsanzo chabwino?
Yehova amathandiza anthu amene sasunthika pochita zabwino
Kodi makolo a Danny anasonyeza bwanji chitsanzo chabwino?