MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Muziuza Ena Zimene Mwaphunzira
Timatsitsimulidwa tikamaphunzira patokha, koma timatsitsimulidwa kwambiri tikamauza ena mfundo zolimbikitsa zimene tapeza. Lemba la Miyambo 11:25 limati: “Amene amatsitsimula ena nayenso adzatsitsimulidwa.”
Tikamauza ndi ena zimene taphunzira, m’pamenenso timazikumbukira mosavuta komanso kuzimvetsa bwino. Timasangalala kugawana ndi ena mfundo zimenezo chifukwa timadziwa kuti zingawathandize.—Mac. 20:35.
Tayesani izi: Mlungu ukubwerawu, yesetsani kupeza mpata woti muuzeko zimene mwaphunzira. Mungauze wachibale wanu, munthu wina mumpingo, amene mumagwira naye ntchito, mnzanu wakusukulu, woyandikana naye nyumba kapena munthu amene mungakumane naye mu utumiki. Muziyesa kufotokoza m’mawu anuanu komanso momveka bwino.
Kumbukirani: Muziuza ena zimene mwaphunzira n’cholinga choti muwalimbikitse, osati kuwagometsa.—1 Akor. 8:1.