Mawu Oyamba
Padziko lonse lapansi, anthu mamiliyoni ambiri amakhudzidwa ndi matenda ovutika maganizo. Anthu osiyanasiyana, ana ndi akulu omwe, akulimbana ndi matenda ovutika maganizo. Iwo akukumana ndi zimenezi posatengera kuti ndi olemera kapena osauka, maphunziro, chipembedzo, mtundu kapena chikhalidwe chawo. Kodi matenda ovutika maganizo ndi chiyani? Nanga amakhudza bwanji anthu? Magaziniyi ikufotokoza kufunika kopeza thandizo loyenerera la kuchipatala komanso ikufotokoza njira zosiyanasiyana za mmene Baibulo lingathandizire anthu amene akuvutika ndi matendawa.