MBIRI YA MOYO WANGA
Ndadalitsidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Ndinaphunzira kwa Anthu Ena
NDILI wamng’ono ndinkavutika kwambiri kulalikira. Nditakula ndinapatsidwa utumiki umene ndinkaona kuti sindinali woyenera kuchita. Ndikufotokozerani za anthu ena achitsanzo chabwino amene anandithandiza kuti ndisiye kuchita mantha komanso kuti ndilandire madalitso ambiri pa zaka 58 zimene ndakhala mu utumiki wa nthawi zonse.
Ndinabadwira ku Canada mumzinda wa Quebec City, umene uli m’chigawo cha Quebec ndipo anthu ake amalankhula Chifulenchi. Makolo anga anali Louis ndi Zélia ndipo ankandisamalira mwachikondi kwambiri. Bambo anga anali amanyazi koma ankakonda kuwerenga. Ineyo ndinkakonda kulemba nkhani ndipo ndinkafuna kuti ndidzakhale mtolankhani.
Ndili ndi zaka pafupifupi 12, munthu wina dzina lake Rodolphe Soucy yemwe ankagwira ntchito ndi bambo anabwera kunyumba kwathu limodzi ndi mnzake. Iwo anali a Mboni za Yehova. Sindinkadziwa zambiri zokhudza a Mboni ndipo sindinkachita chidwi kwenikweni ndi chipembedzochi. Koma ndinkasangalala chifukwa ankayankha bwino mafunso pogwiritsa ntchito Baibulo. Makolo anga ankasangalalanso choncho tinavomera kuti azitiphunzitsa Baibulo.
Pa nthawiyo, ndinkapita kusukulu ya Chikatolika. Nthawi zina, ndinkakambirana ndi anzanga kusukulu mfundo zimene tinkaphunzira m’Baibulo ndi a Mboni. Koma kenako aphunzitsi, omwe anali ansembe, anadziwa zimene ndinkachita. M’malo mogwiritsa ntchito Malemba kuti asonyeze kuti zimene ndinkanena sizinali zoona, mmodzi wa iwo anangoyamba kundinena pamaso pa kalasi yonse kuti ndine woukira. Ngakhale kuti ndinachita mantha, zimenezi zinandithandiza kuzindikira kuti zimene sukuluyo inkaphunzitsa zokhudza chipembedzo zinali zosagwirizana ndi Baibulo. Ndiye ndinazindikira kuti ndiyenera kuchoka pasukuluyo. Makolo anga anavomereza ndipo ndinayamba kupita kusukulu ina.
NDINAYAMBA KUKONDA UTUMIKI
Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo koma sindinkapita patsogolo chifukwa ndinkaopa kulalikira kunyumba ndi nyumba. Tchalitchi cha Katolika chinali champhamvu kwambiri ndipo chinkatsutsa koopsa ntchito yathu yolalikira. Mtsogoleri wandale wamkulu ku Quebec, dzina lake Maurice Duplessis ankagwirizana kwambiri ndi tchalitchichi. Iye ankalola kuti magulu a anthu azizunza a Mboni. Choncho munthu ankafunika kulimba mtima kwambiri kuti alalikire.
M’bale wina amene anandithandiza kuti ndisiye kuchita mantha anali John Rae. M’baleyu analowa kalasi ya nambala 9 ya Sukulu ya Giliyadi. John anali wodziwa zambiri, wodekha, wosadzikweza komanso wosavuta kucheza naye. Sankakonda kundipatsa malangizo koma chitsanzo chake n’chimene chinandithandiza kwambiri. John ankavutika kulankhula Chifulenchi choncho ndinkayenda naye mu utumiki kuti ndizimuthandiza. Kuchita zinthu ndi John kunandithandiza kuti ndilimbe mtima n’kukhala wa Mboni za Yehova. Ndinabatizidwa pa 26 May 1951 ndipo apa n’kuti patapita zaka 10 kuchokera pamene ndinakumana ndi a Mboni koyamba.
Chitsanzo chabwino cha John Rae (A) chinandithandiza ineyo (B) kuti ndisiye kuopa kulalikira kunyumba ndi nyumba
Mumpingo wathu ku Quebec City munali apainiya ambiri. Chitsanzo chawo chinandithandiza kuti nanenso ndiyambe upainiya. Tinkalalikira kunyumba ndi nyumba pogwiritsa ntchito Baibulo basi. Popeza tinalibe mabuku, tinkafunika kugwiritsa ntchito Malemba mwaluso. Choncho ndinayesetsa kuti ndidziwe malemba ambiri n’cholinga choti ndiziphunzitsa bwino choonadi. Koma anthu ambiri ankakana kuwerenga Baibulo ngati silinali Baibulo lovomerezedwa ndi Akatolika.
Mu 1952, ndinakwatira mlongo wokhulupirika dzina lake Simone Patry. Tinasamukira ku Montreal, ndipo chaka chisanathe tinakhala ndi mwana wamkazi dzina lake Lise. Ngakhale kuti ndinasiya upainiya nditangotsala pang’ono kukwatira, ine ndi Simone tinkakhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti tizithandiza kwambiri mumpingo.
Panapitanso zaka 10 ndisanayambe kuganizira kwambiri zowonjezera utumiki wanga. Mu 1962 ndinapita ku Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Beteli ya ku Canada imene inatenga mwezi umodzi. Anandiika chipinda chimodzi ndi m’bale Camille Ouellette. Khama la m’baleyu linandichititsa chidwi kwambiri, makamaka chifukwa choti nayenso anali ndi banja. Kalelo sizinkachitikachitika ku Quebec kuti munthu azichita upainiya ali ndi mwana, koma izi n’zimene Camille ankafuna kuchita. Iye anandilimbikitsa kuti ndiganizire zimene ndingachite pa moyo wanga. Patangopita miyezi yochepa, ndinazindikira kuti ndikhoza kuyambiranso upainiya wokhazikika. Ena ankaona kuti sindinasankhe zinthu mwanzeru koma sindinabwerere m’mbuyo podziwa kuti Yehova adzandithandiza kuti ndichite zambiri mu utumiki.
TINABWERERA KU QUEBEC CITY KUKACHITA UPAINIYA WAPADERA
Mu 1964, ine ndi mkazi wanga tinauzidwa kuti tikachite upainiya wapadera mumzinda wa kwathu wa Quebec City ndipo tinatumikirako kwa zaka zingapo. Anthu anali atasiya kutsutsa kwambiri ntchito yolalikira koma panali ena amene ankatitsutsabe.
Loweruka lina masana, ndinamangidwa m’katauni kena kapafupi ndi kwathu kotchedwa Sainte-Marie. Wapolisi wina ananditsekera m’ndende chifukwa cholalikira kunyumba ndi nyumba popanda chilolezo. Kenako anandipititsa kwa woweruza woopsa dzina lake Baillargeon. Woweruzayu anandifunsa kuti, Loya wako akhala ndani? Ndinamuyankha kuti akhala Glen How,a yemwe anali loya wodziwika bwino pa nkhani yoteteza a Mboni kukhoti. Atangomva zimenezi, anachita mantha n’kunena kuti: “Iii ayi, bola asakhale ameneyo!” Kenako akukhoti anandiuza kuti nkhani yatha, palibenso mlandu.
Popeza anthu ambiri ku Quebec ankatitsutsa, zinali zovuta kupeza malo ochitira misonkhano. Choncho mpingo wathu unangopeza kanyumba kenakake koimika galimoto. Kanali kakale komanso kankazizira kwambiri m’nyengo yozizira. Pofuna kuti m’kanyumbako muzitenthera, abale ankagwiritsa ntchito mbaula yoyendera mafuta. Nthawi zambiri, tinkafika maola angapo misonkhano isanayambe n’kumalimbikitsana kwinaku tikuotha.
N’zosangalatsa kuona kuti ntchito yolalikira yakhala ikuyenda bwino kwambiri. Mwachitsanzo, m’ma 1960 kunali mipingo yochepa kwambiri tikaphatikiza madera a ku Quebec City, Côte-Nord ndi Gaspé Peninsula. Koma panopa kuli madera oposa awiri m’malo amenewa ndipo kuli Nyumba za Ufumu zokongola kwambiri.
TINAPEMPHEDWA KUTI TIGWIRE NTCHITO YOYENDAYENDA
Mu 1977, ndinakhala nawo pamsonkhano wa oyang’anira oyendayenda mumzinda wa Toronto ku Canada
Mu 1970, ine ndi Simone tinapemphedwa kuti tiyambe ntchito yoyang’anira dera. Kenako mu 1973, tinayamba ntchito yoyang’anira chigawo. Pa zaka zimenezi, ndinaphunzira zambiri kwa abale aluso monga Laurier Saumurb ndi David Splane,c omwenso anali oyang’anira oyendayenda. Msonkhano wadera uliwonse ukatha, ine ndi M’bale Splane tinkauzana zimene tingachite kuti tiwonjezere luso lathu lophunzitsa. Tsiku lina m’baleyu anandiuza kuti: “Léonce, nkhani yako yomaliza ija inandisangalatsa. Inali yabwino, koma zimene unanena zija ine ndikanatha kuzikamba mu nkhani zitatu.” Ndinkaika mfundo zambirimbiri munkhani zanga. Choncho ndinafunika kupewa kuchulutsa gaga m’diwa.
Ndinatumikira m’mizinda yosiyanasiyana kum’mawa kwa Canada
Udindo wa oyang’anira chigawo unali wolimbikitsa oyang’anira madera. Koma ofalitsa ambiri ku Quebec ankandidziwa bwino. Nthawi zambiri ndikafika m’dera lawo ankafuna kuti ayende nane mu utumiki. Ngakhale kuti ndinkasangalala kulalikira nawo, sindinkakhala ndi nthawi yokwanira yoti ndilimbikitse woyang’anira dera. Woyang’anira dera wina anandiuza kuti: “Zili bwino kuti mumapeza nthawi yolimbikitsa abale koma musaiwale kuti mukundiyendera ineyo mlungu uno. Nanenso ndikufunika kulimbikitsidwa.” Malangizo amenewa anandithandiza kwambiri.
Mu 1976, ndinamva chisoni kwambiri mkazi wanga Simone atayamba kudwala kwambiri kenako n’kumwalira. Anali mkazi wabwino kwambiri chifukwa anali ndi mtima wodzipereka komanso ankakonda Yehova. Kulalikira mwakhama kunandithandiza kuti ndipirire vutoli ndipo ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa chondithandiza pa nthawi yovutayi. Patapita nthawi, ndinakwatira mlongo wina wolankhula Chingelezi dzina lake Carolyn Elliott. Mlongoyu anali mpainiya wakhama amene anabwera ku Quebec kudzalalikira kudera limene kunalibe ofalitsa okwanira. Carolyn ndi wosavuta kucheza naye ndipo amaganizira anthu, makamaka amanyazi kapena amene samasuka ndi anthu. Wandithandiza kwambiri pa ntchito yanga yoyendayenda.
CHAKA CHOFUNIKA KWAMBIRI
Mu January 1978, ndinapemphedwa kuti ndikaphunzitse Sukulu ya Utumiki Waupainiya yoyamba ku Quebec. Ndinachita mantha kwambiri chifukwa maphunzirowo anali achilendo kwa ophunzira komanso ineyo. Mwamwayi, m’kalasi yoyamba imene ndinaphunzitsa munali anthu ambiri amene anali atachita upainiya kwa nthawi yaitali. Ngakhale kuti ndinali mlangizi, ndinaphunzira zambiri kwa ophunzirawo.
Kenako m’chaka chomwecho, msonkhano wa mayiko unachitikira musitediyamu ya ku Montreal. Unali msonkhano waukulu kwambiri umene unachitika ku Quebec chifukwa panali anthu oposa 80,000. Ndinapemphedwa kuti ndigwire ntchito mu Dipatimenti ya Zofalitsa Nkhani. Ndipo ndinalankhula ndi atolankhani ambiri komanso ndinasangalala kuona kuti analemba zinthu zabwino zokhudza msonkhanowu. Panalembedwa nkhani mahandiredi angapo ndipo kwa maola oposa 20 anaulutsa nkhani zambiri pa TV ndi wailesi. Choncho anthu ambiri anali ndi mwayi womva uthenga wathu.
TINASAMUKIRA KUGAWO LINA
Mu 1996, utumiki wanga unasintha kwambiri. Kuyambira pamene ndinabatizidwa, ndakhala ndikutumikira m’dera la Chifulenchi ku Quebec koma apa ndinapemphedwa kuti ndikatumikire kuchigawo cha Chingelezi ku Toronto. Ndinkadzikayikira kwambiri ndipo ndinkaopa kukamba nkhani m’Chingelezi chothyokathyoka. Ndinkafunika kupemphera kwambiri kwa Yehova ndiponso kumudalira.
Ngakhale kuti poyamba ndinkachita mantha, kunena zoona zaka ziwiri zimene tinatumikira ku Toronto zinali zosangalatsa. Carolyn anandithandiza moleza mtima kuti ndizilankhula Chingelezi bwinobwino ndipo abale ankandithandizanso. Pasanapite nthawi, tinapeza anzathu atsopano.
Kuwonjezera pa kukonzekera msonkhano wadera, ndinkakonda kulalikira kwa ola limodzi Lachisanu lililonse madzulo. Mwina ena ankadabwa kuti, ‘Mawa tili ndi msonkhano, ndiye n’chifukwa chiyani akulowa mu utumiki?’ Koma ndinkaona kuti kulalikira kunkandithandiza kuti maganizo anga akhale m’malo. Mpaka pano ndimaona kuti kulalikira kumandithandiza kuti ndizisangalala.
Mu 1998, ine ndi Carolyn tinapemphedwa kuti tikachite upainiya wapadera ku Montreal. Kwa zaka zingapo, ndinkathandizanso kutsogolera ntchito yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri komanso kulankhula ndi ofalitsa nkhani n’cholinga choti tithetse maganizo olakwika okhudza Mboni za Yehova. Panopa ine ndi mkazi wanga timakonda kulalikira anthu amene angobwera kumene ku Canada omwe nthawi zambiri amakhala ofunitsitsa kuphunzira Baibulo.
Ine ndi mkazi wanga Carolyn
Ndikaganizira zaka 68 kuchokera pamene ndinabatizidwa, ndimaona kuti Yehova wandidalitsa kwambiri. Ndimasangalala chifukwa ndinayamba kukonda kwambiri kulalikira komanso ndathandiza anthu ambiri kudziwa choonadi. Mwana wanga Lise ndi mwamuna wake anayamba upainiya wokhazikika ana awo atakula. Ndimasangalala kwambiri kuona kuti Lise ndi wakhama mu utumiki. Ndimayamikiranso kwambiri Akhristu anzanga omwe anandithandiza kuti ndikule mwauzimu komanso kuti ndizichita bwino utumiki uliwonse umene ndinapatsidwa. Ndazindikira kuti tikhoza kukhala okhulupirika pa utumiki wathu ngati timadalira mzimu woyera wa Yehova. (Sal. 51:11) Ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa chondipatsa mwayi wamtengo wapatali wotamanda dzina lake.—Sal. 54:6.
a Onani mbiri ya moyo wa Glen How mu Galamukani! ya Chingelezi ya April 22, 2000 pa mutu wakuti “The Battle Is Not Yours, but God’s.”
b Onani mbiri ya moyo wa Laurier Saumur mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1976 pa mutu wakuti “I Found Something Worth Fighting For.”
c M’bale David Splane ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.