Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb15 tsamba 160-tsamba 161 ndime 1
  • Yehova Watsegula Mitima ya Anthu Ambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Watsegula Mitima ya Anthu Ambiri
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Nkhani Yofanana
  • Anali M’gulu la Zigawenga Kenako Anayamba Kutumikira Mulungu
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Wolemala Koma Wodzipereka
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Ndawona kuti Yehova Ali Wabwino
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Ndinaona “Wamng’ono” Akusanduka “Mtundu Wamphamvu”
    Nsanja ya Olonda—1997
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
yb15 tsamba 160-tsamba 161 ndime 1

DOMINICAN REPUBLIC

Yehova Watsegula Mitima ya Anthu Ambiri

Leonardo Amor

  • KUBADWA 1943

  • KUBATIZIDWA 1961

  • MBIRI YAKE Anaphunzira Baibulo ali kamnyamata ndipo wakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 50.

Chithunzi patsamba 160

Ndinabatizidwa mu 1961, patangopita mwezi umodzi kuchokera pamene Trujillo anaphedwa. Pa nthawiyo ndinkaphunzira uloya ku yunivesite. Bambo anga ankafuna kuti ndidzakhale loya koma ine ndinaona kuti maphunziro a Yehova ndi apamwamba kuposa uloyawo. Ndiyeno ndinasiya sukulu ku yunivesiteko koma bambo anga sanasangalale nazo. Pasanapite nthawi ndinayamba kuchita upainiya wapadera.

Pa nthawi ina ndinatumizidwa kumzinda wa La Vega. Mumzindawu chikatolika chinali chitazika mizu kwambiri. Nthawi yonse imene ndinakhala kumeneko palibe amene ankafuna kuphunzira. Ndinkakamba nkhani za onse koma amene ankapezekapo ndi munthu m’modzi amene ndinkachita naye upainiya. Koma Yehova anandithandiza chifukwa choti ndinkakonda kuphunzira Baibulo pandekha, kupezeka pamisonkhano ikuluikulu ndiponso kupemphera kuchokera pansi pa mtima. Ndinkapempha Yehova kuti athandize n’cholinga choti mumzindawu mukhale mpingo. Panopa ndimasangalala kwambiri chifukwa kuli Nyumba za Ufumu 6, mipingo 14 ndiponso ofalitsa oposa 800.

Mu 1965 ndinakwatira Ángela ndipo mu 1981 tinaitanidwa ku Beteli. Pamene ndinkabatizidwa, m’dzikoli munali ofalitsa 681 okha koma pano kuli ofalitsa oposa 36,000. Anthu masauzande ambiri amapezeka pa misonkhano ikuluikulu. Ndikaganizira mmene zinalili m’mbuyomu ndimasangalala kwambiri poona kuti Yehova watsegula mitima ya anthu ambiri kuti amve uthenga wa m’Baibulo.

Chithunzi patsamba 161

Komiti ya Nthambi. Kuchokera kumanzere: Reiner Thompson, Juan Crispín, Thomas Dean, Leonel Peguero, Leonardo Amor ndi Richard Stoddard

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena