Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w21 October tsamba 29-31
  • 1921​—Zomwe Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1921​—Zomwe Zinachitika Zaka 100 Zapitazo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ALALIKI OLIMBA MTIMA
  • PHUNZIRO LAUMWINI KOMANSO PHUNZIRO LA BANJA
  • BUKU LATSOPANO
  • ANKAYEMBEKEZERA NTCHITO YAMBIRI
  • Timadalitsidwa Tikamachita Zimene Yehova Amatiuza
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • 1922​—Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Zosankha Zimene Zimabweretsa Chisangalalo
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Chuma Chomwe Chakhala ku Banja Lathu kwa Mibadwo 7
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
w21 October tsamba 29-31

1921 Zomwe Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

“KODI ndi ntchito yofunika iti imene mukuona kuti tikufunika tiigwire mofulumira m’chakachi?” Limeneli ndi funso limene linali mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1921, lopita kwa Ophunzira Baibulo akhama pa nthawiyo. Poyankha funsoli, nsanjayo inatchula mawu a pa Yesaya 61:1, 2, omwe anawakumbutsa ntchito yolalikira yomwe anapatsidwa. Lembali limati: “Yehova wandidzoza kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa . . . , wandituma kuti ndikalengeze za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima, ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu.”

ALALIKI OLIMBA MTIMA

Ophunzira Baibulowa ankafunika kukhala olimba mtima kuti akwanitse kugwira ntchito yolalikira yomwe anapatsidwayi. Iwo ankafunika kulengeza “uthenga wabwino” kwa ofatsa, komanso kulengeza za “tsiku lobwezera” kwa anthu oipa.

M’bale J.  H.  Hoskin, yemwe ankakhala ku Canada, ankalalikira mopanda mantha ngakhale kuti ankatsutsidwa. Cha kumayambiriro kwa chaka cha 1921, iye anakumana ndi m’busa wa Tchalitchi cha Methodist. M’bale Hoskin anayamba kukambirana naye pomuuza kuti: “Ndikufuna kuti tikambirane mwamtendere zokhudza Baibulo. Ndipo ngakhale zitakhala kuti sitikugwirizana pa zinthu zina, timalize kukambiranaku bwinobwino ndipo tipitirize kukhala mabwenzi.” Koma izi si zomwe zinachitika. M’bale Hoskin anati: “Tinangokambirana kwa maminitsi ochepa ndipo m’busayo analowa m’nyumba ndi kumenyetsa chitseko mwamphamvu moti ndinkangoona ngati galasi lalikulu la pachitsekopo ligwa n’kusweka.”

M’busayo anakalipa kuti: “Bwanji osapita kumakalalikira anthu omwe si Akhristu?” M’bale Hoskin sanayankhe chilichonse koma pamene ankachoka pakhomopo cha mumtima anangoti, ‘Ndimaona ngatitu amene ndikuyankhula nayeyu si Mkhristu.’

Pamene m’busayo ankalalikira m’tchalitchi chake tsiku lotsatira, ananena zinthu zambiri zabodza zokhudza M’bale Hoskin. M’baleyu ananena kuti, “M’busayo anachenjeza anthu a m’chipembedzo chakewo powauza kuti ndinali munthu wabodza kwambiri m’tawuni yonseyo ndipo ndinkangofunika kuwomberedwa basi.” Koma zimenezi sizinamufooketse ndipo anapitirizabe kulalikira kwa anthu ambiri. Iye anati: “Ndinkasangalala kwambiri kugwira ntchito yolalikira m’dera limeneli. Ena anafika pondiuza kuti, ‘Ndikudziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu.’ Ndipo ankandifunsa ngati angandithandize pa zinthu china kuti ndisamasowe chilichonse.”

PHUNZIRO LAUMWINI KOMANSO PHUNZIRO LA BANJA

Pofuna kuthandiza anthu kumvetsa Malemba, Ophunzira Baibulo ankaika njira zosiyanasiyana zophunzirira Baibulo m’magazini imene panopa imadziwika kuti Galamukani! Mwachitsanzo, m’magaziniyi munkakhala mafunso amene makolo ankayenera kukambirana ndi ana awo. Makolowo ankafunika “kuwafunsa mafunsowa n’kumawathandiza kuti afufuze mayankho ake m’Baibulo.” Mafunso ena monga lakuti, “Kodi m’Baibulo muli mabuku angati?” ankathandiza anawo kudziwa zinthu zina zosavuta zokhudza Baibulo. Pomwe mafunso ena monga lakuti, “Kodi Mkhristu woona aliyense aziyembekezera kuti adzazunzidwa?” ankawakonzekeretsa kuti azilalikira molimba mtima.

M’magaziniyi munkakhalanso mbali imene inkathandiza anthu amene amadziwa kale mfundo zina za m’Baibulo. Mbaliyi inkakhala ndi mafunso omuthandiza munthu kuganizira zimene akuphunzira ndipo mayankho ake ankachokera m’buku la Chingelezi lakuti Studies in the Scriptures. Anthu ambiri ankapindula ndi njira zophunzirira Baibulozi. Koma magazini ya December 21, 1921 inanena kuti njira zophunzirirazi zidzasiya kuikidwa m’magaziniyi. Chifukwa chiyani?

BUKU LATSOPANO

Buku lakuti Zeze wa Mulungu

Kakhadi komuuza wophunzira zimene ayenera kuwerenga

Kakhadi ka mafunso

Abale amene ankatsogolera anazindikira kuti anthu amene akuphunzira Baibulo ankafunika kumaphunzira mfundo zoyambirira za choonadi m’njira yotsatirika. Choncho buku lakuti Zeze wa Mulungu linatulutsidwa mu November 1921. Anthu amene asonyeza chidwi ankapatsidwa bukuli ndipo ankaligwiritsa ntchito pophunzira Baibulo paokha. Kuphunzira mwa njira imeneyi, kunkathandiza anthu kudziwa “cholinga cha Mulungu chomwe ndi kudzapereka moyo wosatha kwa anthu.” Koma kodi njira yophunzirirayi inkachitika bwanji?

Munthu amene walandira bukuli, ankapatsidwanso kakhadi komudziwitsa masamba amene ayenera kuwerenga mlungu umenewo. Mlungu wotsatira, ankapatsidwanso kakhadi kena kokhala ndi mafunso a zimene anawerengazo ndipo kumapeto kwa khadilo ankalembako masamba amene ayenera kuwerenga mlungu winawo.

Mlungu uliwonse kwa milungu 12, wophunzira ankalandira kakhadi kuchokera kumpingo umene anali nawo pafupi. Nthawi zambiri amene ankakapereka makhadiwa anali anthu amene pazifukwa zina sakanatha kulalikira khomo ndi khomo kapenanso achikulire. Mwachitsanzo, Anna K. Gardner wa ku Millvale, Pennsylvania, U.S.A., ananena kuti: “Buku la Zeze wa Mulungu litatulutsidwa mchemwali wanga Thayle, yemwe ankavutika kuyenda, anali ndi ntchito yotumiza timakhaditi kwa ophunzira mlungu uliwonse.” Munthu akamaliza kuphunzira bukuli, ankayenderedwa n’cholinga chofuna kumulimbikitsa kupitirizabe kuphunzira Baibulo.

Thayle Gardner ali panjinga ya olumala

ANKAYEMBEKEZERA NTCHITO YAMBIRI

Chakumapeto kwa chakacho, M’bale J. F. Rutherford anatumiza kalata kumipingo yonse. Iye anati, “M’chaka chimenechi ntchito yokolola yachitika kwambiri kuposa zaka zonse m’nyengo yokololayi.” Poganizira zakutsogolo iye anawonjezera kuti: “Koma pali ntchito yambiri yoti igwiridwe. Tiyeni tilimbikitse ena kuti agwire nawo ntchito yabwinoyi.” N’zosakayikitsa kuti Ophunzira Baibulo pa nthawiyo anatsatira malangizowa. M’chaka cha 1922, iwo anadzagwira ntchito yolengeza za Ufumu mopanda mantha kuposa kale.

Mabwenzi Olimba Mtima

Ophunzira Baibulo ankasonyezana chikondi chenicheni ndipo ankathandizana. Monga mmene tionere, iwo anali mabwenzi olimba mtima omwe ‘ankathandizana pakagwa mavuto.’​—Miy. 17:17.

Lachiwiri pa 31 May 1921, ku Tulsa mumzinda wa Oklahoma, U.S.A., kunachitika chipolowe munthu wina wakuda atamangidwa pa mlandu wochitira nkhanza mayi wina wachizungu. Gulu la amuna oposa 1,000 achizungu litayamba kumenyana ndi kagulu kochepa ka amuna achikuda, kumenyanako kunafalikira mofulumira m’dera lapafupi la Greenwood, komwe kunkakhala anthu akuda. Kumeneko nyumba zoposa 1,400 komanso mabizinezi zinawonongedwa ndiponso kuwotchedwa. Chiwerengero chotsimikizika cha anthu amene anaphedwa chinali 36, koma n’kutheka kuti chiwerengerochi chinapitirira kufika m’mahandiredi.

M’balel Richard J. Hill, Wophunzira Baibulo wachikuda yemwe ankakhala ku Greenwood, anafotokoza zimene zinachitika ndipo anati: “Usiku womwe kunayambika chipolowechi, tinali tikuphunzira Baibulo pamisonkhano monga mwa nthawi zonse. Titangomaliza misonkhanoyo tinayamba kumva kulira kwa mfuti mkati mwa tawuniyo. Kuwomberako kunapitirira mpaka mkati mwa usiku.” Mmene kumacha Lachitatu pa 1 June, zinthu zinali zitaipa kwambiri. M’bale Hill anapitiriza kuti: “Anthu ena anabwera kudzatiuza kuti ngati tikufuna kutetezeka tithawire ku holo ina ya boma yomwe inali m’tawuniyo.” Choncho M’bale Hill limodzi ndi mkazi ndi ana ake 5, anathawira kuholoko. Kumeneko kunali anthu achikuda pafupifupi 3,000 ndipo ankatetezedwa ndi asilikali omwe anatumizidwa ndi boma kuti akakhazikitse mtendere.

Panthawiyo M’bale Arthur Claus yemwe anali mzungu anachita zinthu molimba mtima. Iye anafotokoza kuti: “Nditamva kuti anthu omwe ankachita chiwawawo ali paliponse ku Greenwood, n’kumawononga komanso kuwotcha nyumba za anthu, ndinaganiza zopita kukaona M’bale Hill yemwe anali mnzanga.”

Arthur Claus ndi kalasi ya ana 14, omwe ankawaphunzitsa pogwiritsa ntchito buku la Zeze wa Mulungu

M’bale Arthur atafika kunyumba kwa M’bale Hill, anaona mzungu wina yemwe ankakhala pafupi ndi nyumbayo ali ndi mfuti m’manja. Mzunguyo yemwenso anali mnzake wa M’bale Hill ankaganiza kuti M’bale Arthur anali mmodzi wa anthu amene ankachita chiwawawo. Choncho anamufunsa mokalipa kuti: “Ukufuna chiyani kunyumba imeneyo?”

M’bale Arthur ananena kuti: “Ndikanapanda kumuyankha zomveka akanandiwombera. Koma ndinamutsimikizira kuti ndinali mnzake wa M’bale Hill komanso kuti nthawi zambiri ndinkapita kunyumbayo.” M’bale Arthur komanso munthu woyandikana naye nyumbayo anakwanitsa kuteteza nyumbayo kwa anthu achiwawawo.

Pasanapite nthawi yaitali, M’bale Arthur anadziwa kuti M’bale Hill ndi banja lake anali kuholo ya m’tawuniyo. Iye anauzidwa kuti sizikanatheka kuti munthu wakuda aliyense achoke kuholoyo popanda chilolezo cha mkulu wa asilikali omwe ankayang’anira malowo dzina lake Barrett. M’bale Arthur anati: “Zinali zovuta kwambiri kuti ndikumane ndi mkulu wa asilikaliyo. Nditamufotokozera zomwe ndinkafuna kuchita anandifunsa kuti: ‘Koma kodi ukakwanitsa kuteteza komanso kusamalira banjali?’ Ndi mtima wonse ndinavomera kuti inde.”

Atatenga pepala lachilolezo, M’bale Arthur anathamangira kuholo kuja. Atapereka pepalalo kwa msilikali yemwe anali kuholoko, msilikaliyo anadabwa kuti: “Mpaka abwana ndi amene asainira? Mukudziwa kuti ndinu woyamba kudzatenga anthu kuno lero?” Posakhalitsa M’bale Arthur ndi msilikaliyo anafufuza n’kupeza banja la M’bale Hill. Kenako M’bale Arthur anakweza banjali m’galimoto yake n’kumapita nawo kunyumba kwake.

“Monga anthu a Mulungu, timaonana kuti ndife ofanana”

M’bale Arthur anaonetsetsa kuti M’bale Hill ndi banja lake ndi otetezeka. Anthu ena anachita chidwi ndi zimene M’bale Arthur anachita polimba mtima komanso kusonyeza chikondi kwa abale ake. M’baleyu anati: “Mzungu amene ndinathandizana naye kuteteza katundu wa M’bale Hill uja anayamba kulemekeza kwambiri a Mboni za Yehova. Anthu enanso ambiri anayamba kuchita chidwi ndi uthenga wa Ufumu chifukwa anaona kuti sitisankhana mitundu ndipo monga anthu a Mulungu, timaonana kuti ndife ofanana.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena