Kodi Munayamba Mwadzifunsapo Mafunso Otsatirawa?
Popeza kuti aliyense amafuna mtendere, n’chifukwa chiyani padzikoli pakuchitika nkhondo?
Kodi n’zotheka kukhala mwamtendere m’dziko limene mukuchitika zachiwawa?
Kodi padzakhala nthawi imene sikudzakhalanso nkhondo?
Mukhoza kudabwa ndi mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa ndipo mosakayikira mayankhowo angakulimbikitseni kwambiri.
Mungachitenso bwino kufufuza nokha zimene Baibulo limanena pa nkhani yofunika kwambiriyi. Kuti mudziwe zambiri, werengani magazini ya Nsanja ya Olonda ino.