Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 February tsamba 32
  • Kukhala Olimba Mtima Ena Akamatitsutsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala Olimba Mtima Ena Akamatitsutsa
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Nkhani Yofanana
  • Amapereka Mphoto kwa Onse Omwe Amamutumikira
    Nsanja ya Olonda—2012
  • “Sindingathe Kukhala Chete”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Kodi Mumasankha Anthu Otani Kuti Akhale Anzanu?
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • “Ndidzatsitsimutsa Wolefuka”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 February tsamba 32

ZOTI NDIPHUNZIRE

Kukhala Olimba Mtima Ena Akamatitsutsa

Werengani Yeremiya 38:1-13 kuti muone zimene mungaphunzire kwa mneneri Yeremiya ndi Ebedi-meleki pa nkhani ya kulimba mtima.

Ganizirani nkhani yonse. Kodi Yeremiya anasonyeza bwanji kulimba mtima polengeza uthenga wa Yehova? (Yer. 27:12-14; 28:15-17; 37:6-10) Kodi anthu atamva uthengawo anachita chiyani?—Yer. 37:15, 16.

Fufuzani mozama. Kodi anthu ankafuna kuti Yeremiya achite chiyani? (jr 26-27 ¶20-22) Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza zitsime zakale. (it-1 471) Kodi mukuganiza kuti Yeremiya anamva bwanji pamene anali m’chitsime chamatope? Kodi Ebedi-meleki ayenera kuti ankachita mantha ndi chiyani?—w12 5/1 31 ¶2-3.

Onani zimene mukuphunzirapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsa chiyani ponena za mmene Yehova amatetezera atumiki ake okhulupirika?’ (Sal. 97:10; Yer. 39:15-18)

  • ‘Kodi ndi pa nthawi iti pomwe ndingafunike kusonyeza kulimba mtima?’

  • ‘Kodi ndingatani kuti ndizilimba mtima n’kuchita zoyenera ndikamatsutsidwa?’ (w11 3/1 30)a

a Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mmene mungamaphunzirire, onani “Mfundo Zothandiza Pophunzira” mu Nsanja ya Olonda yophunzira ya July 2023.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena