Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino idzatha liti?
Yesu anati: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:14) Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “mapeto” pavesili komanso mu vesi 6 ndi 13, ndi akuti teʹlos. Mawuwa akunena za mapeto a dziko la Satanali pa Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Choncho tidzapitiriza kulalikira uthenga wabwino mpaka Aramagedo itatsala pang’ono kuyamba. Zimenezi zikusintha zomwe tinkafotokoza poyamba.
M’mbuyomu tinkakhulupirira kuti tidzasiya kulalikira uthenga wabwino chisautso chachikulu chikadzayamba ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu. (Chiv. 17:3, 5, 15, 16) Tinkakhulupirira kuti chisautsochi chikamadzayamba, kudzakhala kutha kwa “chaka [chophiphiritsa] cha Yehova chokomera anthu mtima.” (Yes. 61:2) Tinkakhulupiriranso kuti anthu amene adzapulumuke chisautso chachikulu adzayenera kukhala atasonyeza kukhulupirika kwawo chisautsocho chisanayambe. Tinkawayerekezera ndi Ayuda omwe anapulumuka mu 607 B.C.E., pamene Yerusalemu ankawonongedwa. Ayudawo anali atayikidwa kale chizindikiro chakuti apulumuka chifukwa ankalambira Yehova komanso kudana ndi zoipa. (Ezek. 5:11; 9:4) Koma kuyerekezera kumeneku sikukugwirizana ndi mawu a Yesu a pa Mateyu 24:14, omwe amasonyeza kuti anthu adzakhala ndi mwayi womvetsera uthenga wabwino n’kusintha mpaka Aramagedo itangotsala pang’ono kuyamba.
Kumvetsa lemba la Mateyu 24:14, kukusinthanso mmene tinkamvera lemba la Chivumbulutso 16:21, lomwe limanena za uthenga wokhala ngati matalala. Kufufuza mowonjezereka kukusonyeza kuti malemba awiriwa ndi ogwirizana. Tikutero chifukwa cha zimene anthu amachita akamva uthenga wa Ufumu. Mtumwi Paulo analemba kuti kwa “anthu amene akukapulumutsidwa,” uthenga wa Ufumu uli ngati “kafungo kabwino ka moyo.” Koma kwa adani a Mulungu, uthengawu si wabwino ndipo uli ngati “fungo la imfa.” (2 Akor. 2:15, 16) Adani a Mulunguwa amadana ndi uthenga wa Ufumu chifukwa umafotokoza kuti dziko lomwe amalikondali ndi loipa, ndi lolamulidwa ndi Satana komanso posachedwapa liwonongedwa.—Yoh. 7:7; 1 Yoh. 2:17; 5:19.
Onaninso kuti matalala otchulidwa pa Chivumbulutso 16:21, adzakhala ‘aakulu modabwitsa.’ Zimenezi zikusonyeza kuti uthenga umene uzidzalalikidwa pa chisautso chachikulu udzakhala wopweteka kwambiri kwa adani a Mulungu, chifukwa dzina la Yehova lidzadziwika kwambiri kuposa kale. (Ezek. 39:7) Kodi pa nthawi ya mapeto ngati imeneyo, pambuyo poti Babulo Wamkulu wawonongedwa, padzakhalanso anthu amene adzamvetsere uthengawu n’kumauona ngati kafungo konunkhira bwino? Zimenezotu n’zotheka. N’kutheka kuti iwo angadzakumbukire kapena kuphunzira zimene a Mboni za Yehova akhala akulalikira kwa zaka zambiri zoti zipembedzo zabodza zidzawonongedwa.
Izi zikufanana ndi zimene zinachitika ku Iguputo pambuyo pa miliri 10. Yehova ‘atapereka chiweruzo pa milungu yonse ya mu Iguputo,’ “gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana” linapita limodzi ndi Aisiraeli. (Eks. 12:12, 37, 38) Anthu amitundu inawo ayenera kuti anasankha kupita ndi anthu a Yehova ataona kuti zimene Mose ananena zokhudza miliri 10 zakwaniritsidwa.
Aliyense amene adzayambe kulambira Yehova pambuyo poti Babulo Wamkulu wawonongedwa, adzakhala ndi mwayi wochitira zabwino abale ake a Khristu omwe adzakhale adakali padzikoli. (Mat. 25:34-36, 40) Komabe mwayi woti aweruzidwe monga nkhosa udzatha Aramagedo itangotsala pang’ono kuyamba, odzozedwa omwe adzakhale adakali padzikoli akadzalandira mphoto yawo kumwamba.
Kusintha komwe tafotokoza munkhaniyi kukutsindika mfundo yakuti Yehova ndi wachikondi komanso wachifundo. Iye “sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”—2 Pet. 3:9.