Mawu Oyamba
Kodi zinthu zimene zikuchitika padzikoli zikusonyeza kuti dziko latsala pang’ono kutha? Ngati ndi choncho tingatani kuti tidzapulumuke mapeto a dzikoli? Nanga chidzachitike n’chiyani dzikoli likadzatha? Nkhani za m’magaziniyi zitithandiza kudziwa mayankho otonthoza ochokera m’Baibulo a mafunso amenewa.