Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w20 May tsamba 8-11
  • Mafumu Awiri Olimbana M’nthawi ya Mapeto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafumu Awiri Olimbana M’nthawi ya Mapeto
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi “Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi ya Mapeto Ndi Ndani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Yehova Waulula “Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa”
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndi Ndani Panopa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Ulendo Wautali wa Mphamvu za Dziko Uyandikira Mapeto Ake
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
w20 May tsamba 8-11

Mafumu Awiri Olimbana M’nthawi ya Mapeto

Maulosi omwe ali patchatichi akufotokoza zinthu zina zomwe zinachitika pa nthawi yofanana. Maulosiwa amatitsimikizira kuti tikukhala mu “nthawi yamapeto.”​—Dan. 12:4.

Tchati chosonyeza maulosi komanso mfumu ya kumpoto ndi ya kummwera kuyambira m’chaka cha 1870 mpaka masiku ano.
  • Tchati choyamba, chosonyeza maulosi a zinthu zina zomwe zinachitika pa nthawi yofanana kuyambira m’ma 1870 mpaka m’ma 1918. Zaka zoyambira m’ma 1914 kupita m’tsogolo zafotokozedwa kuti ndi nthawi yamapeto. Ulosi 1: Chilombo cha mitu 7 chomwe chinaonekera chaka cha 1870 chisanafike. Pa nthawi yankhondo yoyamba yapadziko lonse, mutu wa 7 wachilombochi unavulazidwa. Kuyambira mu 1917, mutu wa 7 uja unachira ndipo chilombocho chinakhalanso ndi mphamvu. Ulosi 2: Mu 1870, mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera inadziwika. Mu 1871, mfumu ya kumpoto inali ulamuliro wa Germany. Poyamba mfumu ya ku m’mwera inali ulamuliro wa Great Britain, koma mu 1917 inalowedwa m’malo ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britan ndi America. Ulosi 3: Kuyambira m’ma 1870, m’bale Charles T. Russell ndi anzake anali ngati ‘mthenga.’ Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1880, magazini ya ‘Zion’s Watch Tower’ inalimbikitsa anthu kuti azilalikira uthenga wabwino. Ulosi 4: Kuyambira 1914, nthawi yokolola. Nansongole analekanitsidwa ndi tirigu. Ulosi 5: Kuyambira mu 1917, ulamuliro wa mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo unadziwika. Zochitika zinanso: Nkhondo yoyamba yapadziko lonse, kuyambira mu 1914 mpaka 1918. Zochitika zokhudza anthu a Yehova: Kuyambira mu 1914 mpaka mu 1918, Ophunzira Baibulo a ku Britain ndi Germany anamangidwa. Mu 1918, abale akulikulu ku United States anamangidwa.
    Ulosi 1.

    Malemba Chiv. 11:7; 12:13, 17; 13:1-8, 12

    Ulosi “Chilombo” chakhala chikulamulira kwa zaka zoposa 3,000. Mu nthawi yamapeto, mutu wake wa 7 unavulazidwa. Kenako, unachira ndipo “dziko lonse lapansi” linatsatira chilombocho. Satana anagwiritsa ntchito chilombochi ‘kuchita nkhondo ndi otsala a mbewu’ ya mkazi.

    Kukwaniritsidwa Pambuyo pa Chigumula cha Nowa, maboma otsutsana ndi Yehova anayamba kulamulira anthu. Ndiye patapita zaka zoposa 3,000, pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, boma la Britain linachepa mphamvu kwambiri. Koma linakhalanso ndi mphamvu litagwirizana ndi dziko la United States. Mu nthawi yamapeto, Satana akugwiritsa ntchito maboma onse padziko lapansi kuzunza anthu a Mulungu.

  • Ulosi 2.

    Lemba Dan. 11:25-45

    Ulosi Kulimbana kwa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera m’nthawi yamapeto.

    Kukwaniritsidwa Dziko la Germany linamenyana ndi mayiko a Britain ndi America. Mu 1945 boma la Soviet Union ndi mayiko ogwirizana nalo linakhala mfumu ya kumpoto. Mu 1991, ulamuliro wa Soviet Union unatha ndipo m’kupita kwa nthawi dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo ndi amene anakhala mfumu ya kumpoto.

  • Ulosi 3.

    Malemba Yes. 61:1; Mal. 3:1; Luka 4:18

    Ulosi Ufumu wa Mesiya usanakhazikitsidwe, Yehova anatumiza “mthenga” wake kuti ‘akakonze njira.’ Mthengayu anayamba kulengeza “uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.”

    Kukwaniritsidwa Kuyambira m’ma 1870, M’bale Russell ndi anzake ankaphunzira Baibulo mwakhama kuti azifotokoza bwino mfundo zachoonadi. M’ma 1880, anazindikira kuti n’zofunika kwambiri kuti atumiki a Mulungu azilalikira. Anatulutsa nkhani zokhudza kulalikira monga yakuti “Alaliki 1,000 Akufunika” ndi yakuti “Anadzozedwa Kuti Azilalikira.”

  • Ulosi 4.

    Lemba Mat. 13:24-30, 36-43

    Ulosi Mdani anafesa namsongole m’munda wa tirigu. Namsongoleyo anakula n’kufika pophimba tirigu. Nthawi yokolola itakwana namsongole analekanitsidwa ndi tirigu.

    Kukwaniritsidwa Kuyambira chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kusiyana pakati pa Akhristu oona ndi onyenga kunayamba kuonekera. M’nthawi yamapeto, Akhristu oona anayamba kusonkhanitsidwa mumpingo komanso kulekanitsidwa ndi Akhristu onyenga.

  • Ulosi 5.

    Lemba Dan. 2:31-33, 41-43

    Ulosi Mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo a chifaniziro chopangidwa ndi mitundu yosiyanasiyana yazitsulo.

    Kukwaniritsidwa Dongo likuimira anthu wamba mu ulamuliro wa Britain ndi America omwe amatha kuchita zinthu zotsutsana ndi ulamulirowu. Anthu amenewa amalepheretsa ulamuliro wamphamvuwu kusonyeza mphamvu zake zonse.

  • Tchati chachiwiri, chosonyeza maulosi a zinthu zina zomwe zinachitika pa nthawi yofanana kuyambira m’ma 1919 mpaka mu 1945. Mfumu ya kumpoto inali ulamuliro wa Germany mpaka mu 1945. Mfumu ya kum’mwera inadziwika kuti ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Ulosi 6: Mu 1919, Akhristu odzozedwa anasonkhanitsidwa mumpingo womwe unayeretsedwa. Kuyambira mu 1919, ntchito yolalikira inapitirira ndipo inawonjezereka. Ulosi 7: Mu 1920, bungwe la League of Nations linakhazikitsidwa ndipo linagwira ntchito mpaka kumayambiriro kwa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Zochitika zinanso: Ulosi 1, chilombo cha mitu 7 chikuonekerabe. Ulosi 5, ulamuliro wa mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo ukupitirira. Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse kuyambira mu 1939 mpaka mu 1945. Zochitika zokhudza anthu a Yehova: Ku Germany, kuyambira mu 1939 mpaka mu 1945, a Mboni oposa 11,000 anamangidwa. Ku Britain, kuyambira mu 1939 mpaka mu 1945, a Mboni pafupifupi 1,600 anamangidwa. Ku United States, kuyambira mu 1940 mpaka mu 1944, anthu olusa anachitira zankhanza a Mboni maulendo oposa 2,500.
    Ulosi 6.

    Malemba Mat. 13:30; 24:14, 45; 28:19, 20

    Ulosi “Tirigu” anasonkhanitsidwa n’kumuika “m’nkhokwe” ndipo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anaikidwa kuti aziyang’anira ‘antchito apakhomo.’ Ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ inayamba kufalikira “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”

    Kukwaniritsidwa Mu 1919 kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anaikidwa kuti aziyang’anira anthu a Mulungu. Kuyambira nthawiyi, Ophunzira Baibulo akhala akuchita khama pogwira ntchito yolalikira. Masiku ano, a Mboni za Yehova akulalikira m’mayiko oposa 200 ndipo amafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 1,000.

  • Ulosi 7.

    Malemba Dan. 12:11; Chiv. 13:11, 14, 15

    Ulosi Chilombo cha nyanga ziwiri chinatsogolera popanga “chifaniziro cha chilombo” ndipo chinapereka “mpweya ku chifaniziro cha chilombo chija.”

    Kukwaniritsidwa Ulamuliro wa Britain ndi America unatsogolera pokhazikitsa bungwe la League of Nations. M’bungweli munalowanso mayiko ena. Patapita nthawi, mfumu ya kumpoto nayonso inalowamo koma inangokhalamo kuyambira mu 1926 kufika mu 1933. Monga zilili ndi bungwe la United Nations (UN) panopa, anthu ankakhulupiriranso kuti bungweli lingabweretse mtendere, zomwe ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungakwanitse.

  • Tchati chachitatu, chosonyeza maulosi a zinthu zina zomwe zinachitika pa nthawi yofanana kuyambira m’ma 1945 mpaka mu 1991. Mfumu ya kumpoto inadziwika kuti ndi Soviet Union ndi mayiko ogwirizana nalo mpaka mu 1991, kenako inadziwika kuti ndi dziko la Russia ndi mayiko ogwirizana nalo. Mfumu ya kum’mwera inadziwika kuti ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Ulosi 8: Utsi wa bomba, kusonyeza mmene ulamuliro wa Britain ndi America wawonongera zinthu pankhondo. Ulosi 9: Bungwe la United Nations linakhazikitsidwa mu 1945 ndipo linalowa m’malo mwa bungwe la League of Nations. Zochitika zinanso: Ulosi 1, chilombo cha mitu 7 chikuonekerabe. Ulosi 5, ulamuliro wa mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo ukupitirira. Ulosi 6, mu 1945 ofalitsa oposa 156,000. Mu 1991, ofalitsa oposa 4,278,000. Zochitika zokhudza anthu a Yehova: Ku Soviet Union kuyambira mu 1945 mpaka m’ma 1950, a Mboni masauzande ambiri anatumizidwa ku Siberia.
    Ulosi 8.

    Lemba Dan. 8:23, 24

    Ulosi Mfumu ya maonekedwe oopsa “idzawononga zinthu zambiri.”

    Kukwaniritsidwa Ulamuliro wa Britain ndi America wapha anthu ambiri komanso kuwononga zinthu zambiri. Mwachitsanzo, pa nthawi yankhondo yachiwiri yapadziko lonse dziko la United States linaponya mabomba awiri m’dziko la adani awo. Mabombawo anawononga kwambiri kuposa mabomba onse m’mbuyomo.

  • Ulosi 9.

    Malemba Dan. 11:31; Chiv. 17:3, 7-11

    Ulosi “Chilombo chofiira kwambiri” cha nyanga 10, chomwenso ndi mfumu ya 8, chinatuluka kuphompho. Buku la Danieli limanena kuti mfumuyi ndi “chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko.”

    Kukwaniritsidwa Pa nthawi yankhondo yachiwiri yapadziko lonse bungwe la League of Nations linathetsedwa. Nkhondoyi itatha bungwe la UN, ‘linaikidwa m’malomwake.’ Mofanana ndi la League of Nations, bungwe la UN limapatsidwa ulemerero woyenera Ufumu wa Mulungu.

  • Tchati cha nambala 4, chosonyeza maulosi a zinthu zina zomwe zinachitika pa nthawi yofanana kuyambira m’nthawi yamapeto mpaka pa nkhondo ya Aramagedo. Mfumu ya kumpoto inadziwika kuti ndi dziko Russia ndi mayiko ogwirizana nalo. Mfumu ya kum’mwera inadziwika kuti ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Ulosi 10: Olamulira akulengeza za ‘bata ndi mtendere.’ Kenako, chisautso chachikulu chikuyamba. Ulosi 11: Mayiko akuukira mabungwe azipembedzo zonyenga. Ulosi 12: Maboma onse a padziko lapansi akuukira anthu a Mulungu. Odzozedwa amene adakali padzikoli akutengedwa kupita kumwamba. Ulosi 13: Nkhondo ya Aramagedo. Wokwera pahatchi yoyera wapambana pankhondo. Chilombo cha mitu 7 chikuwonongedwa, chifaniziro chachikulu chikuphwanyidwa kumapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo. Zochitika zinanso: Ulosi 1, chilombo cha mitu 7 chikuonekerabe mpaka pa Aramagedo. Ulosi 5, ulamuliro wa mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo ukupitirira mpaka pa Aramagedo. Ulosi 6, masiku ano ofalitsa oposa 8,580,000. Zochitika zokhudza anthu a Yehova: Mu 2017, akuluakulu aboma la Russia anamanga a Mboni komanso kulanda ofesi ya nthambi.
  • Ulosi 10 ndi 11.

    Malemba 1 Ates. 5:3; Chiv. 17:16

    Ulosi Mayiko akulengeza za “bata ndi mtendere” ndipo “nyanga 10” komanso “chilombo” zikuukira “hule” ndi kuliwononga. Kenako mitundu ya anthu ikuwonongedwa.

    Kukwaniritsidwa Mayiko adzanena kuti akwanitsa kubweretsa bata ndi mtendere. Kenako mayiko amene ali m’bungwe la UN adzawononga zipembedzo zonyenga. Kumeneku kudzakhala kuyamba kwa chisautso chachikulu. Chisautsochi chidzafika kumapeto pa Aramagedo, Yesu akadzawononga dziko lonse la Satanali.

  • Ulosi 12.

    Malemba Ezek. 38:11, 14-17; Mat. 24:31

    Ulosi Gogi adzaukira anthu a Mulungu. Kenako, angelo adzasonkhanitsa “osankhidwa.”

    Kukwaniritsidwa Mfumu ya kumpoto limodzi ndi maboma onse a padziko lapansi adzaukira anthu a Mulungu. Zimenezi zikadzangoyamba kuchitika, Akhristu odzozedwa omwe adakali padzikoli adzatengedwa kupita kumwamba.

  • Ulosi 13.

    Malemba Ezek. 38:18-23; Dan. 2:34, 35, 44, 45; Chiv. 6:2; 16:14, 16; 17:14; 19:20

    Ulosi “Wokwera” pa “hatchi yoyera” “anapambana pa nkhondo yolimbana” ndi Gogi ndi asilikali ake. “Chilombo” “chinaponyedwa m’nyanja ya moto” ndipo mwala unaphwanya chifaniziro chachikulu.

    Kukwaniritsidwa Yesu, amene ndi Mfumu yomwe ikulamulira mu Ufumu wa Mulungu adzapulumutsa anthu a Mulungu. Iye pamodzi ndi anzake 144,000 komanso angelo, adzawononga maboma onse omwe adzaukira anthu a Mulungu. Amenewa adzakhala mapeto a dziko la Satanali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena