Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w23 October tsamba 32
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Tingapezere Zinthu Zimene Zasintha Kamvedwe
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Anasintha Zinthu Zina Zomwe Ankakhulupirira?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Mungaphunzirenso Izi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Buku Lothandiza Kufufuza Nkhani
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
w23 October tsamba 32

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Mmene Tingapezere Zinthu Zimene Zasintha Kamvedwe

Ndi mwayi waukulu kukhala pa nthawi imene mwapang’onopang’ono, Yehova akutithandiza kumvetsa mfundo za m’Baibulo kuposa kale. (Dan. 12:4) Ngakhale zili choncho, nthawi zina zikhoza kumativuta kudziwa mfundo za choonadi za m’Baibulo zimene zasintha. Kodi tingapeze kuti zinthu zimene zasintha komanso kafotokozedwe kake?

• Mu Watch Tower Publications Index pa mutu wakuti “Beliefs Clarified,” pali mndandanda wa zinthu zomwe zinasintha potengera chaka. Kuti mupeze mitu ya nkhani zimene zasintha, lembani “Understanding Clarified” (n’kuika m’mikodolero) pamalo ofufuzira pa Watchtower Library kapena pa LAIBULALE YA PA INTANETI.

• Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani lili ndi mndandanda wochepa potsatira mitu ya nkhani. Pitani pa mutu wakuti “Mboni za Yehova” kenako “Zikhulupiriro za Akhristu Komanso Mmene Amaonera Nkhani Zosiyanasiyana” ndipo kenako pitani pa kamutu kakuti “Kumveketsa Zikhulupiriro Zathu.”

Pophunzira panokha, mukhoza kusankha nkhani yomwe yasintha kamvedwe posachedwapa n’kufufuza kamvedwe katsopano komanso mfundo za m’Malemba zomwe zachititsa kuti tisinthe.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena