Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb13 tsamba 174-177
  • Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo mu 1913

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo mu 1913
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2013
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo—1914
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2014
  • Malo a Msonkhano Wachigawo wa 2007 Wakuti “Tsatirani Khristu!”
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Chikhulupiriro Chachikristu Chidzayesedwa
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Malo a Msonkhano Wachigawo wa 2009 Wakuti “Khalani Maso”
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2013
yb13 tsamba 174-177
[Chithunzi pamasamba 174, 175]

Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo mu 1913

NSANJA YA OLONDA ya January 1, 1913, inanena zimene anthu ambiri amaganiza pamene inagwira mawu mtolankhani wina wa ku America dzina lake Herbert Kaufman. Mawu ake anali akuti: “Mawu akuti ‘n’zosatheka’ ndi achikale . . . Panopa anthu akwanitsa kuchita pafupifupi chilichonse chimene ankalakalaka.” Kumayambiriro kwa chaka cha 1913, anthu ankakhulupirira kuti m’tsogolo mwawo muchitika zinthu zabwino.

[Chithunzi pamasamba 174]

Kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga n’chimodzi mwa zinthu zimene zinkawapatsa chikhulupiriro chimenechi. Mwachitsanzo, ku United States, kampani yopanga magalimoto ya Ford Motor Company inatsegula fakitale yatsopano ku Highland Park, m’chigawo cha Michigan. Zimenezi zinachititsa kuti mitengo ya magalimoto itsike mofulumira kwambiri moti zinali zotheka kuti anthu ambiri agule galimoto. Kodi zinatheka bwanji kuti mitengo itsike choncho? Fakitale yatsopanoyo inali ndi makina apamwamba. Zimenezi zinathandiza kampani ya Ford kupanga galimoto yotchuka ya Model T pa nthawi yochepa kwambiri kuposa kale, zomwe zinachititsa kuti mtengo wa galimoto utsike.

Anthu a Yehova nawonso ankayembekezera zinthu zabwino, koma zosiyana ndi za anthu ena onse. Kwa zaka zambiri chaka cha 1914 chisanafike, Ophunzira Baibulo ankalengeza kuti chaka cha 1914 chidzakhala chaka chapadera kwambiri, moti ankayembekezera chaka chimenechi mwachidwi. Khama limene Ophunzira Baibulowa anali nalo pamene chakachi chinkayandikira, linasonyezeratu kuti akuyembekezera chinthu chinachake chapadera.

[Chithunzi patsamba 177]

Positikhadi yosonyeza ulendo wa Pastor Russell wopita m’mayiko osiyanasiyana

Choncho, mu June 1913 misonkhano ikuluikulu inayamba kuchitika, moti woyamba unali wa tsiku limodzi umene unachitikira ku Kansas City, m’chigawo cha Missouri, m’dziko la United States. Kwa milungu inayi yotsatira, sitima yahayala inkanyamula gulu la abale ndi alongo osangalala oposa 200 kupita ku msonkhano umene unkachitikira kumadzulo kwa United States ndiponso ku Canada. Pamsonkhano uliwonse, alendo ankapatsidwa mwayi wopempha kuti aphunzitsidwe zambiri. Anthu ambirimbiri anapempha kuti aziphunzira Baibulo ndipo patapita nthawi Ophunzira Baibulo anapita kukakumana ndi anthu achidwiwo.

Mu 1913 abale ogwira ntchito kulikulu ku Brooklyn anali kalikiliki kupanga “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.” M’sewero limeneli munali nkhani, zithunzi zokongola komanso nyimbo, ndipo linali la maola 8. Ophunzira Baibulo ankayembekezera kuti anthu ambiri achidwi amva uthenga wabwino kudzera m’seweroli. Ngakhale kuti pa nthawiyo kunali ofalitsa 5,100 okha omwe ankalalikira mwakhama, cholinga chawo chinali choti “afalitse seweroli kwina kulikonse padziko lapansi mmene angathere.”

Ophunzira Baibulo ankayembekezera mwachidwi mayankho a mafunso otsatirawa, ndipo ankakhulupirira kuti Yehova awathandiza. Mafunso ake ndi akuti, Kodi n’chiyani chichitike mu 1914? Kodi seweroli liwakhudza bwanji anthu? Kodi chichitike n’chiyani Nthawi za Akunja zikatha?

Nkhondo Yaikulu, imene kenako inadziwika kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse, inachititsa kuti anthu asinthe maganizo amene anali nawo a zinthu zabwino zimene ankayembekezera. Kupita patsogolo kwa zinthu zopangapanga sikukanathetsa mavuto amene anthu ankakumana nawo. Chaka chotsatira zinthu zinasintha kwambiri pakati pa Ophunzira Baibulo ndiponso pa dziko lonse lapansi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena