ZOTI NDIPHUNZIRE
Anthu Okhulupirika kwa Yehova Amakwaniritsa Zimene Alonjeza
Werengani Oweruza 11:30-40 kuti muone zimene mukuphunzira kwa Yefita ndi mwana wake wamkazi pa nkhani yokwaniritsa malonjezo.
Ganizirani nkhani yonse. Kodi Aisiraeli okhulupirika ankaona bwanji zimene amulonjeza Yehova? (Num. 30:2) Kodi Yefita ndi mwana wake wamkazi anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Yehova?—Ower. 11:9-11, 19-24, 36.
Fufuzani mozama. Kodi Yefita analonjeza chiyani nanga ankatanthauza chiyani? (w16.04 7 ¶12) Kodi Yefita ndi mwana wake anadzimana zinthu ziti kuti akwaniritse zimene analonjeza? (w16.04 7-8 ¶14-16) Kodi ndi zinthu ziti zimene Akhristu angalonjeze masiku ano?—w17.04 5-8 ¶10-19.
Onani zimene mukuphunzirapo. Dzifunseni kuti:
‘N’chiyani chingandithandize kukwaniritsa lonjezo lomwe ndinachita podzipereka kwa Yehova?’ (w20.03 13 ¶20)
‘Kodi ndingadzimane zinthu ziti kuti ndizichita zambiri potumikira Yehova?’
‘Kodi ndingatani kuti ndizikwaniritsa zimene ndinalonjeza mwamuna kapena mkazi wanga pamene tinkakwatirana?’ (Mat. 19:5, 6; Aef. 5:28-33)