Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp21 No. 1 tsamba 14-15
  • Kodi Kupemphera Kungakuthandizeni Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kupemphera Kungakuthandizeni Bwanji?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kupemphera N’kothandiza Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
wp21 No. 1 tsamba 14-15

Kodi Kupemphera Kungakuthandizeni Bwanji?

Munthu wina dzina lake Pamela anadwala kwambiri ndipo anapita kuchipatala. Koma anapempheranso kwa Mulungu kuti amupatse mphamvu yomuthandiza kupirira vutoli. Kodi kupempherako kunamuthandiza?

Pamela anapezeka ndi khansa ndipo anati: “Nthawi zambiri ndinkachita mantha ndikamalandira mankhwala a khansa. Koma ndikapemphera kwa Yehova Mulungu mtima unkakhala m’malo ndipo ndinkatha kuganiza bwino. Ndimavutikabe ndi ululu koma pemphero limandithandiza kuona zinthu moyenera. Anthu akandifunsa kuti, ‘Muli bwanji?’ ndimayankha kuti, ‘Sindikupeza bwino koma ndikusangalala.’”

Koma sitiyenera kudikira mpaka titakumana ndi vuto lalikulu kuti tipemphere. Tonsefe timakumana ndi mavuto, kaya aakulu kapena aang’ono, ndipo timafunika kuthandizidwa kuti tilimbane ndi mavutowo. Koma kodi kupemphera kungathandizedi?

Baibulo limanena kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” (Salimo 55:22) Lembali ndi lolimbikitsa kwambiri. Koma kodi kupemphera kungakuthandizeni bwanji? Mukamapemphera kwa Mulungu m’njira yovomerezeka, iye adzakupatsani zinthu zimene zingakuthandizeni kulimbana ndi mavuto anu.​—Onani bokosi lakuti “Zimene Mungapeze Chifukwa Chopemphera.”

Zimene Mungapeze Chifukwa Chopemphera

Mtendere wamumtima

Bambo yemwe poyamba ntchito inamuthera akumwetulira ndipo akuyenda mosangalala.

“Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Mukamafotokozera Mulungu nkhawa zanu iye adzakuthandizani kuti mtima wanu ukhale m’malo komanso kuti muzichita zinthu mwanzeru mukakumana ndi mavuto.

Nzeru yochokera kwa Mulungu

Mayi yemwe poyamba ankangowerenga mapemphero kuchokera m’buku, akuwerenga Baibulo kunyumba kwake.

“Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” (Yakobo 1:5) Nthawi zina sitisankha zinthu mwanzeru tikapanikizika. Koma tikamapemphera kuti Mulungu atipatse nzeru, angatikumbutse mfundo zambiri zothandiza zopezeka m’Mawu ake Baibulo.

Mphamvu komanso chilimbikitso

Banja lomwe poyamba linali m’chipatala, lili limodzi kupaki. Mwamuna akuthandiza mwachikondi mkazi wake kuti ayendere ndodo.

“Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Popeza Yehova ndi Mulungu wamphamvuyonse, angakupatseni mphamvu zimene mumafunika kuti mulimbane ndi mavuto anu kapena kuwapirira. (Yesaya 40:29) Baibulo limatchulanso Yehova kuti ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” Iye angatilimbikitse “m’masautso athu onse.”​—2 Akorinto 1:3, 4.

KODI KUPEMPHERA KUNGAKUTHANDIZENI INUYO?

Yehova sangakukakamizeni kuti muzipemphera kwa iye. Koma akukupemphani mwachikondi kuti muzipemphera. (Yeremiya 29:11, 12) Koma kodi mungatani ngati mwaona kuti mapemphero anu sanayankhidwe? Musataye mtima kapena kugwa ulesi. Makolo achikondi mwina sangathandize ana awo m’njira kapena pa nthawi imene anawo akuyembekezera. N’kutheka kuti makolowo amadziwa njira yabwino yowathandizira kuposa imene anawo akuganizira. Koma chimene timadziwa n’chakuti makolo achikondi sangalephere kuthandiza ana awo.

Yehova, yemwe ndi Atate wachikondi kwambiri, amafuna kukuthandizani. Mukamaganizira mfundo zimene takambirana komanso kuyesetsa kuzitsatira, Mulungu adzayankha mapemphero anu m’njira yabwino kwambiri.​—Salimo 34:15; Mateyu 7:7-11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena