Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 August tsamba 26-30
  • Ngakhale Kuti Ndinali Wamanyazi, Ndinakhala Mmishonale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngakhale Kuti Ndinali Wamanyazi, Ndinakhala Mmishonale
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NDINAYAMBA UTUMIKI WANTHAWI ZONSE
  • CHOLINGA CHOCHITA UMISHONALE
  • KUTUMIKIRA M’DZIKO LANKHONDO
  • TINAKUMANA NDI MAVUTO ENA
  • MAVUTO OKHUDZA THANZI
  • NDIMAYAMIKIRA KUTI YEHOVA AMANDITHANDIZA
  • Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali
    Galamukani!—2011
  • Ntchito Yapadera ku Bulgaria Inali ndi Zotsatira Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Mumangowona Kawonekedwe Kakunja?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Yehova Wakhala ‘Akuwongola Njira Zanga’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 August tsamba 26-30
Marianne Wertholz.

MBIRI YA MOYO WANGA

Ngakhale Kuti Ndinali Wamanyazi, Ndinakhala Mmishonale

YOFOTOKOZEDWA NDI MARIANNE WERTHOLZ

NDILI mwana ndinali wamanyazi ndipo ndinkaopa anthu. Koma patapita nthawi, Yehova anandithandiza ndipo ndinadzakhala mmishonale wokonda anthu. Poyamba anandithandiza ndi bambo anga. Kenako mlongo wina wachitsikana anandipatsa chitsanzo chabwino. Pomaliza, ndinathandizidwa ndi mwamuna wanga yemwe ankalankhula nane mokoma mtima komanso moleza mtima. Dikirani ndikufotokozereni nkhani yonse.

Ndinabadwa mu 1951, ku Vienna m’dziko la Austria, ndipo makolo anga anali a Chikatolika. Ndinali wamanyazi koma ndinkakhulupirira Mulungu ndipo ndinkapemphera pafupipafupi. Ndili ndi zaka 9, bambo anga anayamba kuphunzira ndi a Mboni za Yehova ndipo patapita kanthawi pang’ono mayi anga anayambanso kuphunzira.

Ndili ndi mng’ono wanga, Elisabeth (kumanzere)

Pasanapite nthawi yaitali tinayamba kusonkhana mumpingo wa Döbling ku Vienna. M’banja lathu tinkachitira limodzi zinthu zambiri. Tinkawerenga komanso kuphunzira Baibulo, kupezeka pamisonkhano ya mpingo ndiponso tinkadzipereka kugwira ntchito zosiyanasiyana pamisonkhano yadera. Kuyambira ndili mwana, bambo anga anandithandiza kuti ndizikonda Yehova. Ndipo nthawi zonse bambo anga ankapemphera kuti ine ndi mchemwali wanga tidzakhale apainiya. Koma pa nthawiyo chimenechi sichinali cholinga changa.

NDINAYAMBA UTUMIKI WANTHAWI ZONSE

Ndinabatizidwa mu 1965, ndili ndi zaka 14. Komabe zinkandivuta kulalikira kwa anthu osawadziwa. Ndinkalimbananso ndi maganizo odziona ngati wotsika ndipo ndinkafunitsitsa kuti achinyamata ena azindikonda. Choncho pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene ndinabatizidwa, ndinayamba kucheza ndi anthu amene sankatumikira Yehova. Ngakhale kuti ndinkasangalala ndikamacheza nawo, chikumbumtima changa chinkandivutitsa chifukwa nthawi zambiri ndinkakhala ndi anthu omwe si a Mboni. Koma zinkandivuta kuti ndisinthe. Ndiye kodi chinandithandiza ndi chiyani?

Marianne ndi Dorothée.

Ndinaphunzira zambiri kwa Dorothée (kumanzere)

Pa nthawiyi mlongo wina wa zaka 16 dzina lake Dorothée anakhala wofalitsa mumpingo wathu. Ndinachita chidwi ndi mmene ankakondera ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. Ndinali wamkulupo kuposa iyeyo koma ine sindinkakonda kwambiri kulalikira. Ndiye ndinaganiza kuti: ‘Makolo anga ndi a Mboni, koma Dorothée alibe achibale omwe ndi a Mboni. Amakhala ndi mayi ake omwe akudwala koma nthawi zonse amapita kukalalikira.’ Chitsanzo chake chinandilimbikitsa kuti ndiyambe kuchita zambiri potumikira Yehova. Pasanapite nthawi yaitali, ine ndi Dorothée tinayamba upainiya. Poyamba tinkachita upainiya wothandiza ndipo kenako tinayamba upainiya wokhazikika. Chifukwa chakuti Dorothée ankakonda kwambiri ntchito yolalikira, inenso ndinayamba kuikonda ntchitoyi. Iye anandithandiza kuyambitsa phunziro la Baibulo langa loyamba. Patapita nthawi ndinayamba kukhala womasuka kulalikira kwa anthu kunyumba zawo, mumsewu komanso m’malo ena.

M’chaka chimene ndinayamba upainiya, m’bale wina wa ku Austria komweko anabwera mumpingo wathu. Dzina lake anali Heinz ndipo anaphunzira choonadi pamene anapita ku Canada kukacheza kwa mchimwene wake yemwe anali wa Mboni. Heinz anatumizidwa mumpingo wathu ku Vienna ngati mpainiya wapadera. Ndinayamba kumukonda nditangomuona. Iye ankafuna kudzachita umishonale pomwe ine ndinalibe cholinga chimenechi. Choncho poyamba sindinafune kuti adziwe kuti ndikumufuna. Komabe patapita nthawi tinayamba chibwenzi, kenako tinakwatirana ndipo tinkachita limodzi upainiya ku Austria.

CHOLINGA CHOCHITA UMISHONALE

Nthawi ndi nthawi Heinz ankandiuza za cholinga chake chofuna kudzachita umishonale. Ngakhale kuti sankandikakamiza, ankandifunsa mafunso olimbikitsa monga akuti: “Popeza tilibe ana, kodi sitingachite zambiri potumikira Yehova?” Popeza ndine wamanyazi, ndinkaopa kukhala mmishonale. N’zoona kuti ndinkachita upainiya, koma ndikaganizira za umishonale ndinkachita mantha. Komabe Heinz anapitiriza kundithandiza moleza mtima kuti ndikhale ndi cholinga chimenechi. Anandithandizanso kuti ndiziganizira kwambiri zothandiza anthu ena m’malo moganizira kwambiri za ineyo. Malangizo ake anandithandiza kwambiri.

Heinz akuchititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda mumpingo waung’ono wa chilankhulo cha ku Yugoslavia ku Salzburg, ku Austria, mu 1974

Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kufuna ntchito ya umishonale, choncho tinafunsira Sukulu ya Giliyadi. Koma mtumiki wa nthambi anandiuza kuti ndiyambe kaye ndaphunzira bwino Chingelezi. Patapita zaka zitatu ndikuphunzira Chingelezi, tinadabwa kulandira kalata yotiuza kuti tizikatumikira mumpingo wa chilankhulo cha ku Yugoslavia womwe unali ku Salzburg, ku Austria. Tinatumikira m’gawo limeneli kwa zaka 7 ndipo kwa chaka chimodzi tinatumikira ngati woyang’anira dera. Chilankhulo chake chinali chovuta koma tinali ndi maphunziro a Baibulo ambiri.

Mu 1979, tinapemphedwa kuti tipite Bulgaria. Kumeneku ntchito yolalikira inali yoletsedwa ndiye tinangopita ngati kutchuthi. Pa nthawi yonse imene tinali kumeneko sitinkalalikira. Komabe tinakwanitsa kunyamula mobisa mabuku athu ang’onoang’ono amene tinakapatsa alongo 5 omwe ankakhala mumzinda wa Sofia, umene ndi likulu la dzikoli. Ndinkachita mantha koma Yehova anandithandiza kuti ndigwire ntchito yosangalatsayi. Kuona kuti alongowa anali olimba mtima komanso osangalala ngakhale kuti akanatha kumangidwa nthawi ina iliyonse, kunandithandiza kuti ndizichita zonse zimene ndingathe pa utumiki uliwonse umene gulu la Yehova lingandipatse.

Patapita nthawi tinafunsiranso Sukulu ya Giliyadi ndipo pa nthawiyi anatiitana. Tinkaganiza kuti tikachitira sukuluyi ku United States m’Chingelezi. Koma mu November 1981, gulu linayamba kukhalanso ndi makalasi a sukuluyi ku nthambi ya ku Wiesbaden, m’dziko la Germany. Choncho tinali ndi mwayi wochita maphunzirowa m’Chijeremani, chomwe chinali chosavuta kwa ine. Koma kodi pambuyo pake tikanatumizidwa kuti?

KUTUMIKIRA M’DZIKO LANKHONDO

Tinatumizidwa kuti tizikatumikira m’dziko la Kenya. Koma ofesi ya nthambi ya ku Kenya inatipempha ngati tingakonde kuti tikatumikire m’dziko loyandikana nalo la Uganda. Zaka zoposa 10 m’mbuyomo, asilikali anali atalanda boma motsogoleredwa ndi mkulu wawo wankhondo dzina lake Idi Amin. M’zaka zotsatira, ulamuliro wake wankhanza unachititsa kuti anthu ambiri aphedwe komanso mamiliyoni ambiri azivutika. Kenako mu 1979, adani ake a Idi Amin anamuthamangitsa m’dzikolo n’kuthetsa ulamuliro wake. Apa mwina mungamvetse chifukwa chake ndinkaopa kukatumikira m’dziko limene munali nkhondo. Koma Sukulu ya Giliyadi inatikonzekeretsa kuti tizidalira Yehova. Choncho tinalolera kupita.

Moyo ku Uganda unali wovuta kwambiri. Mu Buku Lapachaka la 2010, Heinz anafotokoza mmene moyo unalili. Iye anati: “Zinthu zambiri, . . . zinasokonekera. Mayendedwe anali ovuta ndipo madzi ankasowa. . . . Kuomberana, umbava komanso umbanda zinkachitika kwambiri makamaka usiku. . . . Aliyense ankangokhala m’nyumba, moti usiku anthu ankangopemphera kuti bola kuche.” Ngakhale kuti panali mavuto onsewa, abale ndi alongo a m’dzikolo ankatumikira Yehova mosangalala.

Tikukonza chakudya kunyumba kwa a Waiswa

Mu 1982, ine ndi Heinz tinafika mumzinda wa Kampala, womwe ndi likulu la dziko la Uganda. Miyezi 5 yoyambirira tinkakhala kunyumba kwa a Sam ndi a Christina Waiswa, omwe ankakhala ndi ana awo 5 komanso achibale ena 4. Banja la a Waiswa linkadya kamodzi patsiku ndipo zinali zochititsa chidwi kuti anatilandira. Pa nthawi imene ine ndi Heinz tinkakhala kwa a Waiswa, tinaphunzira zinthu zambiri zomwe zinatithandiza pa utumiki wathu wa umishonale. Mwachitsanzo, tinaphunzira kugwiritsa ntchito madzi ochepa posamba ndipo omwe atsala tinkagejemulira toilet. Mu 1983, ine ndi Heinz tinapeza nyumba m’dera lina lotetezekako ku Kampala.

Tinkasangalala kwambiri ndi ntchito yolalikira. Ndimakumbukira kuti mwezi wina tinagawira magazini oposa 4,000. Koma anthu a kumeneko ndi amene ankatisangalatsa kwambiri. Ankalemekeza Mulungu ndipo ankakonda kukambirana za m’Baibulo. Ine ndi Heinz, aliyense ankakhala ndi maphunziro a Baibulo 10 kapena 15. Ndipo tinaphunzira zambiri kwa anthu amene tinkawaphunzitsa. Mwachitsanzo, mlungu uliwonse iwo ankayenda wapansi pobwera kumisonkhano koma sankadandaula ndipo ankamwetulira nthawi zonse.

Mu 1985 ndi 1986, ku Uganda kunachitikanso nkhondo maulendo ena awiri. Nthawi zambiri tinkaona ana omwe ankagwiritsidwa ntchito ngati asilikali atanyamula mifuti n’kuima m’malodibuloko. Pa nthawiyo tinkapempha Yehova kuti atipatse nzeru komanso atithandize kukhala odekha pamene tinkafunafuna anthu achidwi mu utumiki. Yehova anayankha mapemphero athu. Nthawi zambiri mantha athu ankachepa tikakumana ndi munthu amene akufuna kumvetsera uthenga wa Ufumu.

Ine, Tatjana (pakati) ndi Heinz

Tinkasangalalanso kulalikira anthu ochokera m’mayiko ena. Mwachitsanzo, tinkaphunzira Baibulo ndi Murat ndi Dilbar Ibatullin, banja lomwe linachokera ku Tatarstan ku Russia. Murat anali dokotala. Banjali linayamba choonadi ndipo lakhala likutumikira Yehova mokhulupirika mpaka pano. Kenako ndinakumana ndi mayi wina wa ku Ukraine dzina lake Tatjana Vileyska, yemwe anali ndi nkhawa kwambiri moti ankafuna kudzipha. Iye atabatizidwa anabwerera ku Ukraine ndipo ankagwira ntchito yomasulira mabuku athu.a

TINAKUMANA NDI MAVUTO ENA

Mu 1991 ine ndi Heinz tili kutchuthi ku Austria, ofesi ya nthambi inatipempha kuti tizikatumikira ku Bulgaria. Ulamuliro wa chikomyunizimu utatha m’mayiko ena a ku Europe, a Mboni za Yehova ankaloledwa kugwira ntchito yolalikira ku Bulgaria. Monga ndinafotokozera, m’mbuyomo ine ndi Heinz tinapititsako mabuku athu mobisa pa nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa. Koma pa nthawiyi tinatumizidwa kuti tizikalalikira kumeneko.

Tinauzidwa kuti tisabwererenso ku Uganda. Choncho sitinabwerere kukatenga zinthu kunyumba yathu ya amishonale kapenanso kukatsanzikana ndi anzathu. M’malomwake tinapita ku Beteli ya ku Germany ndipo tinapatsidwa galimoto kenako n’kupita ku Bulgaria. Tinapemphedwa kuti tizikasonkhana limodzi ndi kagulu ka ofalitsa pafupifupi 20 ku Sofia.

Ku Bulgaria tinakumana ndi mavuto enanso. Choyamba, sitinkadziwa chilankhulo cha kumeneko. Kuwonjezera pamenepo, mabuku okhawo amene analipo m’chilankhulo cha ku Bulgaria anali Choonadi Chimene Chimatsogolera ku Moyo Wamuyaya ndi Buku Langa la Nkhani za M’Baibulo. Choncho zinali zovuta kuti tiyambe kuphunzira Baibulo ndi anthu. Ngakhale kuti panali mavuto amenewa, kagulu kathuka kankalalikira kwambiri. Anthu a Tchalitchi cha Orthodox anaona zimenezi ndipo pamenepa m’pamene panayambira mavuto aakulu.

Mu 1994, boma la dzikolo linasiya kuona a Mboni za Yehova ngati chipembedzo chovomerezeka. Abale ena anamangidwa. Ofalitsa nkhani ankalemba mabodza oipa okhudza a Mboni za Yehova. Iwo ankanena kuti a Mboni amapha ana awo pokana kuti aikidwe magazi komanso amalimbikitsa Akhristu anzawo kuti azidzipha. Choncho ine ndi Heinz zinkativuta kuti tizilalikira. Nthawi zambiri tikamalalikira tinkakumana ndi anthu aukali omwe ankatikuwiza, kutiitanira apolisi komanso kutigenda. Zinali zosatheka kuti tizilandira mabuku m’dzikoli ndipo kuchita lendi malo oti tizichitirapo misonkhano kunali kovuta. Nthawi ina apolisi anasokoneza msonkhano wathu wachigawo. Ine ndi Heinz tinali tisanazolowere kukhala ndi anthu opanda chikondi ngati amenewa. Anthuwa anali osiyana ndi a ku Uganda omwe ankakonda kuphunzira Baibulo. Ndiye kodi n’chiyani chinatithandiza kulimbana ndi mavutowa?

Kucheza ndi abale ndi alongo athu n’kumene kunatithandiza kwambiri. Iwo ankasangalala kwambiri kuti anapeza choonadi komanso ankayamikira zimene tinkachita powathandiza. Abale ndi alongowa ankagwirizana komanso kuthandizana. Tinaphunzira kuti tikhoza kumasangalala ndi utumiki uliwonse ngati timakonda anthu.

Marianne ndi Heinz Wertholz.

Tili ku nthambi ya ku Bulgaria, mu 2007

Koma patapita nthawi zinthu zinasintha. Mu 1998, gulu lathu linavomerezedwa ndi boma ndipo mabuku athu anayamba kumasuliridwa mu Chibugariya. Kenako mu 2004, kunamangidwa ofesi ya nthambi. Panopa ku Bulgaria kuli mipingo 57 komanso ofalitsa 2,953. Mu 2024, anthu oposa 6,475 anapezeka pa Chikumbutso. Pa nthawi ina ku Sofia kunali alongo 5 okha, koma panopa kuli mipingo 9. Taona ‘wamng’ono akusanduka anthu 1,000.’​—Yes. 60:22.

MAVUTO OKHUDZA THANZI

Pa moyo wanga ndakhala ndikukumana ndi mavuto ambiri okhudza thanzi. Pa zaka zapitazi ndakhala ndikuvutika ndi zotupa, kuphatikizapo china chomwe chinali m’mutu. Ndinalandira thandizo la mankhwala amphamvu lomwe linachititsa kuti chotupacho chibwerere. Komanso ndinapita kuchipatala ku India komwe ndinachitidwa opaleshoni ya maola 12, ndipo anakwanitsa kuchotsa mbali yaikulu ya chotupacho. Pambuyo pa opaleshoniyo tinakhala kunthambi ya ku India, ndipo nditapeza bwino tinabwerera ku utumiki wathu ku Bulgaria.

Pasanapite nthawi yaitali, Heinz anayamba kudwala matenda ena achilendo omwe ankachititsa kuti azilephera kulankhula ngakhalenso kuyenda. Pamene matendawo ankakulirakulira ndinkafunika kuti ndizimuthandiza pa zinthu zambiri. Nthawi zina ndinkatopa kwambiri komanso ndinkakhala ndi nkhawa kuti mwina sindizitha kumusamalira. Koma wachinyamata wina dzina lake Bobi nthawi zambiri ankamutenga Heinz akamakalalikira. Bobi sankachita manyazi ndi mmene Heinz ankalankhulira kapenanso chifukwa chakuti ankalephera kuyenda. Nthawi zonse ndinkadalira Bobi kuti andithandiza pamene sindikanakwanitsa kumuthandiza Heinz. Ngakhale kuti ine ndi Heinz tinasankha kuti tisakhale ndi ana, tinkaona kuti Yehova watipatsa Bobi ngati mwana wathu.​—Maliko 10:29, 30.

Heinz anapezekanso ndi matenda a khansa, ndipo n’zomvetsa chisoni kuti mwamuna wanga wokondedwayu anamwalira mu 2015. Ndimamusowa kwambiri mwamuna wanga chifukwa ndi amene ankandithandiza kuti ndisamade nkhawa, moti zinandivuta kukhulupirira kuti iye kulibenso. Koma ndimamuganizira kwambiri moti kwa ine zimangokhala ngati adakali moyo. (Luka 20:38) Tsiku lililonse ndimaganizira mawu okoma mtima omwe ankandilankhula komanso malangizo abwino omwe ankandipatsa. Ndimayamikira kuti kwa zaka zambiri tinatumikira limodzi Yehova mokhulupirika.

NDIMAYAMIKIRA KUTI YEHOVA AMANDITHANDIZA

Yehova wandithandiza kupirira mayesero anga onse. Iye anandithandizanso kuthana ndi vuto langa la manyazi lija n’kukhala mmishonale wokonda kwambiri anthu. (2 Tim. 1:7) Ndimathokoza Yehova kuti ine ndi mng’ono wanga tili mu utumiki wanthawi zonse. Panopa iye ndi mwamuna wake akutumikira monga oyang’anira dera ndipo amayendera mipingo yolankhula Chisebiya ku Europe. Yehova anayankha mapemphero a bambo anga omwe ankapereka tili ana.

Kuphunzira Baibulo kumandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wamumtima. Pamene ndakumana ndi mavuto, ndaphunzira kupemphera “ndi mtima wonse” ngati mmene Yesu ankachitira. (Luka 22:44) Njira imodzi imene Yehova amayankhira mapemphero anga, ndi kudzera mwa anzanga a mumpingo wa Nadezhda, ku Sofia, omwe amandisonyeza chikondi ndi kukoma mtima. Iwo amandiitana kuti ndikacheze nawo ndipo nthawi zambiri amandiyamikira, zomwe zimachititsa kuti ndizisangalala kwambiri.

Nthawi zambiri ndimaganizira za chiyembekezo chathu chakuti akufa adzauka. M’maganizo, ndimaona makolo anga ataima kutsogolo kwa nyumba yathu, akuoneka okongola ngati mmene ankaonekera atangokwatirana kumene. Ndimaona mng’ono wanga akukonza chakudya. Ndimaonanso Heinz ataima pafupi ndi hatchi yake. Kuganizira zimenezi kumandithandiza kuti ndisamakhale ndi nkhawa ndipo ndimayamikira kwambiri Yehova.

Ndikaganizira zimene Yehova wandichitira pa moyo wanga komanso zimene akuyembekezera kundichitira m’tsogolo, ndimamva ngati Davide, yemwe pa Salimo 27:13, 14 anati: “Kodi ndikanakhala ndili kuti ndikanapanda kukhala ndi chikhulupiriro choti ndidzaona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu amoyo? Yembekezera Yehova. Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Inde, yembekezera Yehova.”

a Onani mbiri ya moyo wa Tatjana Vileyska mu Galamukani! ya Chingelezi ya December 22, 2000, tsamba 20-24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena