Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp23 No. 1 tsamba 6-7
  • 1 | Pemphero​—‘Muzimutulira Nkhawa Zanu Zonse’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 | Pemphero​—‘Muzimutulira Nkhawa Zanu Zonse’
  • sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tanthauzo Lake
  • Mmene Mfundo Zimenezi Zingakuthandizireni
  • Muzimutulira Yehova Nkhawa Zanu Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • N’chiyani Chingandithandize Ndikakhala Ndi Nkhawa?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Tayani Nkhaŵa Yanu Yonse pa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Baibulo Lingathandize Amuna Amene Ali Ndi Nkhawa
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
wp23 No. 1 tsamba 6-7
Mnyamata ali ndi nkhawa ndipo akupemphera ataika dzanja lake pachifuwa.

1 | Pemphero ‘Muzimutulira Nkhawa Zanu Zonse’

BAIBULO LIMATI: ‘Muzimutulira [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 PETULO 5:7.

Tanthauzo Lake

Yehova Mulungu akukupemphani kuti muzimufotokozera mavuto ena aliwonse amene mukukumana nawo komanso zilizonse zomwe zikukudetsani nkhawa. (Salimo 55:22) Muzimufotokozera vuto lililonse lomwe mukukumana nalo kaya ndi lalikulu kapena laling’ono, chifukwa Yehova amationa kuti ndife ofunika. Choncho zilizonse zomwe zikutichitikira zimamukhudza. Ndiye kupemphera kwa iye, ndi njira yofunika kwambiri yokuthandizani kupeza mtendere wa m’maganizo.​—Afilipi 4:6, 7.

Mmene Mfundo Zimenezi Zingakuthandizireni

Tikamalimbana ndi matenda ovutika maganizo, tikhoza kumadzimva kuti tili tokhatokha. Si nthawi zonse pamene anthu ena angamvetse zomwe tikukumana nazo. (Miyambo 14:10) Koma tikamapemphera kwa Mulungu moona mtima, n’kumamuuza mmene tikumvera, nthawi zonse iye amatimvetsera mokoma mtima ndiponso amatimvetsa. Yehova amationa, amadziwa mmene zikutipwetekera komanso mmene tikuvutikira ndipo amafuna kuti tizimuuza m’pemphero chilichonse chomwe chikutidetsa nkhawa.​—2 Mbiri 6:29, 30.

Tikamapemphera kwa Yehova, timalimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti iye amasamala za ife. Tikhoza kumamva ngati mmene wamasalimo wina anamvera, pamene anapemphera kuti: “Mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwera.” (Salimo 31:7) Kungodziwa kokha mfundo yakuti Yehova amadziwa mavuto amene tikulimbana nawo, kungatithandize kuti tipitirizebe kupirira. Komabe sikuti iye amangoona mavuto athu basi, koma amachitapo kanthu. Kuposa wina aliyense, iye amadziwa bwino mavuto amene tikukumana nawo komanso amatitonthoza ndi kutilimbikitsa kudzera m’Baibulo.

Mmene Baibulo Likumuthandizira Julian

Mmene Vuto la Nkhawa Limandikhudzira

Julian.

“Ndimavutika ndi matenda enaake a mu ubongo (Obsessive Compulsive Disorder, OCD) amene amachititsa kuti ndizingoda nkhawa, ndiziganizira zinthu zoipa komanso ndizichita zinthu mobwerezabwereza. Vuto limeneli limandichitikira pa nthawi imene sindikuyembekezera. Pa nthawi ina ndimamva kuti ndili bwinobwino koma mwadzidzidzi, zinthu zimangopezeka kuti zasintha n’kuyamba kuda nkhawa kwambiri popanda chifukwa chilichonse. Nthawi zambiri nkhawa yanga imakula ndikakhala pagulu la anthu chifukwa ndimaganizira mmene akundionera.”

“Anzanga amene amadziwa za vuto langali amayesetsa kundithandiza. Koma ndinene zoona, zimene amanena nthawi zina, ndimaona kuti sizingandithandize. Koma ndimayamikira kwambiri zimene amayesetsa kuchita pondithandiza.”

“Matenda angawa, nthawi zina amandipangitsa kuti ndizilephera kupemphera. Zimanditengera nthawi yayitali kuti maganizo anga akhazikike kuti ndilankhule ndi Yehova m’pemphero. Ndimaganiza zinthu zambirimbiri pa nthawi imodzi zomwe zimandipangitsa kuti ndizibalalika. Ndikamalephera kudziletsa pa zimene ndikuganiza, zimakhala zondivuta kwambiri kuti ndimufotokozere Yehova zomwe ndikuganiza komanso mmene ndikumvera.”

Mmene Baibulo Limandithandizira

“Ndaphunzira kuchokera m’Baibulo kuti sizidalira kuti tikhale ndi luso lapadera kuti tilankhule ndi Mulungu kapena kupereka mapemphero aatali n’cholinga choti atiyankhe. Nthawi zina ndikalephera kufotokoza mmene ndikumvera, ndimangopemphera mwachidule kuti, ‘Yehova chonde ndithandizeni.’ Ndipo zikatero, ndimazindikira kuti Yehova akundimvetsa ndipo amandipatsa zimene zikufunikira pa nthawiyo. Kuwonjezera pa kupemphera, ndimapezanso thandizo lachipatala. Ndine wosangalala komanso ndikuyamikira kuti pemphero kuphatikizaponso thandizo lachipatala, zikundithandiza kuti ndiyambe kupezako bwino tsopano. Ngakhale kuti ndimafunika kuchita khama kwambiri kuti ndizipemphera kwa Atate wanga wakumwamba, ndimayesetsa kuchitabe zimenezi chifukwa ndimadziwa kuti iye amandikonda ndiponso ndi wofunitsitsa kundithandiza.”

Zimene Zingathandize Achinyamata

Vidiyo yakuti, “Khalani Bwenzi la Yehova​—Muzipemphera Nthawi Iliyonse.”

Phunzirani pawebusaiti ya jw.org/ny chifukwa chake mungakhale otsimikiza mtima kuti Yehova amamvetsera komanso kuyankha mapemphero anu.

Onerani vidiyo yakuti, Khalani Bwenzi la Yehova​—Muzipemphera Nthawi Iliyonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena