MBIRI YA MOYO WANGA
“Yehova Ndiye Mwini Nkhondo”
PA 28 JANUARY, 2010, ndinali ndili mumzinda wokongola wa Strasbourg, ku France. Koma sindinapite kumeneko n’cholinga chokaona malo. Ndinali pa gulu la abale amene anatumizidwa kuti akaimire a Mboni za Yehova pa nkhani zamalamulo pamaso pa Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Nkhani yake inali yakuti boma la France linkanena kuti abale athu ayenera kupereka msonkho wa ndalama pafupifupi madola 89 miliyoni, womwe unali wokwera kwambiri. Chofunika kwambiri chinali chakuti kupambana pa mlanduwu kukanachititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe, anthu ake akhale ndi mbiri yabwino komanso apitirize kumulambira momasuka. Zimene zinachitika pa mlanduwu zinatsimikizira kuti “Yehova ndiye mwini nkhondo.” (1 Sam. 17:47) Dikirani ndikufotokozereni mmene zinayendera.
Mu 1999, boma la France linanena kuti ofesi yathu ya m’dzikolo inkafunika kupereka msonkho pa ndalama za zopereka zomwe inkalandira kuyambira mu 1993 mpaka 1996. Tinayesa kutengera nkhaniyi kumakhoti a ku France kuti chilungamo chioneke koma sizinathandize. Tinayesa kuchita apilo za nkhaniyi koma sizinasinthe chilichonse moti boma linalanda ndalama zoposa madola 6.3 miliyoni zomwe zinali ku akaunti ya ofesi ya nthambi. Mwayi wokhawo womwe tinali nawo kuti tibwezeredwe ndalamazi unali kutengera nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Asanamvetsere mlanduwu a khotili anakonza zoti oimira khotilo, ifeyo limodzi ndi maloya oimira boma tikambirane n’kuona ngati tingapeze njira zothetsera nkhaniyi isanapite kukhoti.
Tinkayembekezera kuti mkulu wa oimira khotiwo atikakamiza kuti tiperekeko ndalama pang’ono pa ndalama zimene boma linkafuna. Koma tinkadziwa kuti kupereka ndalama ngakhale pang’ono kukanakhala kosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Abale ndi alongo anali atapereka ndalamazo kuti zithandize pa ntchito ya Ufumu. Choncho sizinkafunika kupita ku boma. (Mat. 22:21) Choncho tinapitabe kumsonkhanoko pofuna kulemekeza malamulo a khotilo.
Ine ndi anzanga omwe ndinapita nawo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe mu 2010
Msonkhanowo unachitikira m’chipinda china cha pakhotipo chomwe chinali chokongola kwambiri. Zokambiranazo sizinayambe bwino. M’mawu ake oyamba, woimira khotiyo ananena kuti ankayembekezera kuti a Mboni za Yehova apereke zina mwa ndalamazo ku boma la France. Mosayembekezera tinangopezeka kuti tafunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti boma lalanda kale ndalama zoposa madola 6.3 miliyoni?”
Iye anadabwa kwambiri atamva zimenezi. Maloyawo atavomereza kuti boma linachitadi zimenezi, maganizo a woimira khotiyo anasinthiratu pa nkhaniyi. Iye anawakalipira kwambiri maloyawo ndipo anathetsa nkhaniyo. Ndinazindikira kuti Yehova anatithandiza m’njira imene sitinkayembekezera kuti tiwine mlanduwo. Tinachoka pamsonkhanowo tikusangalala kwambiri ndipo sitinkamvetsa zimene zinachitikazo.
Pa 30 June, 2011, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linagamula mlanduwu motikomera. Khotilo linagamula kuti sitikuyenera kupereka msonkhowo komanso kuti boma liyenera kubweza ndalama zonse zomwe linalanda limodzi ndi chiwongoladzanja. Chigamulo chosaiwalikachi chinathandiza kuti kulambira koona kuziyenda bwino ku France mpaka lero. Funso losakonzekera lija linali ngati mwala umene Davide anaphera Goliyati. Linathandiza kuti zinthu zisinthe. Koma n’chifukwa chiyani tinawina mlanduwu? Chifukwa mogwirizana ndi mawu amene Davide anauza Goliyati, “Yehova ndiye mwini nkhondo.”—1 Sam. 17:45-47.
Mlandu umene tinawina si wokhawu. Mwachitsanzo, makhoti akuluakulu a m’mayiko 70 komanso makhoti angapo oona milandu padziko lonse anagamula milandu yokwana 1,225 mokomera a Mboni za Yehova. Zigamulozi zinateteza ufulu wathu, monga ufulu wodziwika mwalamulo ngati chipembedzo, ufulu wolalikira, ufulu wokana kuchita nawo miyambo yosonyeza kukonda dziko lako komanso wokana kuikidwa magazi.
Popeza ndimatumikira ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova mumzinda wa New York, ku U.S.A, kodi zinatheka bwanji kuti ndikapezeke nawo pa milandu ya ku Europe?
NDINALEREDWA NDI MAKOLO OMWE ANALI NDI MTIMA WA UMISHONALE
Makolo anga, a George ndi a Lucille, omwe analowa kalasi nambala 12 ya Sukulu ya Giliyadi, ankatumikira ku Ethiopia ndipo ine ndinabadwa mu 1956. Iwo anandipatsa dzina lakuti Philip potengera dzina la mlaliki wina wa m’nthawi ya atumwi. (Mac. 21:8) M’chaka chotsatira boma linaletsa kulambira kwathu. Ngakhale kuti pa nthawiyi ndinali wamng’ono kwambiri ndimakumbukira kuti banja lathu linkalambira mobisa. Monga mwana, ndinkaganiza kuti zimenezi ndi zosangalatsa. Koma ndi zomvetsa chisoni kuti mu 1960, akuluakulu a boma anatiuza kuti tichoke m’dzikolo.
M’bale Nathan H. Knorr (kumanzere) atabwera kudzaona banja lathu ku Addis Ababa, ku Ethiopia, mu 1959
Banja lathu linasamukira m’tauni ya Wichita, ku Kansas, ku U.S.A. Makolo anga ankakondabe kulalikira ngati mmene ankachitira ali amishonale. Iwo ankakonda kwambiri choonadi moti anaphunzitsa ineyo, mlongo wanga wamkulu Judy ndi mng’ono wanga Leslie kuti tizikonda komanso kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Azibale angawanso anabadwira ku Ethiopia. Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 13. Papita zaka zitatu, banja lathu linasamukira ku Arequipa, ku Peru, komwe kunkafunika olalikira ambiri.
Mu 1974, ndili ndi zaka 18 zokha, ofesi yanthambi ya ku Peru inandipempha ine ndi abale ena 4 kuti tizikatumikira monga apainiya apadera. Tinkakalalikira kumadera komwe kunali kusanalalikidwepo kumapiri a Andes. Tinkalalikiranso kwa anthu a kuderalo olankhula Chikwechuwa ndi Chiayimara. Tinkayenda pa galimoto yomwe tinkangoitchula kuti chingalawa chifukwa cha mmene inkaonekera. Ndimasangalala ndikamakumbukira nthawi imene ndinkagwiritsa ntchito Baibulo pothandiza anthu a m’deralo kudziwa kuti posachedwapa Yehova athetsa mavuto onse monga umphawi, matenda komanso imfa. (Chiv. 21:3, 4) Anthu ambiri ankamvetsera uthenga wa Ufumu ndipo anayamba kutumikira Yehova.
Chingalawa, mu 1974
NDINAKAYAMBA KUTUMIKIRA KULIKULU LATHU LA PADZIKO LONSE
Mu 1977, M’bale Albert Schroeder, yemwe anali wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anabwera kudzayendera nthambi ya ku Peru. Iye anandilimbikitsa kuti ndifunsire utumiki wa pa Beteli ndipo ndinachitadi zimenezo. Pasanapite nthawi yaitali, pa 17 June, 1977, ndinayamba kutumikira ku Beteli ya ku Brooklyn. Pa zaka 4 zotsatira, ndinatumikira mu dipatimenti yoyeretsa komanso yokonza zinthu.
Pa tsiku la ukwati wathu, mu 1979
Mu June 1978, ndinakumana ndi Elizabeth Avallone kumsonkhano wa mayiko, womwe unachitikira ku New Orleans, ku Louisiana. Iyenso analeredwa ndi makolo omwe mofanana ndi makolo anga ankakonda choonadi. Elizabeth anali atatumikira Yehova monga mpainiya wokhazikika kwa zaka 4 ndipo ankafuna kuchita utumiki wa nthawi zonse kwa moyo wake wonse. Tinayamba kucheza, ndipo pasanapite nthawi yaitali tinayamba kukondana kwambiri. Tinakwatirana pa 20 October, mu 1979 ndipo tinayamba kutumikira pa Beteli monga banja.
Abale ndi alongo a mumpingo wathu woyamba wa Brooklyn Spanish ankatikonda kwambiri. Pa zaka zimenezi tatumikiranso m’mipingo ina itatu ndipo abale ndi alongo akhala akutilimbikitsa komanso kutithandiza pa utumiki wathu wa pa Beteli. Timayamikira kwambiri thandizo lawo komanso la anzathu ndi achibale omwe ankatithandiza kusamalira makolo athu okalamba.
Abale ndi alongo a pa Beteli omwe ankasonkhana mumpingo wa Brooklyn Spanish, mu 1986
NDINAYAMBA KUTUMIKIRA M’DIPATIMENTI YA ZAMALAMULO
Mu January 1982, ndinadabwa kuti ndinapemphedwa kuti ndizitumikira m’Dipatimenti ya Zamalamulo ya ku Beteli. Patapita zaka zitatu, ananditumiza kuyunivesite kuti ndikachite maphunziro a zamalamulo kuti ndikhale loya. Pamene ndinkaphunzira, ndinadabwa kuona kuti maufulu amene anthu ambiri ankawanyalanyaza m’dziko la United States komanso mayiko ena, analimbikitsidwa chifukwa cha milandu imene a Mboni za Yehova anawina. Anthu ankakambirana kwambiri milandu yofunikayi m’kalasi.
Mu 1986 ndili ndi zaka 30, ndinaikidwa kukhala woyang’anira Dipatimenti ya Zamalamulo. Ndinkaona kuti ndi mwayi waukulu, koma popeza ndinali wamng’ono ndipo sindinkadziwa zambiri zokhudza utumikiwu, ndinkachita mantha.
Ndinamaliza maphunziro anga ndipo ndinakhala loya mu 1988, koma sindinkadziwa kuti maphunzirowa akhoza kusokoneza moyo wanga wauzimu. Maphunziro apamwamba angachititse kuti munthu ayambe kudzikweza n’kumadziona ngati wofunika kuposa anthu amene sanachite maphunziro ofanana ndi ake. Koma Elizabeth anandithandiza kuti ndiyambirenso kuchita zinthu zimene zinandithandiza kuti ndikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ngati mmene zinalili ndisanapite kusukulu ya zamalamulo. Zinatenga nthawi, kenako ubwenzi wanga ndi Yehova unalimbanso. Ndatsimikizira kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo si kukhala ndi maphunziro enaake apadera. Chofunika ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kumukonda komanso kukonda anthu ake.
KUTETEZA NDI KUKHAZIKITSA MWALAMULO NTCHITO YOLALIKIRA UTHENGA WABWINO
Nditamaliza maphunziro a zamalamulo ndinayamba kuthandiza pa ntchito yokhudza zamalamulo pa Beteli komanso kuteteza gulu la Mulungu ndi ufulu wathu wolalikira. Ntchito yanga inali yosangalatsa koma yovuta chifukwa zinthu zinkasintha mofulumira m’gulu lathu. Mwachitsanzo, kuyambira mu 1991, Dipatimenti ya Zamalamulo inapemphedwa kuti ithandize popereka malangizo akuti mabuku athu asamakhale ndi mtengo. Kuyambira nthawi imeneyi, a Mboni za Yehova amapereka mabuku popanda kutchula mtengo. Zimenezi zinachepetsa ntchito ku Beteli komanso kufiludi ndipo mpaka pano, zimathandiza kuti tisamalipitsidwe misonkho yosafunika. Ena ankaganiza kuti kusintha kumeneku kuchititsa kuti gulu lizipeza ndalama zochepa ndipo kusokoneza ntchito yolalikira. Koma si zimene zinachitika. Chiwerengero cha amene akutumikira Yehova kuyambira m’ma 1990 chawonjezereka kwambiri, ndipo masiku ano anthu angathe kupeza chakudya chauzimu chopatsa moyo popanda kulipira kalikonse. Ndaona kuti mphamvu imene Yehova amapereka komanso malangizo amene amatipatsa kudzera mwa kapolo wokhulupirika, ndi zimene zathandiza kuti kusintha kumeneku komanso kusintha kwina komwe kwachitika m’gululi, kukhale kotheka.—Eks. 15:2; Mat. 24:45.
Sikuti timawina milanduyi chifukwa chokhala ndi maloya abwino otiimira m’makhoti. Nthawi zambiri, chimene chimachititsa akuluakulu a boma kuti atithandize ndi khalidwe labwino la anthu a Yehova. Ndinaona chitsanzo cha zimenezi mu 1998 pamene abale atatu a m’Bungwe Lolamulira ndi akazi awo anakapezeka pamisonkhano yapadera ku Cuba. Iwo anali okoma mtima komanso aulemu, ndipo zimenezi zinapereka umboni wamphamvu kwa akuluakulu a boma woti sitichita nawo zandale kuposa zimene tinkakambirana nawo tikakumana pamisonkhano yosiyanasiyana.
Komabe nthawi zina nkhani zokhudza malamulo zimalephereka kuzithetsa pongokambirana. Zikatero timafunika kupita kukhoti n’cholinga chofuna ‘kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito yolengeza uthenga wabwino.’ (Afil. 1:7) Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri akuluakulu a boma ku Europe ndi ku South Korea sankazindikira ufulu wathu wokana kugwira ntchito za usilikali. Chifukwa cha zimenezi, abale 18,000 ku Europe komanso oposa 19,000 ku South Korea anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali.
Pamapeto pake, pa 7 July 2011, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapereka chigamulo chosaiwalika pa mlandu wa pakati pa a Bayatyan ndi boma la Armenia. Chigamulo chimenechi chinathandiza kuti a Mboni za Yehova ku Europe azipatsidwa ntchito zina m’malo mwa usilikali. Chigamulo ngati chimenechi chinaperekedwanso ndi khoti la ku South Korea pa 28 June 2018. Sizikanatheka kupambana pa milandu imeneyi zikanakhala kuti abale achinyamata a m’mayiko amenewa ankavomera kulowa usilikali.
Abale a mu Dipatimenti ya Zamalamulo kulikulu lathu komanso m’maofesi a nthambi padziko lonse amagwira ntchito mwakhama poteteza ufulu wathu wolambira komanso ntchito yolalikira uthenga wabwino. Timayamikira kwambiri mwayi woimira abale ndi alongo athu omwe akutsutsidwa ndi boma. Kaya tiwine mlandu kapena ayi, kupezeka kwathu m’makhoti kumathandiza kuti tilalikire kwa akuluakulu a boma, mafumu komanso mitundu ya anthu. (Mat. 10:18) Oweruza, oimira boma, atolankhani komanso anthu ena amaganizira malemba amene timagwiritsa ntchito pa milanduyi. Anthu oona mtima amadziwa zambiri zokhudza a Mboni za Yehova komanso kuti zimene timakhulupirira zimachokera m’Baibulo. Ena mwa anthu amenewa amayamba kulambira Yehova.
ZIKOMO YEHOVA
Pa zaka 40 zapitazi, ndakhala ndi mwayi wogwira ntchito ndi abale m’maofesi a nthambi padziko lonse pa nkhani zamalamulo komanso kuonekera m’makhoti osiyanasiyana ndiponso pamaso pa akuluakulu a boma ambiri. Ndimakonda komanso kuyamikira anzanga omwe ndimagwira nawo ntchito m’Dipatimenti ya Zamalamulo kulikulu lathu ndiponso amene ali m’maofesi a nthambi padziko lonse. Yehova wakhala akundidalitsa ndipo ndimasangalala.
Pa zaka 45 zapitazi, Elizabeth wakhala akundithandiza mokhulupirika komanso mwachikondi pa nthawi zabwino komanso zovuta. Ndimamuyamikira chifukwa wakhala akuchita zimenezi ngakhale kuti akudwala matenda omwe amachititsa kuti chitetezo cha m’thupi lake chizikhala chotsika komanso mphamvu zake zizichepa.
Taona kuti Yehova ndi amene amatipatsa mphamvu komanso kutithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino. Paja Davide ananena kuti, “Yehova ndi mphamvu kwa anthu ake.” (Sal. 28:8) Kunena zoona, “Yehova ndiye mwini nkhondo.”