Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp21 No. 1 tsamba 3-4
  • Zimene Anthu Amanena Zokhudza Kupemphera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Anthu Amanena Zokhudza Kupemphera
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Mapemphero Amene Amayankhidwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Kupemphera Kumathandizadi?
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
wp21 No. 1 tsamba 3-4
Anthu am’mayiko osiyanasiyana akupemphera komanso kudalira Mulungu kuti aziwatsogolera.

Zimene Anthu Amanena Zokhudza Kupemphera

“Ndikamapemphera ndimamva ngati Mulungu ali pambali panga ndipo wandigwira dzanja n’kumanditsogolera ndikaona kuti ndasochera.”​—MARÍA.

“Mkazi wanga anamwalira atavutika ndi khansa kwa zaka 13. Ndikukumbukira kuti pa nthawiyo ndinkapemphera kwa Mulungu tsiku lililonse ndipo ndinkaona kuti akundimvetsera komanso kumvetsa mmene zinkandipwetekera. Ndikapemphera ndinkapeza mtendere wamumtima.”​—RAÚL.

“Pemphero ndi mphatso yabwino kwambiri imene Mulungu watipatsa anthufe.”​—ARNE.

María, Raúl, Arne komanso anthu ena ambiri amaona kuti pemphero ndi mphatso yapadera. Iwo amaona kuti akamapemphera amatha kulankhula ndi Mulungu, kumuthokoza komanso kumupempha kuti awathandize. Amakhulupirira ndi mtima wonse lonjezo la m’Baibulo lokhudza pemphero lakuti: “Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”​—1 Yohane 5:14.

Koma anthu ambiri sakhulupirira kwenikweni zimene Baibulo limanena pa nkhani ya pemphero. Mwachitsanzo, munthu wina dzina lake Steve ananena kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 17, anzanga atatu anafa pa ngozi. Mmodzi anafa pa ngozi ya galimoto pomwe awiri enawo anamira m’nyanja.” Kodi Steve anatani? Iye anati: “Ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kumvetsa zimene zinachitikazi, koma sanandiyankhe. Ndiye ndinaona kuti palibe chifukwa chopempherera.” Anthu ambiri amene amaona kuti mapemphero awo sanayankhidwe amayamba kuganiza kuti kupemphera n’kosathandiza.

Anthu enanso ali ndi zifukwa zina zowachititsa kuganiza kuti kupemphera n’kosathandiza. Mwachitsanzo, ena amanena kuti Mulungu amadziwa zonse choncho amadziwa kale zimene timafunikira komanso mavuto athu ndiye palibe chifukwa chomuuzira m’pemphero.

Pomwe ena amakhulupirira kuti Mulungu samvetsera mapemphero awo chifukwa cha zimene analakwitsa m’mbuyomu. Munthu wina dzina lake Jenny anati: “Vuto langa n’lakuti ndinachita zinthu zimene ndimanong’oneza nazo bondo ndipo ndimadziona kuti ndine wachabechabe. Ndiye ndimadziuza kuti si ine woyenera kuti Mulungu azimvetsera mapemphero anga.”

Mayi ali mutchalitchi ndipo akupemphera akuyang’ana kumwamba pomwe anthu ena akupemphera atazyolika.

Kodi inuyo mumaona bwanji nkhani ya kupemphera? Ngati inunso munaganizapo mofanana ndi anthuwa zokhudza pemphero, mungasangalale kudziwa kuti Baibulo limapereka mayankho othandiza pa nkhaniyi. Baibulo limafotokoza mfundo zodalirika zokhudza pempheroa ndipo lingakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso monga awa:

  • Kodi Mulungu amamvadi mapemphero athu?

  • N’chifukwa chiyani mapemphero ena sayankhidwa?

  • Kodi mungatani kuti Mulungu azimva mapemphero anu?

  • Kodi kupemphera kungakuthandizeni bwanji?

a M’Baibulo muli mapemphero a atumiki ambiri a Mulungu, kuphatikizapo a Yesu Khristu. M’Malemba Achiheberi, omwe anthu ambiri amati Chipangano Chakale, muli mapemphero oposa 150.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena