NKHANI YOPHUNZIRA 10
NYIMBO NA. 31 Muziyenda Ndi Mulungu
Tizitsanzira Mmene Yehova ndi Yesu Amaganizira
“Popeza Khristu anavutika pa nthawi imene anali munthu, nanunso konzekerani pokhala ndi maganizo ofanana ndi amene Khristu anali nawo.”—1 PET. 4:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona mmene Petulo anaphunzirira kukhala ndi maganizo ngati a Yesu komanso zimene ifeyo tiyenera kuchita.
1-2. Kodi kukonda Yehova kumaphatikizapo chiyani, nanga Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda Yehova ndi mtima wake wonse?
“MUZIKONDA Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.” (Luka 10:27) Apa Yesu anasonyeza kuti limeneli linali lamulo lofunika kwambiri m’Chilamulo cha Mose. Onani kuti kukonda Yehova kumaphatikizapo mtima wathu, womwe ukuimira zimene timakonda, mmene timamvera komanso mmene timaganizira. Kumaphatikizaponso kudzipereka kwa Yehova ndi mtima wathu wonse komanso mphamvu zathu zonse. Komabe kukonda Yehova kumaphatikizaponso maganizo athu, omwe akuimira mmene timaonera nkhani zosiyanasiyana. N’zoona kuti sitingamvetse mokwanira mmene Yehova amaganizira. Komabe tingathe kumvetsa mmene Mulungu amaganizira pophunzira “maganizo a Khristu,” chifukwa Yesu amatsanzira ndendende mmene Atate wake amaganizira.—1 Akor. 2:16.
2 Yesu ankakonda Atate wake ndi mtima wonse. Iye ankadziwa zimene Mulungu ankafuna kuti achite ndipo anali wokonzeka kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo ngakhale kuti zikanachititsa kuti akumane ndi mavuto. Popeza kuti ankaganizira kwambiri zosangalatsa Atate wake, Yesu sanalole kuti chilichonse chimulepheretse kukwaniritsa cholinga chakechi.
3. Kodi mtumwi Petulo anaphunzira chiyani kwa Yesu, nanga analimbikitsa Akhristu anzake kuchita chiyani? (1 Petulo 4:1)
3 Petulo ndi atumwi anzake anali ndi mwayi wokhala ndi Yesu ndipo anaphunzira mmene Yesuyo ankaganizira. Pamene Petulo ankalemba kalata yake yoyamba youziridwa analimbikitsa Akhristu kuti adzikonzekeretse pokhala ndi maganizo amene Khristu anali nawo. (Werengani 1 Petulo 4:1.) Pamene Petulo ananena kuti nanunso “konzekerani,” anagwiritsa ntchito mawu omwe m’chilankhulo choyambirira amafotokoza za msilikali yemwe wanyamula zida zake pokonzekera nkhondo. Choncho Akhristu akamatsanzira mmene Yesu amaganizira, amakhala kuti atenga chida champhamvu chomwe chingawathandize kulimbana ndi uchimo komanso dziko lolamulidwa ndi Satanali.—2 Akor. 10:3-5; Aef. 6:12.
4. Kodi nkhaniyi itithandiza bwanji kuti tizitsatira malangizo amene Petulo anapereka?
4 Munkhaniyi tikambirana mmene Yesu ankaganizira ndipo tiona mmene tingamutsanzirire. Tiona zimene tingachite kuti (1) tizitsanzira maganizo a Yehova, zomwe zingathandize kuti tonse tikhale ndi maganizo amodzi, (2) tikhale odzichepetsa, komanso (3) tiziganiza bwino n’kumadalira Yehova popemphera kwa iye.
TIZITSANZIRA MMENE YEHOVA AMAGANIZIRA
5. Kodi pa nthawi ina Petulo analephera bwanji kukhala ndi maganizo ngati a Yehova?
5 Taganizirani zimene zinachitika pa nthawi ina pamene Petulo analephera kukhala ndi maganizo a Yehova. Yesu anali atauza atumwi ake kuti akuyenera kupita ku Yerusalemu ndipo akaperekedwa m’manja mwa atsogoleri achipembedzo, akazunzidwa ndipo pamapeto pake akaphedwa. (Mat. 16:21) Ziyenera kuti zinamuvuta Petulo kukhulupirira kuti Yehova angalole kuti Yesu, yemwe anali chiyembekezo cha Isiraeli, komanso Mesiya wolonjezedwa, aphedwe. (Mat. 16:16) Choncho Petulo anamutengera Yesu pambali n’kumuuza kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” (Mat. 16:22) Popeza kuti Petulo sankaganiza ngati Yehova pa nkhaniyi, sanali ndi maganizo ofanana ndi a Yesu.
6. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankaganiza ngati mmene Yehova ankaganizira?
6 Maganizo a Yesu anali ogwirizana kwambiri ndi a Atate wake wakumwamba. Yesu anauza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.” (Mat. 16:23) N’kutheka kuti Petulo anali ndi zolinga zabwino, koma Yesu anakana kutsatira malangizo ake. Pamenepatu pali phunziro kwa ife. Sichinali cholinga cha Yehova kuti Yesu adzakhale ndi moyo popanda kukumana ndi mavuto alionse. Pa nthawiyi Petulo anaphunzira mfundo yofunika kwambiri yakuti ayenera kukhala ndi maganizo a Yehova.
7. Kodi Petulo anasonyeza bwanji kuti ankafuna kusintha kuti maganizo ake azigwirizana ndi a Yehova? (Onani chithunzi.)
7 Patapita nthawi, Petulo anasonyeza kuti ankafuna kuphunzira kuti aziganiza ngati mmene Yehova amaganizira. Nthawi ya Yehova inali itakwana yoti anthu a mitundu ina omwe anali osadulidwa akhale mbali ya anthu a Mulungu. Petulo anatumidwa kukalalikira kwa Koneliyo, yemwe anali munthu woyamba mwa anthu a mitundu ina kukhala Mkhristu. Ayuda sankayenderana ndi anthu a mitundu ina, choncho n’zosadabwitsa kuti Petulo anafunika kukonzekeretsedwa bwino kuti achite utumiki umene anapatsidwawu. Petulo atazindikira zimene Mulungu ankafuna pa nkhaniyi anasintha maganizo ake. Zotsatirapo zake n’zakuti, Koneliyo atamupempha kuti apite kunyumba kwake, Petulo anapita ‘mosanyinyirika.’ (Mac. 10:28, 29) Iye analalikira kwa Koneliyo ndi anthu a m’banja lake ndipo iwo anabatizidwa.—Mac 10:21-23, 34, 35, 44-48.
Petulo akulowa m’nyumba ya Koneliyo (Onani ndime 7)
8. Kodi tingasonyeze bwanji kuti maganizo athu akugwirizana ndi maganizo a Yehova? (1 Petulo 3:8 ndi mawu a m’munsi.)
8 Patapita zaka, Petulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti akhale “amaganizo amodzi.” (Werengani 1 Petulo 3:8, ndi mawu a m’munsi.) Monga anthu a Yehova, tingakhale ndi maganizo amodzi potsanzira maganizo a Yehova, omwe amafotokozedwa m’Mawu ake Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti aziika Ufumu pamalo oyamba. (Mat. 6:33) Poganizira zimenezi, wofalitsa wina mumpingo wanu angaganize zoti ayambe kuchita utumiki winawake wanthawi zonse. M’malo momulimbikitsa kuti adzikomere mtima, tiyenera kulankhula zabwino zokhudza zimene wasankhazo komanso kumuthandiza kuti akwaniritse zolinga zake.
MUZIKHALA ODZICHEPETSA
9-10. Kodi Yesu anasonyeza kudzichepetsa m’njira yapadera iti?
9 Pa usiku wake womaliza, Yesu anaphunzitsa Petulo ndi atumwi anzake mfundo yofunika kwambiri yokhudza kudzichepetsa. Patsikulo Yesu anali atatuma Petulo ndi Yohane kuti akonze zina ndi zina, pokonzekera chakudya chomaliza chomwe akanadya nawo limodzi asanaphedwe. Pokonzekerapo, ayenera kuti ankafunika kuonetsetsa kuti pali beseni la madzi komanso zopukutira n’cholinga choti alendo amene abwere adzasambitsidwe mapazi asanadye chakudya. Koma kodi ndi ndani amene akanagwira ntchito yooneka ngati yonyozekayi?
10 Mosazengereza, Yesu anasonyeza kudzichepetsa m’njira yapadera kwambiri. Atumwiwo ayenera kuti anadabwa kwambiri kuona Yesu akugwira ntchito imene nthawi zambiri inkagwiridwa ndi wantchito wapanyumba. Yesu anavula malaya ake akunja, kumanga chopukutira m’chiuno mwake, kuika madzi m’beseni n’kuyamba kuwasambitsa mapazi. (Yoh. 13:4, 5) Ziyenera kuti zinamutengera nthawi kuti asambitse mapazi a atumwi onse 12, kuphatikizapo Yudasi, yemwe anali atatsala pang’ono kumupereka. Koma modzichepetsa, Yesu anamaliza kugwira ntchitoyi. Kenako moleza mtima Yesu ananena kuti: “Kodi mukudziwa chifukwa chake ndasambitsa mapazi anu? Inu mumanditchula kuti ‘Mphunzitsiʼ komanso ‘Ambuye,’ mumalondola, chifukwa ndinedi Mphunzitsi komanso Ambuye. Choncho ngati ine amene ndi Ambuye komanso Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso mukuyenera kusambitsana mapazi.”—Yoh 13:12-14.
Kudzichepetsa kwenikweni kumaphatikizapo . . . mmene timadziganizirira ifeyo komanso anthu ena
11. Kodi Petulo anasonyeza bwanji kuti anali ataphunzira kukhala wodzichepetsa? (1 Petulo 5:5) (Onaninso chithunzi.)
11 Petulo anaphunzira kudzichepetsa kuchokera kwa Yesu. Yesu atabwerera kumwamba, Petulo anachita chozizwitsa pomwe anachiritsa munthu yemwe anabadwa ali wolumala. (Mac 1:8, 9; 3:2, 6-8) Zimene zinachitikazi zinachititsa kuti anthu ambiri asonkhane pamalowo. (Mac 3:11) Kodi Petulo akanasankha kuti ulemerero upite kwa iyeyo poganizira kuti anakulira m’chikhalidwe chomwe chimaona kuti kutchuka ndi udindo n’zofunika kwambiri? Ayi, modzichepetsa Petulo sanalole kutamandidwa. M’malomwake anapereka ulemerero kwa Yehova ndi Yesu ponena kuti: “M’dzina [la Yesu] komanso chifukwa choti timakhulupirira dzina lakelo, munthu amene mukumuona ndiponso kumudziwayu wachira.” (Mac 3:12-16) Mawu amene Petulo anagwiritsa ntchito m’kalata imene analembera Akhristu pa nkhani ya kufunika kokhala odzichepetsa, akutikumbutsa zomwe Yesu anachita pomanga chopukutira m’chiuno mwake, n’kusambitsa mapazi a atumwi ake.—Werengani 1 Petulo 5:5.
Atachita zodabwitsa, modzichepetsa Petulo anapereka ulemerero kwa Yehova ndi Yesu. Ifenso tingasonyeze kuti ndife odzichepetsa, tikamachita zabwino popanda kuyembekezera kuti ena atione kapena atipatse mphoto (Onani ndime 11-12)
12. Mofanana ndi Petulo, kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzichepetsa?
12 Tingatengere chitsanzo cha Petulo pokhala odzichepetsa. Kumbukirani kuti kudzichepetsa kwenikweni kumaphatikizapo zambiri osati kungolankhula mawu abwino. Mawu amene Petulo anagwiritsa ntchito pofotokoza za kudzichepetsa, akusonyeza kuti kudzichepetsa kumaphatikizapo mmene timaganizirira zokhudza ifeyo komanso anthu ena. Timachitira ena zabwino chifukwa chakuti timakonda Yehova ndi anthu, osati chifukwa chakuti timafuna kuti ena atione. Timasonyeza kuti ndife odzichepetsadi ngati timasangalala potumikira Yehova ndi abale athu, ngakhale ena asamaone zimene tikuchita.—Mat. 6:1-4.
MUZIKHALA “OGANIZA BWINO”
13. Kodi kukhala “oganiza bwino” kumaphatikizapo chiyani?
13 Kodi kukhala “oganiza bwino” kumaphatikizapo chiyani? (1 Pet. 4:7) Mkhristu woganiza bwino amayesetsa kusankha zochita potengera maganizo a Yehova. Mkhristu wotereyu amadziwa kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse. Iye sayenera kudziganizira kuposa mmene ayenera kudziganizirira, chifukwa amadziwa kuti sakudziwa zonse. Ndipo amasonyeza kuti amadalira Mulungu popemphera kwa iye nthawi zonse.a
14. Kodi pa nthawi ina Petulo analephera bwanji kudalira Yehova?
14 Pa usiku wake womaliza Yesu asanaphedwe, anachenjeza ophunzira ake kuti: “Nonsenu muthawa n’kundisiya ndekha usiku uno.” Petulo anayankha motsimikiza kuti: “Ngakhale ena onse atathawa n’kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!” Usiku womwewo Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Khalani maso ndipo mupitirize kupemphera.” (Mat. 26:31, 33, 41) Ngati Petulo akanatsatira malangizo amenewa poyamba pomwe, akanalimba mtima n’kuvomera kuti anali wophunzira wa Yesu. Koma m’malomwake, iye anakana Mbuye wake ndipo pambuyo pake anadzimvera chisoni kwambiri.—Mat. 26:69-75.
15. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali woganiza bwino pa usiku wake womaliza?
15 Yesu ankadalira kwambiri Yehova. Ngakhale kuti anali wangwiro, Yesu ankapemphera mobwerezabwereza kwa Atate wake. Zimenezi zinamuthandiza kuti alimbe mtima n’kuchita zimene Yehova ankafuna. (Mat. 26:39, 42, 44; Yoh 18:4, 5) N’zoonekeratu kuti kuona Yesu akupemphera kambirimbiri kunathandiza Petulo kwa moyo wake wonse.
16. Kodi Petulo anasonyeza bwanji kuti anakhala woganiza bwino? (1 Petulo 4:7)
16 Patapita nthawi, Petulo anayamba kudalira kwambiri Yehova popemphera kwa iye. Yesu, yemwe anali ataukitsidwa, anatsimikizira Petulo ndi atumwi ena kuti adzalandira mzimu woyera kuti athe kukwanitsa kugwira ntchito yolalikira. Komabe iye anawauza kuti akadikire ku Yerusalemu kufikira zimenezo zitachitika. (Luka 24:49; Mac 1:4, 5) Ndiye kodi Petulo ankachita chiyani podikirapo? Petulo ndi Akhristu anzake “ankalimbikira kupemphera.” (Mac. 1:13, 14) Pambuyo pake, m’kalata yake yoyamba, Petulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ayenera kukhala oganiza bwino komanso kudalira Yehova popemphera kwa iye. (Werengani 1 Petulo 4:7.) Petulo anaphunzira kudalira Yehova ndipo ankatha kulimbikitsa abale ndi alongo ake.—Agal. 2:9.
17. Ngakhale titakhala ndi maluso enaake apadera, kodi tiyenera kumapitiriza kuchita chiyani? (Onaninso chithunzi.)
17 Kuti tikhale oganiza bwino, tiyenera kumapemphera kwa Yehova nthawi zonse. Timazindikira kuti tiyenera kumapemphera kwa Yehova kuti azitithandiza, ngakhale zitakhala kuti tili ndi maluso enaake apadera. Timapempheranso kwa Yehova makamaka pamene tikufunika kusankha zinthu zofunika kwambiri ndipo timakhulupirira kuti iye akudziwa zomwe ndi zabwino kwambiri kwa ife.
Petulo anaphunzira kudalira Yehova popemphera kwa iye. Ifenso tingakhale oganiza bwino tikamapemphera kwa Yehova kuti atithandize, makamaka tikamasankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri (Onani ndime 17)b
18. Kodi tingatani kuti tisinthe mmene timaganizira n’kukhala ndi maganizo ngati a Yehova?
18 Timayamikira kwambiri kuti Yehova anatilenga m’njira imene tingathe kutsanzira makhalidwe ake. (Gen. 1:26) N’zoona kuti sitingathe kumutsanzira ndendende. (Yes. 55:9) Komabe mofanana ndi Petulo, tingathe kusintha n’kukhala ndi maganizo ngati a Yehova. Choncho tiyeni tipitirize kuganiza ngati mmene Yehova amaganizira, kukhala odzichepetsa komanso kukhala oganiza bwino.
NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa
a Kuti mudziwe zimene “kuganiza bwino” kumatanthauza, onani pa jw.org kapena pa JW Library, nkhani yakuti, “2 Timoteyo 1:7—Mulungu Sanatipatse Mzimu Wamantha” pa gawo lakuti “Kufotokoza Mavesi a m’Baibulo,” pansi pa kamutu kakuti “Kuganiza bwino.”
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akupemphera chamumtima pamene akuyembekezera kufunsidwa mafunso asanalembedwe ntchito.