NKHANI YOPHUNZIRA 40
NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala
Yehova Amatithandiza Kuti ‘Tizisangalala Kwambiri’
“Ndidzapita . . . kwa Mulungu amene amandisangalatsa kwambiri.”—SAL. 43:4.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona zimene zingachititse kuti tisamasangalale ndi zimene tingachite kuti tiyambirenso kusangalala.
1-2. (a) Kodi anthu ambiri amakumana ndi zotani masiku ano? (b) Kodi tikambirana chiyani?
MASIKU ano anthu amachita zambiri kuti azisangalala. Ngakhale zili choncho, amakhalabe osasangalala. Ambiri amavutika ndi maganizo odziona kuti ndi achabechabe komanso amakhala achisoni. Atumiki a Yehova amavutikanso ndi maganizo ngati amenewa. Popeza tikukhala ‘m’masiku otsiriza,’ nthawi zina tingakumane ndi mavuto amene angachititse kuti tikhale ndi nkhawa komanso chisoni.—2 Tim. 3:1.
2 Munkhaniyi, tikambirana zinthu zimene zingachititse kuti tisamasangalale komanso zimene tingachite kuti tiyambirenso kusangalala. Koma choyamba tiyeni tione amene angatithandize kuti tizisangalala zenizeni.
KODI NDI NDANI ANGATITHANDIZE KUTI TIZISANGALALA ZENIZENI?
3. Kodi zimene Yehova analenga zimatiphunzitsa chiyani zokhudza iye? (Onaninso zithunzi.)
3 Nthawi zonse Yehova amasangalala ndipo amafuna kuti ifenso tizisangalala. N’chifukwa chake anapanga zinthu zambiri zimene timasangalala nazo. Mwachitsanzo, timasangalala tikaona dziko lokongolali limene lili ndi zinthu za mitundu yosiyanasiyana, tikaona nyama zikusewera komanso tikamadya zakudya zimene timazikonda. N’zoonekeratu kuti Mulungu amatikonda kwambiri ndipo amafuna tizisangalala.
Baby elephant: Image © Romi Gamit/Shutterstock; penguin chicks: Vladimir Seliverstov/500px via Getty Images; baby goats: Rita Kochmarjova/stock.adobe.com; two dolphins: georgeclerk/E+ via Getty Images
Tikaona nyama zikusewera timakumbukira kuti Yehova ndi Mulungu wachimwemwe (Onani ndime 3)
4. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amasangalalabe ngakhale kuti amaona anthu akuvutika? (b) Kodi Yehova anatipatsa mphatso iti? (Salimo 16:11)
4 Ngakhale kuti Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe,” amadziwa mavuto amene akuchitika padzikoli. (1 Tim. 1:11) Koma zimenezi sizimamuchititsa kuti asamasangalale. Iye akudziwa kuti mavutowa ndi akanthawi moti anasankha kale tsiku limene adzawathetse. Ndipo akupirira moleza mtima poyembekezera tsiku limene adzachotse chisoni ndi kuvutika mpaka kalekale. Panopa Yehova amamvetsa mavuto amene tikukumana nawo ndipo amatithandiza kuti tizisangalala. (Werengani Salimo 16:11.) Tiyeni tione mmene anathandizira Yesu kuti azisangalala.
5-6. N’chiyani chimathandiza Yesu kuti azisangalala?
5 Pa zonse zimene Yehova analenga, Yesu ndi amene amasangalala kwambiri. Tikutero pa zifukwa ziwiri izi. (1) “Iye ndi chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo,” n’chifukwa chake amasangalala kwambiri ngati Yehova. (Akol. 1:15; 1 Tim. 6:15) (2) Yesu anakhala zaka zambiri ndi Yehova yemwe ndi Mulungu wachimwemwe.
6 Yesu amasangalala chifukwa nthawi zonse amachita zimene Atate wake amafuna. (Miy. 8:30, 31; Yoh. 8:29) Popeza ndi wokhulupirika, Yehova amasangalala naye kwambiri.—Mat. 3:17.
7. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala?
7 Nafenso tingamasangalale ngati titakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova yemwe ndi Mulungu wachimwemwe. Tikamakhala ndi nthawi yokwanira yophunzira za Yehova n’kumamutsanzira, m’pamene timasangalala kwambiri. Timasangalalanso tikamachita zimene Yehova akufuna komanso tikadziwa kuti amatikonda.a (Sal. 33:12) Koma bwanji ngati nthawi zina timakhala osasangalala kwa nthawi yochepa kapena yaitali? Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu satikonda? Ayi. Popeza si ife angwiro, nthawi zina timamva ululu, chisoni komanso timakhala ndi nkhawa. Yehova amamvetsa bwino zimenezi. (Sal. 103:14) Tiyeni tikambirane zimene zingachititse kuti tisamasangalale komanso zimene tingachite kuti tiyambirenso kusangalala.
MUSALOLE KUTI CHILICHONSE CHIKULEPHERETSENI KUKHALA OSANGALALA
8. Kodi mavuto amene timakumana nawo angapangitse bwanji kuti tisamasangalale?
8 1: Mavuto amene timakumana nawo. Kodi panopa mukuzunzidwa, mukuvutika ndi ngozi yam’chilengedwe, umphawi, matenda kapena uchikulire? Mavuto ngati amenewa angachititse kuti tisamasangalale, makamakanso ngati palibe chimene tingachite kuti tiwathetse. Ndipotu Baibulo limati “munthu sasangalala ngati mtima ukumupweteka.” (Miy. 15:13) M’bale Babis, yemwe ndi mkulu, amene bambo ake, mayi ake komanso mchimwene wake anamwalira mu zaka 4 zokha, ananena kuti: “Ndinkamva kuti ndili ndekhandekha ndipo palibe angandithandize. Nthawi zina ndinkamva chisoni chifukwa panali zambiri zimene ndinkalimbana nazo moti sindinkakhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi mchimwene komanso makolo anga asanamwalire.” Ifenso nthawi zina mavuto angatichititse kuti tizikhala otopa komanso a nkhawa.
9. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiyambirenso kusangalala? (Yeremiya 29:4-7, 10)
9 Zimene tingachite kuti tiyambirenso kusangalala. Tingayambirenso kusangalala tikamaona zinthu moyenera komanso tikakhala ndi mtima woyamikira. Anthu ambiri m’dzikoli amaganiza kuti angamasangalale pokhapokha ngati zinthu zikuwayendera bwino. Koma si zoona. Mwachitsanzo, Yehova analangiza Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo kuti azichita zonse zimene angathe n’cholinga choti azisangalala ngakhale anali akapolo. (Werengani Yeremiya 29:4-7, 10.) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Muzivomereza mmene zinthu zilili pa moyo wanu n’kumasangalala ndi zinthu zabwino zimene zikukuchitikirani. Muzikumbukira kuti Yehova sadzakusiyani, iye adzakuthandizani. (Sal. 63:7; 146:5) Mwachitsanzo, Mlongo Effie yemwe anachita ngozi n’kulumala, anati: “Yehova, anthu am’banja langa komanso abale ndi alongo anandilimbikitsa ndiponso kundithandiza kwambiri. Ndiye pofuna kuwasonyeza kuti ndimayamikira zimene amandichitira, ndimayesetsa kukhala wosangalala.”
10. N’chiyani chingatithandize kuti tizisangalalabe ngakhale tikukumana ndi mavuto?
10 N’zotheka kumasangalalabe ngakhale zitakhala kuti zinthu sizikuyenda mmene tinkafunira komanso anthu am’banja lathu kapena ifeyo tikukumana ndi mavuto aakulu.b (Sal. 126:5) Tikutero chifukwa kuti munthu azisangalala, sizidalira mmene zinthu zilili pa moyo wake. Maria, yemwe ndi mpainiya, anati: “Ukakumana ndi mavuto n’kumasangalalabe sizitanthauza kuti ukubisa mmene ukumvera. Koma zimasonyeza kuti sunaiwale zimene Yehova analonjeza. Atate wathu adzatithandiza kuti tizisangalalabe.” Tizikumbukira kuti ngakhale mavuto athu atakhala aakulu, sadzakhalapo mpaka kalekale, ngati mmene zimakhalira zidindo za mapazi tikaponda pamchenga. Posachedwapa Yehova athetsa mavuto athu onse.
11. Kodi chitsanzo cha mtumwi Paulo chimakulimbikitsani bwanji?
11 Nthawi zina tingamaganize kuti tikukumana ndi mavuto chifukwa Yehova wasiya kutikonda. Tikayamba kuganiza zimenezi, tizikumbukira za atumiki okhulupirika a Yehova amene anakumana ndi mavuto aakulu. Taganizirani za mtumwi Paulo. Iye anasankhidwa ndi Yesu kuti akalalikire uthenga wabwino “kwa anthu a mitundu ina komanso kwa mafumu ndi Aisiraeli.” (Mac. 9:15) Uwutu unali mwayi wapadera. Ngakhale zinali choncho, Paulo anakumana ndi mavuto ambiri. (2 Akor. 11:23-27) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova anali atasiya kumukonda? Ayi. M’malomwake, Paulo anakwanitsa kupirira mavuto ake chifukwa Yehova ankamuthandiza. (Aroma 5:3-5) Ndiye taganizirani mavuto amene mukukumana nawo. Mukuyesetsa kupirira n’kumatumikira Yehova mokhulupirika ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto onsewo. Mofanana ndi Paulo, inunso mukuona kuti Yehova akukuthandizani ndipo amakukondani.
12. Kodi zimene timayembekezera zikalephereka zimachititsa bwanji kuti tisamasangalale?
12 2: Zimene timayembekezera zikalephereka. (Miy. 13:12) Timakonda Yehova ndipo timayamikira zimene amatichitira. Choncho timayesetsa kukhala ndi zolinga zoti tizichita zambiri pomutumikira. Komabe ngati tili ndi zolinga zimene sitingathe kuzikwaniritsa chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu, zingachititse kuti tisamasangalale. (Miy. 17:22) Mpainiya wina dzina lake Holly ananena kuti: “Ndinkafuna kulowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, kukatumikira kudziko lina kapena kukathandiza ntchito yomanga ku Ramapo. Koma zinthu zinasintha pa moyo wanga moti sindikanathanso kukwaniritsa zolingazi. Ndinakhumudwa kwambiri. Zimakhala zopweteka munthu ukamafunitsitsa kuchita zinazake potumikira Yehova koma sungakwanitse.” Mmenemu ndi mmenenso amamvera atumiki a Yehova ambiri.
13. Kodi tingakhale ndi zolinga zotani ngati sitingakwanitse kuchita zambiri potumikira Yehova?
13 Zimene tingachite kuti tiyambirenso kusangalala. Tizikumbukira kuti Yehova safuna kuti tizichita zimene sitingakwanitse. Iye sationa kuti ndife ofunika potengera zimene timakwanitsa kuchita pomutumikira. Koma amafuna kuti tikhale odzichepetsa komanso okhulupirika. (Mika 6:8; 1 Akor. 4:2) Amasangalala akaona makhalidwe athu abwino ngakhale tikulephera kuchita zambiri pomutumikira. Ndiye kodi ndi nzeru kuyembekezera kuti tizichita zambiri kuposa zimene Yehova amafuna?c Ayi. Choncho ngati simungakwanitse kuchita zambiri chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wanu, muziyesetsa kungochita zimene mungakwanitse. Mwina mungaphunzitse achinyamata kapena kulimbikitsa achikulire. Mwinanso mungalimbikitse winawake pomuyendera, kumuimbira foni kapena kumutumizira uthenga. Yehova adzakudalitsani komanso kukuthandizani kuti muzisangalala mukakhala ndi zolinga zimene mungakwanitse. Muzikumbukira kuti posachedwapa, tikhala ndi mwayi wotumikira Yehova m’dziko latsopano m’njira zabwino kwambiri zimene sitinaziganizirepo. Zimenezi ndi zimene zinathandiza Holly amene tamutchula m’ndime yapita ija. Iye anati: “Ndikayamba kuganiza zofooketsa, ndimakumbukira kuti, ‘Ndili ndi mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale.’ Ndipo ndi thandizo la Yehova, ndidzakwanitsa kuchita chilichonse pomutumikira m’dziko latsopano.”
14. Kodi chinanso n’chiyani chimene chimachititsa kuti tisamasangalale?
14 3: Kukonda zosangalatsa. Anthu ena amagwiritsira ntchito malo ochezera a pa intaneti polimbikitsa maganizo akuti munthu amakhala wosangalala komanso wokhutira akamangokhalira kuchita zimene amasangalala nazo. Choncho tingamaganize kuti tingamasangalaledi tikamachita zosangalatsa, kugula zimene tikufuna komanso kuyenda m’malo osiyanasiyana. N’zoona kuti si kulakwa kuchita zosangalatsa. Yehova anatilenga m’njira yoti tizisangalala ndi zinthu zokongola. Komabe anthu ambiri anazindikira kuti zinthu zimene amaona ngati zingawathandize kuti asangalale, n’zimenenso zinawapangitsa kuti asamasangalale. Eva, amene ndi mpainiya ananena kuti, “Ukamangokhalira kuchita zinthu zimene zimakusangalatsa sukhutira.” Tikamangokhalira kuchita zosangalatsa, sitisangalala komanso timakhumudwa.
15. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Mfumu Solomo?
15 Mfumu Solomo inachita zinthu zosiyanasiyana kuti izisangalala. Mwachitsanzo, iye ankadya zakudya zabwino, ankamvetsera nyimbo zosangalatsa komanso ankagula zinthu zapamwamba. Koma zimenezi sizinamuthandize kuti azisangalala. Iye anati: “Diso silikhuta ndi kuona, ndipo khutu silidzaza chifukwa cha kumva.” (Mlal. 1:8; 2:1-11) Maganizo a anthu a m’dzikoli pa nkhani ya zimene zingapangitse munthu kuti azisangalaladi ali ngati ndalama yachinyengo. Amaoneka anzeru, koma amakhala osathandiza.
16. Kodi kupatsa kungatithandize bwanji kuti tiyambirenso kusangalala? (Onaninso zithunzi.)
16 Zimene tingachite kuti tiyambirenso kusangalala. Yesu anati “kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Alekos yemwe ndi mkulu ananena kuti: “Ndimayesetsa kuchita zinthu zing’onozing’ono pothandiza ena. Ndikamathandiza ena, ndimasiya kumangoganizira zofuna zanga ndipo ndimasangalala.” Kodi ndi zinthu ziti zimene inuyo mungachitire ena? Mukazindikira kuti munthu wina ali ndi nkhawa, mungamulimbikitse. Mwina simungathe kuthetsa mavuto ake, koma mungamulimbikitse mutamumvetsera mwachifundo, kumusonyeza kuti mukumvetsa mmene akumvera ndiponso kumulimbikitsa kuti aziuza Yehova nkhawa zake. (Sal. 55:22; 68:19) Mungamutsimikizire kuti Yehova sanamusiye. (Sal. 37:28; Yes. 59:1) Mungachitenso zinthu zina zosonyeza kuti mumamuganizira monga kumuphikira chakudya, kupita naye koyenda komanso kulowa naye mu utumiki. Muzilola kuti Yehova azikugwiritsani ntchito polimbikitsa anthu ena. Tikamagwiritsa ntchito nthawi yathu pothandiza anthu ena, zimathandiza kuti tizisangalala zenizeni.—Miy. 11:25.
M’malo mongoganizira zofuna zanu, muziyesetsa kuthandiza ena (Onani ndime 16)d
17. Kodi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kungatithandize bwanji kuti tizisangalala? (Salimo 43:4)
17 Tikhoza kumasangalala zenizeni ngati titapitiriza kudziwa Yehova n’kumayesetsa kumusangalatsa. Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova ndi amene amatithandiza kuti ‘tizisangalala kwambiri.’ (Werengani Salimo 43:4) Ndiye kaya tikumane ndi mavuto otani, sitikufunika kuda nkhawa. Choncho tiyeni tipitirize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, amene angatithandize kuti tizisangalala mpaka kalekale.—Sal. 144:15.
NYIMBO NA. 155 Chimwemwe Chosatha
a Onani bokosi lakuti “Muzidalira Yehova Kuti Akuthandizeni Kukhala Osangalala.”
b Mwachitsanzo, mungaone nkhani ya pa jw.org ya M’bale Dennis komanso Irina Christensen mu Lipoti la Nambala 5 la Bungwe Lolamulira la 2023.
c Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Musadzipanikize, Ndipo Mudzakhala Achimwemwe” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wagula zinthu zake zambirimbiri, koma akusangalala kwambiri pamene wagulira maluwa mlongo wachikulire amene akufunika kulimbikitsidwa.