Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb14 tsamba 26-35
  • Lipoti la Milandu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lipoti la Milandu
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2014
  • Nkhani Yofanana
  • Lipoti la Milandu
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2013
  • Lipoti la Milandu
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Lipoti la Milandu
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2014
yb14 tsamba 26-35

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Lipoti la Milandu

Mtumwi Paulo anauza Akhristu kuti: “Kumbukirani amene ali m’ndende ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi.” (Aheb. 13:3) Monga atumiki a Yehova, timakumbukira abale ndi alongo athu okhulupirika ndipo timapempherera “anthu onse apamwamba, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso tikhale oganiza bwino.”—1 Tim. 2:1, 2; Aef. 6:18.

M’munsimu muli milandu ina imene Mboni za Yehova zinali nayo chaka chathachi:

Abale athu ku Russia akupitiriza “mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino” ngakhale kuti tchalitchi cha Orthodox komanso akuluakulu aboma akuyesetsa kuletsa ntchito yathu kumeneko. (Mac. 5:42) Akuluakulu aboma ku Russia akupitiriza kugwiritsa ntchito molakwika lamulo lawo losamveka bwino lokhudza kuchita zinthu monyanyira, limene poyamba analikhazikitsa pofuna kuthana ndi uchigawenga. Iwo akugwiritsa ntchito lamuloli poletsa zofalitsa zathu komanso pozunza abale ena. Zimenezi zachititsa kuti makhoti agamule kuti zofalitsa zathu zokwana 70 zili ndi mfundo zolimbikitsa anthu kuchita zinthu monyanyira. Ndipo akuluakulu aboma aika zofalitsa zimenezi pa mndandanda wa mabuku oletsedwa m’dzikolo. Zimenezi zachititsa kuti akuluakulu ena aboma azilowa m’Nyumba za Ufumu ndiponso m’nyumba za abale athu kuti akafufuze mabukuwa amenewo. Apolisi amagwira komanso kujambula ndi kutenga zidindo za zala za anthu ambiri a Mboni chifukwa cholalikira ndipo kawirikawiri amawaopseza.

Kuyambira mu May 2013, abale ndi alongo a mumzinda wa Taganrog anaimbidwa mlandu chifukwa chochita misonkhano ndiponso kulalikira. Aka n’koyamba kuchokera pamene boma la Soviet Union linagwa kuti a Mboni aimbidwe milandu chifukwa chochita zinthu zokhudza chikhulupiriro chawo. Akukuakulu aboma m’madera ena ku Russia komweko akukakamiza akhoti kuti agamule zoti mabuku athu amasokoneza anthu komanso kuti abale athu amalimbikitsa anthu kuti azidana chifukwa chosiyana zipembedzo.

Abale ndi alongo athu akuzunzidwabe ku Eritrea. Pofika mu July 2013, m’ndende za m’dzikoli munali abale ndi alongo athu okwana 52. Chiwerengero chimenechi chikuphatikizapo abale 8 a zaka 70 ndi alongo 6. Abale atatu omwe ndi Paulos Eyassu, Isaac Mogos ndi Negede Teklemariam, akhala m’ndende kuyambira pa September 24, 1994, chifukwa chokana kulowa usilikali.

Pa abale ndi alongo onse amene ali m’ndende m’dzikoli, ambiri ali kundende ya Meiter yomwe ili m’chipululu kumpoto kwa mzinda wa Asmara, womwe ndi likulu ladzikoli. Kuchokera mu October 2011 mpaka mu August 2012, akuluakulu aboma analanga abale athu okwana 25 powatsekera m’nyumba ya malata okhaokha. Hafu ya nyumba imeneyi inali m’nthaka ndipo hafu inayo inali pamtunda. M’miyezi yotentha, apolisi olondera akaidi amatulutsa akaidi m’ndendezi kuti asafe ndi kutentha. Komanso, akaidiwa sawapatsa chakudya chabwino ndi madzi okwanira moti abale athu amawonda ndiponso kufooka. Zomvetsa chisoni n’zakuti M’bale Yohannes Haile, wa zaka 68, anamwalira mu August 2012 chifukwa cha kuzunzidwaku, ndipo M’bale Misghina Gebretinsae anamwalira mu 2011.

Anakana Usilikali Chifukwa cha Chikumbumtima Chawo

Mogwirizana ndi Yesaya 2:4 komanso Yohane 18:36.

ARMENIA

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya (ECHR) linapereka chigamulo chotikomera pa November 27, 2012, pa mlandu wapakati pa a Khachatryan ndi anthu ena ndi boma la Armenia. Boma linkaimba mlandu wosavomerezeka a Mboni okwana 17 amene anakana zoti asilikali aziwayang’anira pogwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali. Boma la Armenia linapereka chipukuta misozi komanso linabweza ndalama zimene abalewo anawononga pa mlanduwu.

Ngakhale kuti khoti linapereka chigamulo chotikomera pa mlandu wa a Khachatryan ndiponso pa mlandu wina wotchuka wapakati pa a Bayatyan ndi boma la Armenia, komanso milandu ina imene khoti la ECHR linagamula, boma la Armenia linapitiriza kuimba mlandu achinyamata a Mboni chifukwa chokana usilikali. Koma pa June 8, 2013, bomali linavomereza kusintha lamulo lokhudza ntchito zimene anthu okana kulowa usilikali angamagwire. Zimenezi zithetsa vuto loti asilikali aziyang’anira anthu amene akugwira ntchito zoterezi. Abale onse amene anali m’ndende chifukwa chokana usilikali anamasulidwa pofika pa November 12, 2013. Komanso panopa abale onse amene amapempha kuti azigwira ntchito zina m’malo molowa usilikali amaloledwa.

SOUTH KOREA

Pofika pa October 31, 2013, m’ndende za m’dzikoli munali abale okwana 602. Kuchokera mu 1950, boma la South Korea latsekera m’ndende anthu 17,605 a Mboni za Yehova chifukwa chokana kulowa usilikali. Zaka zonse zimene anthuwa akhala m’ndende zakwana 34,184.

M’mbuyo monsemu, a Mboni ambiri amene anali m’ndende ankawaika m’chipinda chimodzi ndi zigawenga komanso anthu ena amene anapalamula milandu ikuluikulu. Koma posachedwapa gulu la abale linapita kwa mkulu woyang’anira ndende m’dziko la Korea kukam’pempha kuti abale athu asamawasakanike ndi akaidi ena. Mofulumira akuluakulu andende analekanitsa abale athuwo ndi zigawenga. Pofika mu April 2013, 75 peresenti ya abale amene anali m’ndende anawapatsa zipinda zawozawo moti abale 4 kapena 5 ankakhala chipinda chimodzi. Kodi zimenezi zathandiza bwanji abalewo?

M’bale wina anati: “Sitikukhalanso ndi anthu okonda zachiwerewere komanso kutukwana.” M’bale wina anati: “Panopa tikutha kumalimbikitsana ndipo tikumachita misonkhano yonse 5 mlungu uliwonse.”

Panopa m’dzikoli muli anthu 56 amene anasiya usilikali n’kukhala m’gulu la asilikali amene angathe kuwaitana ngati atafunika. Patapita nthawi anthu amenewa anakhala Mboni ndipo masiku ano akumawamanga pafupipafupi, kuwalipiritsa chindapusa komanso kuwatsekera chifukwa chokana kukachita maphunziro a usilikali. Abalewa amawaitana maulendo angapo pa chaka mwina kwa zaka 8 ndipo n’zovuta kupirira kwa nthawi yonseyi.

SINGAPORE

Abale 12 a m’dzikoli amene anakana kulowa usilikali anapempha kuti awapatse ntchito zina. Koma ngakhale kuti anapempha zimenezi mobwerezabwereza, onsewa akugwira ukaidi wa miyezi 39 m’ndende za asilikali. M’bale wina akugwira ukaidi wa chaka chimodzi chifukwa chokana zoti adzamuitane pakadzafunika asilikali.

TURKMENISTAN

Abale 9 amene anakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo akugwira ukaidi wa miyezi 18 mpaka zaka ziwiri. Kawirikawiri abalewa amamenyedwa mopanda chifundo ndi alonda a kundendeko komanso asilikali. Abalewa akamasulidwa amawamanganso n’kuwapatsa chilango chokhwima cha “akabwerebwere.” Anthu amene akumenyera ufulu wa a Mboni 10 amene anakana kulowa usilikali anakapereka madandaulo awo ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu.

Kukana Kuchita Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko Lako

Mogwirizana ndi Danieli 3:16-18.

Tanzania: Awa ndi ena mwa achinyamata a Mboni omwe anabwerera kusukulu, khoti litapereka chigamulo chowakomera

TANZANIA

Oweruza onse m’Khoti la Apilo ku Dar es Salaam, lomwe ndi khoti lalikulu kwambiri m’dziko la Tanzania, anagwirizana pa chigamulo chakuti zimene akuluakulu a sukulu ina anachita pochotsa sukulu ophunzira 5 ndi kuimitsa ena 122 chifukwa chokana kuimba nyimbo ya fuko n’zosavomerezeka. Chigamulo chimene khotili linapereka pa July 12, 2013, chinanena kuti ana a sukulu a Mboniwo ali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo malamulo akuwapatsa ufulu wochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chawo komanso ali ndi ufulu wopembedza, ndipo ufuluwu uyenera kutetezedwa. Zimene achinyamatawa anachita pokhalabe okhulupirika kwa Mulungu zathandiza kuti apambane mlanduwu ndi kuyeretsa dzina la Yehova. Zathandizanso kuti ufulu wathu wolambira m’dziko la Tanzania utetezeke.

Ufulu Wolankhula

Mogwirizana ndi Machitidwe 4:19, 20.

KAZAKHSTAN

Bungwe lina loona zachipembedzo litachita kafukufuku wawo linalengeza kuti mabuku athu amasokoneza anthu. Bungweli linanena kuti mabukuwa amalimbikitsa kuti anthu komanso zipembedzo zisamagwirizane. Choncho pa April 6, 2013, apolisi mumzinda wa Karabalyk analowa m’nyumba ya m’bale wina popanda chilolezo n’kulanda mabuku. Abale ankachitira misonkhano yawo ya mpingo m’nyumbayi, moti pa nthawi imene apolisiwo anafika, n’kuti misonkhano ili mkati. Pa July 3, 2013, khoti lazachuma mumzinda wa Astana linagwirizana ndi chigamulo choletsa mabuku athu okwana 10. Izi zikutanthauza kuti aboma apitiriza kufufuza mabuku athu kuti aone ngati muli zokayikitsa komanso azitsatira malamulo okhwima okhudza kuitanitsa mabuku kuchokera kumayiko ena. Kuwonjezera pamenepo, mu December 2012, akuluakulu aboma anayamba kumanga ndi kugwira abale athu ati chifukwa chakuti akuchita umishonale popanda chilolezo. Pa March 28, 2013, bungwe loona za zipembedzo linalamula bungwe la Mboni za Yehova m’dzikoli (Regional Religious Center of Jehovah’s Witnesses) kuti liuze anthu onse a Mboni za Yehova ku Kazakhstan kuti kulalikira m’malo ena, osati malo awo olambirira amene analembetsa kuboma, n’kuphwanya malamulo. Pofika mwezi wa July 2013, aboma anali atatsegulira milandu abale ndi alongo okwana 21.

Ufulu Wosonkhana Ndiponso Kucheza ndi Ena

Mogwirizana ndi Aheberi 10:24, 25.

AZERBAIJAN

M’mwezi wa January 2010 bungwe laboma loona za zipembedzo linakana kuti bungwe la Mboni za Yehova lilembetsenso m’dzikoli. Akuti linakana chifukwa chakuti panali zolakwika zina pa fomu yopempha kuti alembetsenso bungweli. Ngakhale kuti Mboni za Yehova zinayesetsa mobwerezabwereza kukonza zimene akuti zinalakwikazo, akuluakulu abomawo akupitiriza kukana kulemba bungweli m’kaundula. Pa July 31, 2012, abale athu anatengera nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Abalewa akudandaula kuti boma likuwakaniza kulembetsa bungwe lathu monga gulu lovomerezeka lachipembedzo pa zifukwa zosamveka ndipo izi zikuwaphwanyira ufulu wopembedza. Malinga ndi malamulo adzikoli, ngati gulu lathu sililembedwanso m’kaundula, sitingakhale ndi ufulu wonse wolambira umene magulu olembetsedwa amakhala nawo.

Ufulu Ndiponso Chitetezo cha Munthu ndi Katundu

Mogwirizana ndi Afilipi 1:7.

UKRAINE

Ngakhale kuti abale ndi alongo ali ndi ufulu wolambira m’dziko la Ukraine, akukumana ndi mavuto monga kumenyedwa, kuwonongeredwa katundu ndi Nyumba za Ufumu. Izi zikachitika, aboma safufuza mokwanira n’kupereka chilango choyenera kwa anthu amene akuchita zimenezi. Zimenezi zachititsa kuti anthu otsutsa aziganiza kuti angathe kuchita chilichonse popanda kupatsidwa chilango. Zotsatira zake n’zoti m’chaka cha 2012 ndi 2013, anthu oipawa anawirikiza kwambiri kuchitira nkhanza abale athu. Mwachitsanzo, mu 2010 anthuwa anawononga katundu wa abale athu m’madera 5. Koma mu 2011 chiwerengerochi chinakwera kufika pa 15, mu 2012 chinafika pa 50 ndipo m’miyezi yoyambirira ya chaka cha 2013, zimenezi zinachitika m’malo 23. Ofesi ya nthambi ikukonza zokasuma milandu ya nkhanza zimenezi ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu.

Ukraine: Abale athu akukonzekera kumanganso Nyumba ya Ufumu iyi yomwe anthu anaiwononga n’kuitentha

Ufulu Wosankha Zimene Munthu Akufuna

Mogwirizana ndi Machitidwe 5: 29 ndi Machitidwe 15:28, 29.

ARGENTINA

Tsiku lina m’chaka cha 2012 m’bale Pablo Albarracini anapezeka pamalo amene anthu ena ankafuna kuba katundu. Akubawo anawombera M’bale Albarracini mobwerezabwereza ndipo anthu anathamangira naye kuchipatala ali chikomokere. Mwamwayi, m’baleyu anali ndi Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala lolembedwa bwino. M’khadili anakana kumuika magazi kapena kumuthandiza pogwiritsa ntchito zinthu zopangidwa kuchokera ku magazi. Ngakhale kuti achipatala anali okonzeka kutsatira zimene analemba pakhadilo, wachibale wake amene si Mboni anapita kukhoti kuti akatenge chikalata chokakamiza achipatalawo kuika magazi M’bale Albarracini. Iye ankanena kuti magaziwo ndi amene akanathandiza kupulumutsa moyo wake. Koma khoti lalikulu kwambiri ku Argentina linapereka chigamulo chokomera M’bale Albarracini ponena kuti iye ali ndi ufulu wonena thandizo la mankhwala limene akufuna ngakhale atakomoka. Choncho sanamuike magaziwo ndipo anachira bwinobwino. M’baleyu akuthokoza kwambiri Yehova pomuthandiza kuti akhalebe wokhulupirika pa nkhani yofunikayi.

Akuzunzidwa Chifukwa cha Chipembedzo

Mogwirizana ndi Luka 21:12-17.

KYRGYZSTAN

Pa April 16, 2013, khoti linapereka chigamulo chokomera m’bale wina ku Toktogul, kumene anthu a m’deralo anawononga Nyumba ya Ufumu kawiri konse. Akhoti anamanga anthu amene ankatsogolera chiwembuchi ndipo anawalamula kuti alipire chipukuta misozi. Panopa milandu ya anthu amene anatsogolera chiwembuchi ulendo woyambawo ili mkati, ndipo zimenezi zithandiza kuti mavuto amenewa athe m’deralo. Koma padakali pano, mpingo ukukonza zomanganso Nyumba ya Ufumuyo.

Kyrgyzstan: Nyumba ya Ufumu iyi inawonongedwa kawiri ndi anthu a m’derali

Milandu Ikuluikulu Imene Yatiyendera Bwino

  1. Nkhani yake: Kodi gulu la chipembedzo liyenera kupeza kaye chilolezo kuti lichite misonkhano ikuluikulu komanso ya mpingo?

    Chigamulo chake: Pa December 5, 2012, Khoti Loona za Malamulo a Dziko la Russia linanena kuti Malamulo a dziko la Russia amapereka ufulu wachipembedzo ndipo linagamula kuti abale athu ali ndi ufulu wochita misonkhano yachipembedzo popanda kupempha chilolezo kwa akuluakulu a boma kapena kuwadziwitsa za misonkhanoyi.

  2. Nkhani yake: Kodi nzika zili ndi ufulu wosunga chinsinsi pa nkhani zawo zachipatala? Zimene zinachitika: Mu 2007, wachiwiri kwa woimira boma pa milandu mumzinda wa St. Petersburg, m’dziko la Russia, analamula kuti zipatala zonse mumzindawu zizikanena ku ofesi yake ngati aliyense wa Mboni za Yehova wakana kuikidwa magazi, koma wodwalayo asamamuuze chilichonse. Makhoti a ku Russia atalephera kuteteza ufulu wosunga chinsinsi cha odwala, abale anakatula nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya (ECHR).

    Chigamulo chake: Pa June 6, 2013, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula kuti zimene woimira boma pa milanduyo ananena zinaphwanya ufulu wa munthu wosunga chinsinsi ndipo ananena kuti palibe “chifukwa chomveka kapena chokwanira” choululira zinsinsi za anthu kwa aliyense wa m’boma. Chigamulochi chinayamba kugwira ntchito pa October 7, Komiti Yaikulu ya khotili itakana pemphe la boma la Russia loti komitiyi iunikenso nkhaniyi.—Mlandu wapakati pa Avilkina ndi anthu ena ndi boma la Russia.

Mfundo Zina Zokhudza Milandu Imene Tinaitchula mu Buku Lapachaka la Chaka Chatha

Boma la France linamvera chigamulo cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya cha pa July 5, 2012, chokhudza msonkho wosavomerezeka uja. Bomali linabweza ndalama zonse zimene linatenga komanso chiwongola dzanja chake. Linabwezanso ndalama zimene tinawononga pa nthawi ya mlanduwu, ndipo anachotsa lamulo lakuti malo a nthambi ndi chikole cha ndalama zamsonkho zimene timayenera kupereka.—Buku Lapachaka la 2013, tsamba 34.

Mboni za Yehova ku India zikutsutsidwabe m’madera osiyanasiyana m’dzikoli. Koma sanamangidwe kapena kuimbidwa milandu yowanamizira ngati mmene zinalili m’mbuyomu. Pakali pano tili ndi milandu pafupifupi 20 imene cholinga chake n’kuthetsa zinthu zoipa zimene abale athu achitiridwa.—Buku Lapachaka la 2013, tsamba 35.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena