Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w21 June tsamba 26-30
  • Ndimadalira Yehova Posankha Zochita

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndimadalira Yehova Posankha Zochita
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NTCHITO YOLALIKIRA KU LEBANON
  • KUSAMUKIRA KUDZIKO LINA
  • TINAKUMANA NDI VUTO LALIKULU
  • KUSANKHA KUCHITA ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI
  • KUSINTHA KWINA KWAKUKULU
  • TINALANDIRA MPHATSO MWADZIDZIDZI
  • BANJA LATHU LINASAMUKA
  • NDIKANASANKHANSO ZOMWEZI
  • Kukhala Moyandikira ku Gulu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kuyamikira Choloŵa Cholimba Chachikristu
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kuunika Kwauzimu Kukuwala ku Middle East
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Ndagwira Chovala cha Myuda kwa Zaka Zoposa 70
    Nsanja ya Olonda—2012
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
w21 June tsamba 26-30

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndimadalira Yehova Posankha Zochita

YOFOTOKOZEDWA NDI DYAH YAZBEK

Dyah Yazbek ali wamng’ono.

TSIKU lina m’mawa mu 1984, ndinkachoka kunyumba kupita kuntchito. Nyumba yathu inali m’dera lina lomwe kunkakhala anthu olemera, ku Caracas m’dziko la Venezuela. Ndili m’njira, ndinkaganizira nkhani ina yomwe inali itatuluka mu Nsanja ya Olonda. Nkhani yake inali yokhudza mmene anthu ena amationera. Nditayang’ana nyumba za anthu oyandikana nawo, ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi anthuwa amangondiona kuti ndine munthu wogwira ntchito kubanki, yemwe zinthu zikumuyendera? Kapena kodi amandiona kuti ndine mtumiki wa Mulungu amene amagwira ntchito kubanki n’cholinga choti azisamalira banja lake?’ Posasangalala ndi zimene ndinkaona kuti ndiye yankho pa funsoli, ndinaganiza zosintha zinthu pa moyo wanga.

Ndinabadwa pa 19 May 1940, m’tawuni ya Amioûn ku Lebanon. Patapita zaka zochepa banja lathu linasamukira mumzinda wa Tripoli. Ndinakulira m’banja losangalala, lomwe anthu ake ankadziwa komanso kukonda Yehova Mulungu. M’banja lathu, tinalipo ana 5, atsikana atatu ndi anyamata awiri ndipo ine ndi womaliza. Makolo anga sankaona kuti kupeza ndalama ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo. Zinthu zomwe tinkaona kuti n’zofunika kwambiri zinali kuphunzira Baibulo, kupita kumisonkhano ya Chikhristu komanso kuthandiza anthu ena kuti adziwe Mulungu.

Mumpingo wathu munali Akhristu odzozedwa angapo. Mmodzi wa iwo anali M’bale Michel Aboud, yemwe ankachititsa msonkhano womwe pa nthawiyo unkadziwika kuti phunziro la buku. Iyeyu anaphunzira choonadi ku New York ndipo ndi amene anachibweretsa ku Lebanon, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1920. Ndimakumbukira mmene ankalemekezera komanso kuthandiza Anne ndi Gwen Beavor, alongo awiri omwe anali atalowa Sukulu ya Giliyadi. Alongo amenewa anakhala anzathu abwino kwambiri. Patapita zaka zambiri ndinasangalala kukumana ndi Anne ku United States. Kenako, ndinadzakumana ndi Gwen, yemwe anakwatiwa ndi Wilfred Gooch ndipo ankatumikira ku Beteli ya ku London ku England.

NTCHITO YOLALIKIRA KU LEBANON

Ndili mnyamata, ku Lebanon kunali a Mboni ochepa. Koma tinkachita khama kuphunzitsa ena zimene tinkaphunzira m’Baibulo. Tinkachita zimenezi ngakhale kuti atsogoleri ena achipembedzo ankatitsutsa. Ndipo pali zochitika zina zomwe sindimaziiwala.

Tsiku lina, ine ndi mlongo wanga Sana tinkalalikira uthenga wa m’Baibulo m’nyumba ina yosanjikizana. Tikulalikira pakhomo lina, panabwera wansembe. Munthu wina ayenera kuti ndi amene anamuitana. Wansembeyo anayamba kunyoza mlongo wanga. Iye anayamba zachiwawa ndipo anamukankha Sana pamasitepe moti anavulala. Ndiyeno munthu wina anaimbira foni apolisi, ndipo atabwera anaonetsetsa kuti Sana walandira thandizo loyenera. Iwo anatengera wansembeyo kupolisi komwe anamupeza kuti anali ndi mfuti. Mkulu wa apolisi anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani makamaka? Mtsogoleri wachipembedzo, kapena mtsogoleri wa gulu lazachiwawa?”

Ndimakumbukiranso zimene zinachitika nthawi ina, pamene mpingo wathu unachita hayala basi, n’kupita kukalalikira uthenga wabwino kutawuni ina yakutali. Zonse zinkayenda bwino mpaka pamene wansembe wina wa kumaloko anamva n’kusonkhanitsa anthu kuti atiukire. Iwo ankatinyoza mpaka anafika potigenda moti bambo anga anavulala kwambiri. Nkhope yonse ili magazi okhaokha, iwo anabwerera ndi mayi anga komwe tinaimika basi ija, ndipo ena tonsefe tili ndi nkhawa tinawatsatira. Komabe sindidzaiwala zimene amayi ananena pamene ankawapukuta bambo. Iwo anati: “Yehova, akhululukireni chifukwa sakudziwa chimene akuchita.”

Nthawi ina tinapita kukaona achibale m’tawuni yakwathu. Kumeneko tinakumana ndi bishopu wina wotchuka yemwe ankacheza ndi agogo anga a amuna. Iye ankadziwa kuti makolo anga ndi a Mboni za Yehova. Ngakhale kuti ndinali ndi zaka 6 zokha, bishopuyo anasankha kundifunsa ineyo kuti, “Iwe, n’chifukwa chiyani sunabatizidwe?” Ndinayankha kuti ndine mwana ndipo kuti ndibatizidwe ndiyenera kudziwa kaye zambiri zokhudza Baibulo n’kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Chifukwa chosasangalala ndi zomwe ndinayankhazi, iye anauza agogo angawo kuti ndine wamwano.

Komabe, zinthu ngati zimenezi sizinkachitika kawirikawiri. Tikutero chifukwa anthu ambiri ku Lebanon ndi ansangala komanso amalandira bwino alendo. Choncho tinkasangalala kukambirana ndi anthu nkhani zopezeka m’Mawu a Mulungu komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri.

KUSAMUKIRA KUDZIKO LINA

Ndili pasukulu, m’bale wina wachinyamata wa ku Venezuela anabwera kudzacheza ku Lebanon. Iye ankasonkhana mumpingo wathu ndipo kenako anayamba kucheza kwambiri ndi mlongo wanga, dzina lake Wafa. Patapita nthawi anakwatirana ndipo anapita kukakhala ku Venezuela. M’makalata ake, Wafa ankakonda kulimbikitsa bambo anga kuti banja lathu lonse lisamukire ku Venezuela chifukwa choti ankatisowa kwambiri. Pamapeto pake zinatheka ndipo tinasamukadi.

Tinafika ku Venezuela mu 1953 ndipo tinkakhala mumzinda wa Caracas, womwe ndi likulu la dzikoli. Nyumba yathu inali pafupi ndi nyumba ya pulezidenti. Popeza ndinali wamng’ono, ndinkasangalala ndikamaona pulezidenti akudutsa pa galimoto yake yapamwamba. Komabe, sizinali zophweka kuti makolo anga azolowere zinthu zina monga chilankhulo, chikhalidwe, zakudya komanso nyengo m’dziko limeneli. Ndipo pamene ankati aziyamba kuzolowera moyo watsopanowu, panachitika chinthu china chosayembekezereka.

Kuchokera kumanzere kupita kumanja: Bambo anga. Mayi anga. Ineyo mu 1953, banja lathu litasamukira ku Venezuela

TINAKUMANA NDI VUTO LALIKULU

Bambo anga anayamba kudwala kwambiri. Zimenezi zinatidabwitsa chifukwa iwo anali a mphamvu komanso a thanzi. Sitinkakumbukira n’komwe nthawi imene anadwalapo. Anawapeza ndi khansa ya mukapamba ndipo kenako anawachita opaleshoni. N’zomvetsa chisoni kuti patangotha mlungu umodzi anamwalira.

N’zovuta kufotokoza mmene tinamvera pa nthawiyo poganizira mmene zinthu zinalili. Ndinali ndi zaka 13 zokha. Tinakhumudwa kwambiri moti tinkaona ngati sizingatheke kudzakhalanso osangalala. Kwa kanthawi, amayi zinkawavuta kuvomereza kuti amuna awo kunalibenso. Komabe tinaona kuti tiyenera kupirira ndipo Yehova anatithandiza kuti tikwanitse. Ndili ndi zaka 16, ndinamaliza maphunziro anga a kusekondale ndipo ndinkafunitsitsa kuthandiza banja lathu.

Mlongo wanga Sana ndi mwamuna wake Rubén anandithandiza kuti ndizikonda kwambiri Yehova

Pa nthawiyo, mlongo wanga Sana anakwatiwa ndi Rubén Araujo, yemwe anali atamaliza maphunziro a Sukulu ya Giliyadi ndipo anabwerera ku Venezuela. Iwo anasankha kusamukira ku New York. Banja lathu litagwirizana kuti ndichite maphunziro a kuyunivesite, ndinapita ku New York kumakakhala nawo limodzi. Mlongo wanga ndi mwamuna wake anandithandiza kwambiri kuti ndikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Kuwonjezera pamenepo, mumpingo umene tinkasonkhana womwe unali wa Chisipanishi ku Brooklyn, munali abale okonda Yehova. Awiri mwa abalewa, omwe ndinasangalala kudziwana nawo, anali M’bale Milton Henschel komanso M’bale Fredrick Franz ndipo ankatumikira pa Beteli ya ku Brooklyn.

Pa ubatizo wanga mu 1957

Nditatsala pang’ono kumaliza chaka choyamba kuyunivesite, ndinayamba kudzifunsa zimene ndinkachita ndi moyo wanga. Ndinali nditawerenga komanso kuganizira mozama nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda, zofotokoza za Akhristu omwe anakhala ndi zolinga zotumikira Yehova. Ndinkaonanso mmene apainiya komanso atumiki a pa Beteli a mumpingo wathu ankasangalalira ndipo ndinkafuna kukhala ngati iwowo. Koma ndinali ndisanabatizidwe. Pasanapite nthawi, ndinazindikira kufunika koti ndidzipereke kwa Yehova. Choncho ndinadzipereka ndipo kenako ndinabatizidwa pa 30 March 1957.

KUSANKHA KUCHITA ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI

Nditabatizidwa, ndinayamba kuganiza zochita upainiya. Ndinkalakalaka kwambiri nditachita zimenezi koma ndinkadziwa kuti sizikhala zophweka. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikwanitsa bwanji kuchita upainiya kwinaku ndikuchita maphunziro a kuyunivesite?’ Ndinkalemberana makalata pafupipafupi ndi amayi komanso azibale anga omwe anali ku Venezuela, kuwafotokozera zimene ndinasankha zofuna kusiya maphunziro a kuyunivesite n’kubwerera kuti ndikachite upainiya.

Ndinabwerera ku Caracas mu June 1957. Komabe ndinaona kuti banja lathu linkavutika kupeza zofunika pa moyo. Pankafunika kuti munthu wina azigwira ntchito. Choncho pofuna kuwathandiza ndinayamba kugwira ntchito kubanki koma ndinkafunitsitsabe nditachita upainiya. Ndipotu paja chimenechi ndi chifukwa chomwe ndinabwererera kwathu ku Venezuela. Choncho ndinasankha kuti ndizichita zonse ziwiri. Kwa zaka zingapo ndinkagwira ntchito kubanki kwinaku ndikuchita upainiya. Ndinkatanganidwa kwambiri koma ndinkakhalanso wosangalala kwambiri.

Chimwemwe changa chinawonjezekanso nditakumana ndi Sylvia, mlongo wokongola wa ku Germany, yemwe amakonda kwambiri Yehova ndipo tinakwatirana. Iye anali atasamukira ku Venezuela kuno ndi makolo ake. Patapita nthawi, tinakhala ndi ana awiri, Michel (Mike) ndi mchemwali wake Samira. Ndinayambanso kusamalira mayi anga, omwe anabwera kudzakhala nafe limodzi. Ngakhale kuti ndinasiya upainiya kuti ndizisamalira banja langa, ndinkapitirizabe kulalikira mwakhama. Ndipo ine ndi Sylvia tinkachita upainiya wothandiza pa nthawi iliyonse imene tinali patchuthi.

KUSINTHA KWINA KWAKUKULU

Pa nthawi yomwe ndinkaganiza zomwe ndafotokoza koyambirira kuja, ana athu anali adakali pasukulu. Kunena zoona, pa nthawiyo ndinkakhala moyo wofewa ndipo anthu omwe ndinkagwira nawo ntchito kubanki ankandilemekeza kwambiri. Komabe, ndinkafunitsitsa kuti anthu azindiona ngati mtumiki wa Yehova ndiye ndinapitiriza kuganizira zomwe ndingachite kuti zimenezi zitheke. Choncho, ine ndi mkazi wanga tinakhala pansi n’kukambirana kuti tione ndalama zimene tinali nazo. Ngati ndikanasiya ntchito kubanki, ndikanalandira ndalama zambiri. Popeza kuti tinalibe ngongole iliyonse, tinaona kuti tikamakhala moyo wosalira zambiri, tikhoza kukhala ndi ndalama zokwanira kugwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali.

Sizinali zophweka kuti ndisiye ntchito koma mkazi wanga wokondedwa limodzi ndi mayi anga anandithandiza kwambiri. Choncho zinatheka kuti ndiyambirenso utumiki wa nthawi zonse ndipo ndinasangalala kwambiri. Chilichonse chinkaoneka kuti chinali m’malomwake. Koma pasanapite nthawi panachitikanso zinthu zina zosayembekezereka.

TINALANDIRA MPHATSO MWADZIDZIDZI

Dyah ndi Sylvia ali ndi mwana wawo wobadwa kumene Gabriel.

Mwana wathu wachitatu Gabriel anali mphatso yadzidzidzi

Tsiku lina dokotala anatiuza kuti Sylvia anali woyembekezera. Zimenezi zinatidabwitsa tonse. Inali nkhani yosangalatsa kwambiri komabe ndinkaganizira mmene zikanakhudzira zomwe ndinasankha zoti ndiyambe upainiya. Posakhalitsa tinakhazikitsa maganizo m’malo ndipo tinayamba kuyembekezera kukhala ndi mwana wina. Koma ndinkadzifunsabe ngati ndingakwaniritse cholinga changa chija.

Titakambirana tinagwirizana kuti ndiyambebe kuchita upainiya. Mwana wathu Gabriel anabadwa mu April 1985. Komabe ndinasiya ntchito kubanki kuja ndipo ndinayamba upainiya wokhazikika mu June chaka chomwecho. Patapita nthawi, ndinayamba kutumikira m’Komiti ya Nthambi. Ofesi ya nthambi sinali ku Caracas choncho ndinkafunika kumayendera kwa masiku awiri kapena atatu pa mlungu ndipo unali mtunda wa makilomita 80.

BANJA LATHU LINASAMUKA

Ofesi ya nthambi inali m’tawuni ya La Victoria choncho tinaganiza zosamukira m’tawuniyi kuti tikakhale pafupi ndi ku Beteli. Kumeneku kunali kusintha kwakukulu. Ndimayamikira anthu a m’banja langa chifukwa cha mtima wawo wokonzeka kusintha zinthu ndipo zimenezi zinandithandiza kwambiri. Mchemwali wanga Baha anadzipereka kuti azisamalira mayi athu. Mwana wathu Mike anali atakwatira ndipo Samira ndi Gabriel tinali tikukhalabe nawo limodzi. Choncho kusamukaku kunachititsa kuti asiyane ndi anzawo a ku Caracas. Komanso mkazi wanga wokondedwa, Sylvia ankafunika kuzolowera kukhala m’tawuni yaing’ono. Ndipo tonsefe tinkafunikanso kuzolowera kukhala m’nyumba yaing’ono. Kunena zoona tinkafunikadi kusintha zambiri kuti tisamuke kuchoka ku Caracas kupita ku La Victoria.

Koma zinthu zinasinthanso. Mwana wathu Gabriel anakwatira ndipo Samira anayamba kukhala payekha. Ndiye mu 2007, ine ndi Sylvia tinaitanidwa kuti tizikakhala ku Beteli, komwe tikutumikirabe mpaka pano. Panopa, mwana wathu woyamba Mike ndi mkulu ndipo akuchita upainiya limodzi ndi mkazi wake Monica. Nayenso Gabriel ndi mkulu ndipo limodzi ndi mkazi wake Ambra, amakhala ku Italy. Samira akuchita upainiya komanso amathandiza ntchito za pa Beteli ali kunyumba.

Kuchokera kumanzere kupita kumanja: Ndili ndi mkazi wanga Sylvia ku nthambi ya ku Venezuela. Mwana wathu wamkulu Mike ndi mkazi wake Monica. Mwana wathu wamkazi Samira. Gabriel ndi mkazi wake Ambra

NDIKANASANKHANSO ZOMWEZI

Kunena zoona, pa moyo wanga ndakhala ndikusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Koma sindimanong’oneza bondo moti ndikanapatsidwa mwayi wina woti ndisankhenso zochita, ndikanasankhabe zomwezi. Ndimayamikira kwambiri chifukwa cha zonse zimene ndakwanitsa kuchita potumikira Yehova. Pa zaka zimenezi, ndaona kuti chofunika kwambiri ndi kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Kaya tikufunika kusankha zochita pa nkhani zazikulu kapena zazing’ono, iye angatipatse mtendere “umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afil. 4:6, 7) Panopa, ine ndi Sylvia tikusangalala kutumikira pa Beteli ndipo timaona kuti Yehova wakhala akudalitsa zosankha zathu chifukwa choti timamudalira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena